Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb22 March tsamba 7
  • Muzithandiza Ophunzira Baibulo Kuti Asiye Makhalidwe Oipa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzithandiza Ophunzira Baibulo Kuti Asiye Makhalidwe Oipa
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Nkhani Yofanana
  • Muzithandiza Ophunzira Anu Kuti Akhale pa Ubwenzi ndi Yehova
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Muzilola Kuti Yehova Azikuthandizani Kudzera M’pemphero
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Zimene Mungachite Kuti Muzisangalala Kwambiri Mu Utumiki​—Muzifunsa Mafunso
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Muziwafika Pamtima
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
mwb22 March tsamba 7

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI | ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZISANGALALA KWAMBIRI MU UTUMIKI

Muzithandiza Ophunzira Baibulo Kuti Asiye Makhalidwe Oipa

Anthu okhawo amene ali ndi makhalidwe abwino, ndi amene angakhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (1Pe 1:14-16) Ophunzira Baibulo akasiya makhalidwe oipa, zinthu zingamawayendere bwino m’banja, sangakumane ndi mavuto azachuma komanso angakhale ndi thanzi labwino.

Muziwafotokozera momveka bwino mfundo za makhalidwe abwino za Yehova, chifukwa chake mfundozo zilipo komanso kufunika kozitsatira. Muzithandiza ophunzira anu kuti asinthe mmene amaganizira, ndipo akatero, adzayamba kuchita zimene Yehova amasangalala nazo. (Aef 4:22-24) Muziwatsimikizira kuti mothandizidwa ndi Yehova, akhoza kusiya makhalidwe oipa. (Afi 4:13) Muziwaphunzitsa kuti azichonderera Yehova akaona kuti ayamba kulakalaka kuchita zinthu zoipa. Muziwaphunzitsa kuti azipewa zochitika zimene zingawachititse kuti ayesedwe. Muziwalimbikitsa kuti azichita zinthu zimene zingawathandize m’malo mochita zinthu zoipa. Mudzasangalala kwambiri mukadzaona ophunzira Baibulo anu akukwanitsa kusintha makhalidwe awo oipa mothandizidwa ndi Yehova.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZITHANDIZA AMENE MUKUPHUNZIRA NAWO BAIBULO KUTI ASIYE MAKHALIDWE OIPA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Muzithandiza Amene Mukuphunzira Nawo Baibulo Kuti Asiye Makhalidwe Oipa.” Anita ndi Jane ali ndi akulu.

    Kodi akulu komanso Anita anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira Jane?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Muzithandiza Amene Mukuphunzira Nawo Baibulo Kuti Asiye Makhalidwe Oipa.” Anita akuphunzira Baibulo ndi Jane.

    Kodi Anita anapitiriza bwanji kuthandiza Jane?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Muzithandiza Amene Mukuphunzira Nawo Baibulo Kuti Asiye Makhalidwe Oipa.” Jane akupemphera kuti Yehova amuthandize.

    Kodi Jane anafufuza bwanji thandizo lochokera kwa Yehova?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena