Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb21 November tsamba 15
  • Muzithandiza Ophunzira Anu Kuti Azidzidyetsa Mwauzimu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzithandiza Ophunzira Anu Kuti Azidzidyetsa Mwauzimu
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Nkhani Yofanana
  • Muzithandiza Ophunzira Anu Kuti Akhale pa Ubwenzi ndi Yehova
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Muzithandiza Ophunzira Baibulo Kuti Asiye Makhalidwe Oipa
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Zimene Mungachite Kuti Muzisangalala Kwambiri Mu Utumiki​—Muzifunsa Mafunso
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Muziwafika Pamtima
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
mwb21 November tsamba 15

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI | ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZISANGALALA KWAMBIRI MU UTUMIKI

Muzithandiza Ophunzira Anu Kuti Azidzidyetsa Mwauzimu

Kuti ophunzira amudziwe bwino Yehova komanso akhale olimba mwauzimu, ayenera kuphunzira zambiri osati mfundo za choonadi zokha zomwe timawaphunzitsa. (Mt 5:3; Ahe 5:12–6:2) Ayeneranso kuphunzira mmene angamadzidyetsere okha mwauzimu.

Phunziro likangoyamba kumene, muzisonyeza ophunzira anu mmene angamakonzekerere phunziro la Baibulo ndipo muziwalimbikitsa kuchita zimenezi. (mwb18.03 6) Muziwalimbikitsa kuti azipemphera asanayambe kuphunzira paokha. Muziwathandiza kupeza komanso kugwiritsa ntchito zinthu zophunzirira za pazipangizo zamakono. Muziwasonyeza mmene angapezere zinthu zatsopano pa jw.org ndi JW Broadcasting®. Pakapita nthawi, muziwaphunzitsa kuti aziwerenga Baibulo tsiku lililonse, azikonzekera misonkhano yampingo, komanso azifufuza mayankho a mafunso awo. Muziwathandiza kuti aziganizira mozama zimene akuphunzirazo.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZITHANDIZA AMENE MUKUPHUNZIRA NAWO BAIBULO KUTI AZIDZIDYETSA MWAUZIMU, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Muzithandiza Amene Mukuphunzira Nawo Baibulo Kuti Azidzidyetsa Mwauzimu.” Jane akufotokoza kuti amakumbukira zinthu zimene zimam’fika pamtima.

    Kodi Anita anathandiza bwanji Jane kudziwa kuti kuphunzira kumaphatikizapo zambiri osati kungodziwa mayankho okha?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Muzithandiza Amene Mukuphunzira Nawo Baibulo Kuti Azidzidyetsa Mwauzimu.” Anita akuthandiza Jane kupeza yankho kuchokera m’malemba.

    Kodi n’chiyani chinathandiza Jane kutsimikiza kuti Yehova salakwitsa akamaletsa anthu zachiwerewere?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Muzithandiza Amene Mukuphunzira Nawo Baibulo Kuti Azidzidyetsa Mwauzimu.” Jane akuganizira mozama zimene wawerenga atakhala pafupi ndi chibwenzi chake.

    Muzithandiza ophunzira anu kudziwa mmene angadziphunzitsire okha komanso mmene angagwiritsire ntchito zimene aphunzirazo

    Pa nkhani yoganizira mozama zomwe waphunzira, kodi Jane anazindikira chiyani?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena