KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI | ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZISANGALALA KWAMBIRI MU UTUMIKI
Muzithandiza Ophunzira Baibulo Kuti Asamacheze ndi Anthu Olakwika
Kuti ophunzira Baibulo akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, ayenera kumacheza ndi anthu abwino. (Sl 15:1, 4) Anzawo abwino adzawathandiza kuti azichita zinthu zabwino.—Miy 13:20; lff phunziro 48.
Muzikhala achifundo mukamathandiza ophunzira Baibulo anu kuti asamacheze ndi anthu a makhalidwe oipa. Zikhoza kuwavuta kuti asiye kucheza ndi anzawo amene ankacheza nawo poyamba. Choncho muzisonyeza kuti mumawaganizira ngakhale pa masiku amene simukuphunzira nawo. Mukhoza kuwatumizira meseji, kuwaimbira foni kapena kuwayendera kumene. Ophunzira Baibulo anu akamapita patsogolo, mungawaitane kuti mudzacheze nawo limodzi ndi abale ndi alongo ena. Mukamachita zimenezi, adzaona mosavuta kuti akupeza zambiri kuposa zimene akusiya. (Mko 10:29, 30) Inunso mudzasangalala kwambiri mukadzaona kuti banja la Yehova likukula.
ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZITHANDIZA AMENE MUKUPHUNZIRA NAWO BAIBULO KUTI ASAMACHEZE NDI ANTHU OLAKWIKA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi kugwirizana ndi anthu oipa kumatanthauza chiyani?—1Ak 15:33
Kodi Jane anaganiza kuti macheza Achikhristu angakhale otani?
Kodi Anita anamuthandiza bwanji Jane kuti asamacheze ndi anthu a makhalidwe oipa?