“Zinthu Zonse Zitheka ndi Mulungu”
1 Ntchito yofunika kwambiri ya mpingo wachikristu ndiyo kulalikira uthenga wa Ufumu padziko lonse lapansi. (Mat. 24:14) Imeneyitu ndi ntchito yaikulu kwabasi. Anthu ambiri amaona kuti imafunika zinthu zambiri kuposa zimene tili nazo. Ena amaona kuti n’kosatheka kugwira ntchitoyi chifukwa anthu amatinyoza, kutitsutsa ndi kutizunza. (Mat. 24:9; 2 Tim. 3:12) Anthu osakhulupirira amaonadi kuti n’kosatheka kukwanitsa ntchitoyi. Koma, Yesu anati: “Zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.”—Mat. 19:26.
2 Zitsanzo Zabwino Kuzitsanzira: Yesu anayamba utumiki wake ali yekhayekha pamene otsutsa anali ambiri. Adani ake pofuna kumulepheretsa ntchito yake, anam’chitira mwano m’njira zosiyanasiyana, mapeto ake anamupha imfa yopweteka kwambiri. Komabe potsiriza Yesu ananena motsimikiza kuti: “Ndalilaka dziko lapansi.” (Yoh. 16:33) Ndithudi anakwanitsa zinthu zooneka zosatheka!
3 Ophunzira a Yesu anasonyeza kulimba mtima ndi changu chofananacho mu utumiki wachikristu. Ambiri anawakwapula, kuwamenya, kuwaika mundende ngakhale kuwapha kumene. Koma “[a]nakondwera kuti anayesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzinalo.” (Mac. 5:41) Ngakhale zinali zovuta, anakwaniritsa ntchito yooneka yosatheka, yolalikira uthenga wabwino “kufikira malekezero ake a dziko.”—Mac. 1:8; Akol. 1:23.
4 Mmene Tingakhozere Lerolino: Ifenso tikugwira ntchito yolalikira Ufumu mwachangu pamene zinthu zili zovuta kwambiri. Ngakhale pali ziletso, chizunzo, kumangidwa ndi ziwawa zina pofuna kutisiyitsa ntchitoyi, tikuitha. Kodi zikutheka bwanji? “Ndi khamu la nkhondo ayi, ndi mphamvu ayi, koma ndi Mzimu wanga, ati Yehova wa makamu.” (Zek. 4:6) Chifukwa Yehova akutilimbikitsa, palibe chingalepheretse ntchito yathu!—Aroma 8:31.
5 Polalikira, palibe chifukwa chochitira manyazi kapena mantha kapena kudziona kuti sitikuyenera. (2 Akor. 2:16, 17) Tili ndi zifukwa zazikulu zopitirizira kufalitsa uthenga wabwino wa Ufumu. Ndi thandizo la Yehova, tidzakwanitsa “zosatheka”!—Luka 18:27.