Gwirani Nawo Ntchito Yotuta Mokwanira
1 Aneneri a Yehova akale komanso Yesu Kristu weniweniyo ananena za ntchito yosonkhanitsa. (Yes. 56:8; Ezek. 34:11; Yoh. 10:16) Panopa ntchito imeneyi ikukwaniritsidwa pamene uthenga wabwino wa Ufumu ukulalikidwa padziko lonse lapansi. (Mat. 24:14) Kusiyana kwa anthu otumikira Mulungu ndi osam’tumikira kukuoneka bwino kwabasi. (Mal. 3:18) Kodi zimenezi zikutiuza chiyani?
2 Udindo wa Aliyense: Titengere chitsanzo cha Paulo, amene anatanganidwa kwambiri kutsogolera utumiki wachikristu. Anadziŵa kuti unali udindo wake wolalikira kuti anthu onse akhale ndi mwayi womva uthenga wabwino ndiponso wopulumuka. Zimenezi zinamusonkhezera kugwira ntchito mosalekeza n’cholinga chakuti awathandize. (Aroma 1:14-17) Popeza tikudziŵa ngozi imene ili patsogolo pa anthu lerolino, kodi sindiye kuti tili ndi udindo waukulu wolalikira anthu a m’gawo lathu?—1 Akor. 9:16.
3 Nthaŵi Yofunika Kuchita Changu: Ntchito yolalikira tingaiyerekeze ndi kupulumutsa anthu pangozi. Tiyenera kufufuza anthu ndi kuwathandiza kupita kumalo otetezeka nthaŵi isanathe. Nthaŵi ndi yochepa. Miyoyo ili pachiswe! N’chifukwa chake Yesu analimbikitsa ophunzira ake ‘kupempha Mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake.’—Mat. 9:38.
4 Pozindikira kufunika kwa ntchitoyi lerolino, antchito ya Ufumu ambiri awonjezera zomwe amachita mu ntchito imeneyi yopulumutsa miyoyo. Mnyamata wina wotchedwa Hirohisa ankakhala ndi mayi ake komanso azibale ake aang’ono anayi. Kuti athandize banja lake, ankadzuka 3 koloko m’bandakucha kukagulitsa nyuzipepala. Ngakhale zinali choncho, Hirohisa ankafuna kuchita zochuluka mu utumiki, chotero anayamba kuchita upainiya wanthaŵi zonse. Kodi pali zina zimene mungachite kuti mugwire nawo mokwanira ntchitoyi imene sidzabwerezedwanso?
5 Nthaŵi imene yatsala “yafupika.” (1 Akor. 7:29) Chotero, tonse tichite zimene tingathe mu ntchito yofunika kwambiri imene ikuchitika m’dziko lerolino, yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndiponso yopanga ophunzira. Yesu anayerekeza utumiki umenewu ndi ntchito yotuta. (Mat. 9:35-38) Tikagwira nawo ntchito yotutayi mokwanira, zipatso za ntchito yathu zidzakhala kuthandiza wina kubwera m’khamu lalikulu la olambira otchulidwa pa Chivumbulutso 7:9, 10.