Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/10 tsamba 1-2
  • M’minda Mwayera Kale Ndipo M’mofunika Kukolola

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • M’minda Mwayera Kale Ndipo M’mofunika Kukolola
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
  • Nkhani Yofanana
  • Limbikirani ntchito yotuta!
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Sangalalani Ndi Ntchito Yotuta!
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Zotsatira za Ntchito Yolalikira—“M’mindamo Mwayera Kale Ndipo M’mofunika Kukolola”
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
  • Muzigwira Nawo Mokwanira Ntchito Yokolola Mwauzimu
    Nsanja ya Olonda—2010
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
km 11/10 tsamba 1-2

M’minda Mwayera Kale Ndipo M’mofunika Kukolola

1. Kodi ndi ntchito yofunika iti imene ikuchitika?

1 Atamaliza kulalikira kwa mkazi wachisamariya, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Kwezani maso anu muone m’mindamo, mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola.” (Yoh. 4:35, 36) Kukolola kwauzimu kunali kutayamba ndipo Yesu anatha kuoneratu kuti ntchitoyo idzafalikira padziko lonse. Panopa Yesu ali kumwamba koma amakhudzidwabe kwambiri ndi ntchito yokololayi. (Mat. 28:19, 20) Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti ntchito imeneyi ikuwonjezerekabe pamene mapeto ake akuyandikira?

2. Kodi n’chiyani chimene chikusonyeza kuti ntchito yokolola ya padziko lonse lapansi ikuwonjezereka?

2 Ntchito yokolola yapadziko lonse: M’chaka chautumiki cha 2009, chiwerengero cha ofalitsa padziko lonse lapansi chinawonjezereka ndi 3.2 peresenti. M’madera amene ntchito yathu ndi yoletsedwa chiwerengerochi chinawonjezereka ndi 14 peresenti. Chiwerengero cha maphunziro a Baibulo apanyumba amene anachitiridwa lipoti mwezi ndi mwezi chinali choposa 7,619,000. Chiwerengero chimenechi chinali choposa chiwerengero chapamwamba cha ofalitsa ndiponso chinaposa chiwerengero cha maphunziro a Baibulo amene anachitiridwa lipoti chaka chatha ndi hafu miliyoni. Pamene ntchitoyi ikuwonjezereka m’madera ambiri, mayiko ambiri akupempha kuti tiwatumizire amishonale amene amaliza maphunziro awo a Gileadi. M’mayiko ambiri, anthu ochuluka olankhula zinenero zakunja akuphunzira choonadi. Apa n’zoonekeratu kuti Yehova akufulumiza ntchito yokololayi pamene ikuyandikira kumapeto ake. (Yes. 60:22) Kodi mumakonda “munda” wanu umene mumalalikira?

3. Kodi anthu ena angamaganize chiyani pa ntchito yokolola m’gawo lawo?

3 Kukolola M’gawo Lanu: Ena anganene kuti: “Koma ife gawo lathu ndi louma.” N’zoona kuti madera ena amaoneka ngati ouma kusiyana ndi madera ena kapena anthu ake angamaoneke ngati chidwi chawo chayamba kuchepa. Choncho Mboni zina zingamaganize kuti m’madera amenewa ntchito yokolola inatha ndipo kwangotsala ntchito yochepa yokunkha anthu owerengeka amene atsala. Koma kodi zimenezi ndi zoona?

4. Kodi ntchito yathu tiyenera kuiona motani, nanga n’chifukwa chiyani?

4 Ntchito yokolola imakhala yambiri kungoyambira pachiyambi mpaka kumapeto kwake. Taonani mmene mawu a Yesu akusonyezera kuti ntchito imeneyi ndi yofunika kuigwira mwachangu. Iye anati: “Zokolola n’zochuluka, koma antchito ndi ochepa. Choncho pemphani Mwini zokolola kuti atumize antchito kukakolola.” (Mat. 9:37, 38) Yehova ndiye Mwini zokolola ndipo ali ndi udindo wosankha nthawi ndiponso malo amene tingapeze anthu achidwi. (Yoh. 6:44; 1 Akor. 3:6-8) Nanga ifeyo tili ndi udindo wanji? Baibulo limayankha kuti: “Bzala mbewu zako m’mawa, ndipo dzanja lako lisapume mpaka madzulo.” (Mlal. 11:4-6) Ndithudi, pamene ntchito yokololayi ili pachimake si nthawi yopumitsa dzanja lathu.

5. Kodi n’chifukwa chiyani tifunika kupitirizabe kulalikira mwachangu m’magawo amene anthu ake amaoneka kuti ndi opanda chidwi?

5 Pitirizani Kukolola: Ngakhale zitakhala kuti tinalalikira gawo lathu lonse maulendo angapo ndipo anthu ake amaoneka ngati alibe chidwi, tili ndi chifukwa chomveka chogwirira ntchitoyi mwachangu. (2 Tim. 4:2) Kusintha kwambiri kwa zinthu m’dzikoli kumachititsa anthu kusintha mmene amaonera zinthu ndiponso kuyamba kuganizira mofatsa za tsogolo lawo. Achinyamata akamakula amayamba kuona kufunika kokhala ndi mtendere wa m’maganizo komanso kukhala otetezeka. Komanso anthu ena akhoza kuchita chidwi chifukwa chakuti tawafikira mobwerezabwereza. Zimenezi zikusonyeza kuti anthu amene sankamvetsera m’mbuyomu akhoza kumvetsera. Ngakhale amene amakana mwadala uthenga wathu afunika kuchenjezedwa.—Ezek. 2:4, 5; 3:19.

6. Ngati gawo lathu ndi lovuta, kodi n’chiyani chingatithandize kukhalabe achangu?

6 Ngati gawo lathu ndi lovuta, kodi n’chiyani chingatithandize kukhalabe achangu? Kuwonjezera pa kulalikira khomo ndi khomo, mwina tingayese kulalikira m’malo a bizinezi kapena pa telefoni. Kapena tikhoza kusintha zomwe timanena polalikira kuti ulaliki wathu ukhale wosiyana ndi poyamba. Mwina tingasinthe nthawi kapena ndandanda yathu yolowera mu utumiki kuti tizilalikira masana kapena nthawi ina imene tingapeze anthu pakhomo. Tikhozanso kuphunzira chinenero china kuti tithe kufikira anthu ambiri ndi uthenga wabwino. Tingathe kuwonjezeranso utumiki wathu mwa kuchita upainiya wokhazikika kapena kusamukira kudera limene lili ndi okolola ochepa. Ngati timaona ntchito yokololayi moyenera, tidzayesetsa kugwira nawo ntchito yofunikayi mmene tingathere.

7. Kodi tiyenera kugwira ntchito yokololayi mpaka liti?

7 Nthawi yokolola imakhala yochepa, choncho alimi amagwira ntchitoyo mwachangu ndipo sakhala ndi nthawi yopuma mpaka ntchitoyo itatha. Nayonso ntchito yokolola mwauzimu ikufunika changu. Kodi tiyenera kugwira ntchito yokololayi mpaka liti? Tiyenera kugwirabe ntchitoyi “m’nyengo ya mapeto a nthawi ino” mpaka “mapeto” adzafike. (Mat. 24:14; 28:20) Mofanana ndi Mtumiki wamkulu wa Yehova, ifenso tikufuna kutsiriza ntchito imene tapatsidwa. (Yoh. 4:34; 17:4) Choncho tiyeni tipitirize kuchita utumiki wathu mwachangu, mwachimwemwe, ndiponso ndi maganizo oyenera mpaka mapeto. (Mat. 24:13) Kukolola sikunathe.

[Chithunzi patsamba 2]

Ntchito yokolola imakhala yambiri kungoyambira pachiyambi mpaka kumapeto

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena