“Mawu a Mulungu . . . Amapatsa Mphamvu”
1 “Mawu a Mulungu ali amoyo ndipo amapatsa mphamvu,” analemba motero mtumwi Paulo. (Aheb. 4:12, NW) Kodi ankatanthauzanji? Anali kutanthauza kuti mawu a Mulungu, kapena kuti uthenga wa m’Baibulo umasonkhezera kwambiri anthu. Mfundo za m’Baibulo zili ndi mphamvu yosintha moyo wa munthu kukhala wabwinopo. Chilimbikitso komanso chiyembekezo cha m’Baibulo zimakokera anthu kwa Wopatsa Moyo, Yehova Mulungu. Uthenga wake umatsogolera anthu oona mtima panjira ya kumoyo wamuyaya. Komabe, kuti zimenezi zichitike, tizigwiritsa ntchito Baibulo polalikira.
2 Ŵerengani Malemba pa Mpata Uliwonse: Zikuoneka kuti ofalitsa ambiri sakonda kugwiritsa ntchito Baibulo polalikira. Kodi inunso mumatero? Popeza anthu ambiri alibe nthaŵi yokambirana nawo zinthu zochuluka, mwinatu mwazoloŵera kungogaŵira mabuku kapena kungolongosola lemba mwachidule. Tikulimbikitsa ofalitsa onse kuti polalikira uthenga wabwino aziyesetsa kuŵerenga m’Baibulo lemba limodzi kapena aŵiri, kuti anthu aziona kuti uthenga wathu ulidi m’Mawu a Mulungu.
3 Ngakhale kuti anthu ochepa ndiwo amakonda kuŵerenga Baibulo, ambiri amalionabe kukhala lofunika. Nthaŵi zambiri ngakhale anthu otanganidwa adzapatula mphindi imodzi kapena ziŵiri kumvetsera uthenga wochokera m’Mawu a Mulungu enieniwo. Tikaŵerenga mwachimwemwe lemba logwirizana ndi nkhani n’kulitanthauzira mwachidule, mphamvu ya mawu a Yehova ingalimbikitse womvetsera kusintha. Koma kodi mungagwirizanitse bwanji mawu anu oyamba ndi kuŵerenga lemba m’Baibulo?
4 Yesani Izi mu Ulaliki wa Magazini: Woyang’anira woyendayenda amagwiritsa ntchito Malemba mogwira mtima mu ulaliki wa magazini. Amatenga Baibulo laling’ono m’thumba. Akagaŵira magazini ndiponso akatha kufotokoza mwachidule nkhani imodzi, amatsegula Baibulo mofulumira ndi kuŵerenga vesi logwirizana ndi nkhaniyo. Mungachite zimenezi mongofunsa kuti, “Mukuganiza bwanji za lonjezo labwino ngati limeneli?” ndiyeno pitirizani mwa kuŵerenga lemba limene mwasankha.
5 Chikhale cholinga chanu kuŵerengera womvetsera aliyense lemba limodzi kapena aŵiri m’Baibulo. Mphamvu yake yosonkhezera ingatsegule njira yoti anthu ambiri ayandikire kwa Mulungu.—Yoh. 6:44.