Kusangalala Kuzikhala ndi Nthaŵi Yake
1 M’masiku ovuta ano, tonsefe timafuna kusintha zochita nthaŵi zina. Kusangalala n’kwabwino kumlingo wina wake. Komabe, kuthera nthaŵi yambiri pa zosangalatsa, maseŵera, ndiponso kucheza kungapangitse munthu kuthera nthaŵi yochepa pa zinthu zauzimu. Kusangalala kuzikhala ndi nthaŵi yake. (Mat. 5:3) Kodi izi zingachitike motani? Mwa kutsatira langizo la pa Aefeso 5:15-17.
2 Kuzikhala ndi Malire: Paulo analemba kuti Akristu afunika ‘kupenya bwino’ momwe angakhalire mwanzeru pa moyo wawo. Kusapambanitsa ndiponso kudziletsa n’kofunika kwambiri kuti tithe kuchepetsa nthaŵi yosangalala ndi kupatsa mpata zinthu zofunika kwambiri. Ndibwino kuona mofatsa momwe timagwiritsira ntchito nthaŵi yomwe timangokhala. Kusangalala kuzitithandiza m’njira zina osati kutipangitsa kuona kuti tataya nthaŵi yathu pachabe kapena kutisiya tili otopa. Ngati pambuyo pa maseŵera tikhala otopa, osasangalala, ndiponso tidzimva kuti tachimwa, n’chizindikiro chakuti tikufunika kusintha momwe timagwiritsira ntchito nthaŵi yathu.
3 Khalani Wanzeru: Paulo analangiza za ‘kuchita machawi, [“kuwombola nthaŵi,”NW]’ ya zinthu zofunika kwambiri m’moyo, osati kukhala “opusa.” Akristu odzipatulira salola moyo wawo kukhala wokondetsa zosangalatsa. Ngakhale kuti kupuma ndi kusangalala kungatipatse mphamvu, koma gwero la mphamvu yauzimu ndilo mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu. (Yes. 40:29-31) Timalandira mzimu wake mwa kuchita zinthu za Mulungu monga kuŵerenga Baibulo, kupezeka pamisonkhano ya mpingo, kutenga mbali mu utumiki wa kumunda osati kudzera m’zosangalatsa.
4 Zinthu Zofunika Zizikhala Patsogolo: Paulo analangiza Akristu ‘kudziŵitsa chifuniro cha Ambuye n’chiyani.” Yesu anaphunzitsa kuti zochita zathu ziyenera kugona pa Ufumu wa Mulungu monga chinthu chofunika kwambiri m’moyo. (Mat. 6:33) N’kofunika kuchita kaye zinthu zimene zidzatithandiza kukhala mogwirizana ndi kudzipatulira kwathu kwa Yehova. Kenako, kusangalala kudzakhala ndi nthaŵi yake. Tikatero, kusangalala kudzakhala ndi zotsatira zabwino, ndipo tidzasangalala nako kwambiri.—Mlal. 5:12.