Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/05 tsamba 1
  • Gwiritsani Ntchito Nthawi Yanu Mwanzeru

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Gwiritsani Ntchito Nthawi Yanu Mwanzeru
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Nkhani Yofanana
  • Kusangalala Kuzikhala ndi Nthaŵi Yake
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Mmene Tingachitire Machaŵi
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Kodi Zimene Mumachita pa Nthawi Yosangalala Zimakhala Zopindulitsa?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kodi N’chiyani Chomwe Mumaika Poyamba M’moyo Wanu?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 9/05 tsamba 1

Gwiritsani Ntchito Nthawi Yanu Mwanzeru

1 Chifukwa chakuti timafuna kukondweretsa Yehova, moyo wathu wonse umakhala pa zinthu zauzimu. Mawu ake amatilangiza kuti ‘tithange tafuna Ufumu’ ndi kutinso ‘titsimikizire zinthu zofunika kwambiri.’ (Mat. 6:33; Afil. 1:10, NW) Kodi tingapeze bwanji nthawi yochita zinthu za Ufumu ndi kuika zinthu zosafunikira kwambiri pa malo ake oyenerera?—Aef. 5:15-17.

2 Ikani Zinthu za Ufumu Patsogolo: Pangani ndandanda yabwino kotero kuti musamawononge nthawi yanu chifukwa cha zinthu zosafunikira kwambiri. Ambiri akamayamba mwezi wina amalemberatu pa kalendala masiku amene adzapita mu utumiki wa kumunda. Ndipo amakhala osamala kuti pasapezeke chilichonse chododometsa dongosolo limeneli. Nanunso mungachite zomwezi kuti mupeze nthawi yopita ku misonkhano ya mpingo, ya phunziro laumwini, ndi yokapezeka ku misonkhano yadera ndi yachigawo. Enanso ali ndi ndandanda ya tsiku lililonse. Malinga ndi ndandandayo, amayamba kapena kumaliza tsiku lililonse ndi kuwerenga Baibulo. Ikani nthawi ya chinthu chilichonse chofunikira, ndipo musalole kuti zinthu zina zosafunikira kwenikweni zikudodometseni.—Mlal. 3:1; 1 Akor. 14:40.

3 Khalani ndi Malire Pogwiritsa Ntchito Zinthu Zimene Dzikoli Limapereka: M’madera ena, masewera, zosangalatsa, zinthu zimene munthu amakonda kuchita, ndi zochita zinanso zambiri zimapezeka mosavuta. Ambiri amawononga nthawi yochuluka kuonera TV kapena kugwiritsa ntchito kompyuta. Komabe, kutangwanika ndi zosangalatsa ndiponso kulakalaka kukhala ndi katundu watsopano amene dzikoli likupanga kungakugwiritseni mwala. (1 Yoh. 2:15-17) N’chifukwa chake Malemba amatilimbikitsa kuti tisachititse nalo dziko lapansi. (1 Akor. 7:31) Pomvera uphungu umenewu, mungam’sonyeze Yehova kuti mumaika kulambira kwake patsogolo m’moyo wanu.—Mat. 6:19-21.

4 Nthawi yomwe yatsala kuti dongosolo lino lithe ndi yochepa kwambiri. Onse amene akuika zinthu za Ufumu patsogolo adzadalitsidwa ndipo adzapeza chiyanjo cha Mulungu. (Miy. 8:32-35; Yak. 1:25) Chotero, tiyeni tigwiritse ntchito nthawi yathu mwanzeru monga chuma chamtengo wapatali.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena