Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/05 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira September 12
  • Mlungu Woyambira September 19
  • Mlungu Woyambira September 26
  • Mlungu Woyambira October 3
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 9/05 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira September 12

Nyimbo Na. 29

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili patsamba 8 (ngati zingakhale zothandiza m’gawo lanu) kuchitira chitsanzo chosonyeza mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya September 15 ndi Galamukani! ya October 8. Mungathe kugwiritsanso ntchito maulaliki ena. Mkulu achite chitsanzo chimodzi ndipo chinacho achite wachinyamata. Pambuyo pa chitsanzo chilichonse, tchulani mbali zina zothandiza zimene azisonyeza m’chitsanzocho. (Ngati magazini amenewa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)

Mph. 20: “Gwiritsani Ntchito Nthawi Yanu Mwanzeru.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene amachitira zinthu kuti tsiku lililonse azikhala ndi nthawi yowerenga Baibulo. Limbikitsani mabanja komanso aliyense payekha kugwiritsa ntchito mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa May 2005 kukonzera ndandanda ya zochita zauzimu.

Mph. 15: “Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Nkhani yokambirana ndi omvera yozikidwa pa gawo 1 ndi 2 la mphatika. Mungathe kuonanso Utumiki Wathu wa Ufumu wa August 2004 tsamba loyamba. Kodi n’chifukwa chiyani kukonzekera mokwanira bwino pa nthawi iliyonse imene tikukachititsa phunziro la Baibulo kuli kofunika? Kodi kuchita zimenezi kumaphatikizapo chiyani? Pemphani omvera kuti afotokoze mmene agwiritsira ntchito mfundo zimene zinaperekedwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu umenewo. Pomaliza fotokozani zimene zili m’bokosi limene lili pamwamba pa tsamba loyamba la mphatikayo.

Nyimbo Na. 110 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira September 19

Nyimbo Na. 168

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kambani mfundo zikuluzikulu za m’kalata yochokera ku nthambi yomwe ili patsamba loyambirira la Utumiki Wathu wa Ufumu uno.

Mph. 20: Kodi Tinachita Zotani Chaka Chatha? Woyang’anira utumiki afotokoze mmene mpingowo wachitira m’chaka cha utumiki chapitachi ndipo afotokoze makamaka mbali zabwino zimene mpingowo unakwanitsa kuchita mu utumiki ndiponso ayamikire mochokera pansi pa mtima. Atchule mbali imodzi kapena ziwiri zimene zikufunika kugwirirapo ntchito m’chaka chimene tayambachi. Afotokoze zimene apainiya anakwanitsa kuchita, ndipo awayamikire chifukwa cha ntchito yawo yabwinoyo. Afotokoze zotsatira zabwino zimene zakhalapo chifukwa chochita khama kuthandiza anthu amene anasiya kulalikira.

Mph. 15: “Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo​—Gawo 12.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Konzeranitu nthawi idakalipo zoti wofalitsa mmodzi kapena awiri adzafotokoze zimene zinawathandiza kuti apite patsogolo pa nkhani yoyambitsa ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo.

Nyimbo Na. 199 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira September 26

Nyimbo Na. 122

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka ochokera ku nthambi olembedwa pa sitetimenti ya mpingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wa kumunda a mwezi wa September.

Mph. 15: Zosowa za pampingo.

Mph. 20: Kulengeza Uthenga Wabwino Pogwiritsa Ntchito Magazini. Mwezi wa October tidzagawira Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Koyambirira kwa nkhani yanu fotokozani mfundo zotsatirazi kuchokera mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa March 2005, tsamba 8, ndime 3 mpaka 6: (1) Kugawira magazini onse awiri. (2) Kukonza zochita ulaliki wa magazini tsiku limodzi mlungu uliwonse. (3) Kukhala ndi cholinga chogawira magazini mwezi uliwonse. (4) Kugwiritsa ntchito mpata uliwonse kugawira magazini. (5) Kugwiritsa ntchito bwino magazini akale. Fotokozani mmene mungagwiritsire ntchito mfundo zimenezi mogwirizana ndi kwanuko. Ndiyeno mukatero sonyezani chitsanzo cha mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya October 1 ndi Galamukani! ya October 8 pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 8 la Utumiki Wathu wa Ufumu uno (ngati zingakhale zothandiza m’gawo lanu). Mungathe kugwiritsanso ntchito maulaliki ena. Kuwonjezera pamenepo, sonyezani nkhani zina m’magaziniwo zimene anthu a m’gawo lanu akhoza kuchita nazo chidwi ndipo sonyezani chitsanzo chimodzi pogwiritsa ntchito imodzi mwa nkhanizo. Pambuyo pa chitsanzo chilichonse, tchulani mbali zina zothandiza zimene azisonyeza m’chitsanzocho. (Ngati magazini amenewa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)

Nyimbo Na. 3 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira October 3

Nyimbo Na. 54

Mph. 5: Zilengezo za pampingo.

Mph. 20: “Thandizani Ena Kuyamba ‘Kumvera ndi Mtima.’” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Ngati nthawi ilipo pemphani omvera kupereka ndemanga pa malemba osagwidwa mawu.

Mph. 20: Kukondweretsa Mtima wa Yehova. (Miy. 27:11) Funsani atumiki a Yehova okhulupirika awiri kapena atatu amene atumikira kwa nthawi yaitali. Apempheni kuti afotokoze chinthu chimodzi kapena ziwiri zimene zawathandiza kuti apitirizebe kumvera Yehova. Zina mwa zinthu zimene angatchule zingaphatikizepo kuchita phunziro laumwini la Baibulo mwakhama, kupezeka pa misonkhano nthawi zonse, kucheza ndi anthu ena okhulupirika, kuchita nawo utumiki wa kumunda ndi mtima wonse, kupemphera mochokera pansi pa mtima, ndiponso kupewa zosangalatsa zoipa. Kodi anakumana ndi ziyeso zotani pa nkhani ya kumvera, ndipo kodi ziyeso zimenezo anazigonjetsa motani? Kodi apeza madalitso otani chifukwa chomvera?

Nyimbo Na. 170 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena