Kodi Mukugwiritsa Ntchito Zimene Munaphunzira ku Msonkhano Wachigawo Wakuti “Aphunzitsi a Mawu a Mulungu”?
1 Onse amene anapezeka pa msonkhano wachigawo wachaka chino, anaona kuti anthu a Yehova ndi otsimikiza kukwaniritsa ntchito yawo yophunzitsa Mawu a Mulungu. (Mat. 28:19, 20) Mutabwerera ku nyumba, kodi ndi mfundo ziti zimene munatsimikiza kuzigwiritsa ntchito m’moyo wanu ndiponso mu utumiki wakumunda?
2 Malemba Ouziridwa Apindulitsa Pophunzitsa: Tsiku loyamba mutu wankhani unachokera pa 2 Timoteo 3:16. Nkhani yaikulu inasonyeza kuti tingakhale “Okonzeka Mokwanira Kukhala Aphunzitsi a Mawu a Mulungu,” mwa kuona Mawu a Mulungu kuti ndi ofunika kwambiri kuwalemekeza kuposa malingaliro kapena miyambo yonse ya anthu, ndiponso kuwagwiritsa ntchito nthaŵi zonse. Tiyeneranso kupempha mzimu woyera tsiku ndi tsiku kuti utithandize mu utumiki wathu ndiponso kukulitsa chipatso chake choyamba chomwe ndi chikondi. Ndipo tigwiritse ntchito misonkhano yonse ya mpingo kuti gulu la Yehova lapadziko lapansi litiphunzitse kukhala atumiki.
3 Lachisanu, nkhani yosiyirana yamutu wakuti, “Kudziphunzitsa Tokha Pamene Tikuphunzitsa Ena,” inafotokoza kuti tizikhala chitsanzo chabwino pa (1) kumvera malamulo a Mulungu okhudza mikhalidwe yonse yachikristu, (2) kukhalabe ndi zizoloŵezi za kuphunzira mwakhama, ndi (3) kuchotsa maganizo ndi zokhumba za mumtima zimene Mdyerekezi angagwiritse ntchito. Ndiyeno, tinaphunzira njira zotetezera mabanja athu ku mliri wa dzikoli wa nkhani zolaula. Makolo analangizidwa kuti azikhala chitsanzo pokana ngakhale kungoonako pang’ono chithunzi cha anthu amaliseche ndiponso kuyang’anira ana awo pamene akugwiritsa ntchito Intaneti ndiponso akuonera wailesi yakanema. Kodi ndi malangizo ati a m’pulogalamu ya Lachisanu, amene mwayamba kuwagwiritsa ntchito?
4 Nkhani yomaliza tsiku limeneli inatilimbikitsa kupitirizabe kuyamikira kuunika kwa Yehova, kumamatira gulu la odzozedwa a Mulungu okhulupirika , ndiponso kulimbikitsa mtendere wa anthu a Yehova. Kodi mwaŵerenga buku latsopano la Ulosi wa Yesaya—Muuni wa Anthu Onse 2?
5 Okhoza Kuphunzitsa Bwino Ena: Patsiku lachiŵiri lemba la mutu wankhani linali 2 Timoteo 2:2. Pamene mumamvetsera nkhani yosiyirana Loŵeruka m’maŵa, kodi munamvetsa malingaliro a mmene (1) tingafunire anthu oyenera, (2) tingakulitsire chidwi chawo, ndi mmene (3) tingawaphunzitsire kusunga zonse zimene Kristu analamula? Kodi mukugwiritsa ntchito zimene munaphunzira zoti muzionetsa mwininyumba mfundo ngakhale imodzi ya m’Malemba ndiponso kuti muziyala maziko a ulendo wotsatira?
6 Pulogalamu yamasana inagogomezera kufunika kotsanzira Mphunzitsi Wamkulu, Yesu. Kodi ndi m’njira ziti zimene mukuyesetsa kuti mufanane naye? Pa zimene munaphunzira m’nkhani yosiyirana yachiŵiri patsikuli, kodi mukuona kuti ndi motani mmene ‘Mungapindulire Mokwanira ndi Maphunziro Ateokalase’? Kodi ndi malingaliro otani amene mwagwiritsa ntchito kuti mukulitse chidwi chanu chomvetsera pa phunziro laumwini ndi misonkhano ya mpingo?
7 Mosakayikira, buku likudzalo lakuti Benefit From Theocratic Ministry School Education lidzatithandiza kukulitsa luso lathu pokamba nkhani ndi pophunzitsa Mawu a Mulungu. Kwenikweni tidzaika maganizo pa luso la kalankhulidwe limene linali chizindikiro cha atumiki okhulupirika a Mulungu m’nthaŵi za m’Baibulo. Phunziro lililonse m’buku latsopanoli lili ndi mabokosi amene amasonyeza mwachidule zimene tikufunika kuchita, chifukwa chake zimenezo zili zofunika, ndi mmene tingazichitire. Mulinso mbali ya zochita. Alongo adzakhala ndi mitundu 29 ya kukambirana yomwe azidzasankha pokamba nkhani zawo. M’kupita kwanthaŵi, zimene asinthazi zizidzachitika m’sukuluyi. Kodi muli ndi chizoloŵezi chabwino chophunzira ndi kukonzekera n’cholinga choti mupindule kwambiri ndi Sukulu ya Utumiki Wateokalase mlungu uliwonse?
8 Khalani Aphunzitsi Chifukwa cha Nyengoyi: Lamlungu, Ahebri 5:12 anadzutsa chidwi cha omvetsera. Nkhani yosiyirana ya m’maŵa yamutu wakuti, “Ulosi wa Malaki Ukutikonzekeretsa Tsiku la Yehova,” inatilimbikitsa kuti tizipatsa Mulungu zinthu zabwino koposa ndiponso tizidana ndi chinyengo cha mtundu uliwonse kuti tidzapulumuke tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova. Seŵero lamutu wakuti “Lemekezani Ulamuliro wa Yehova,” linasonyeza mwamphamvu momwe kunyada, kufuna mpando, nsanje, ndi kukhulupirika konamizira kunachititsira Kora ndi anzake kupandukira Yehova poyera. Nkhani imene inatsatizana ndi seŵeroli inakamba chifukwa chake masiku ano kuli kofunika kugonjera ulamuliro wa Mulungu m’banja kapena mu mpingo. Nkhani ya onse ya mutu wakuti, “Kodi Ndani Amene Akuphunzitsa Mitundu Yonse Choonadi?,” inapereka umboni wakuti Mboni za Yehova ndizo zikuchita zimenezi, osati Matchalitchi Achikristu, amene amangonena kuti amaphunzitsa choonadi cha m’Baibulo.
9 Ndithudi, Yehova akutiphunzitsa kuti tiphunzitse bwino Mawu ake. Tiyeni tigwiritse ntchito zimene tinaphunzira, ‘tidzipenyerere tokha, ndi chiphunzitsocho, kuti tidzipulumutse tokha ndi iwo akumva ife.’—1 Tim. 4:16.