Kulitsani Luso Lanu la Kuzindikira
1 Masiku ovuta otsiriza ano, abweretsa mavuto ambiri ndi ziyeso zazikulu zamitundumitundu pa anthu a Mulungu kulikonse. (2 Tim. 3:1-5) Tonsefe tifunika kulimbikitsidwa kuti tilimbe m’chikhulupiriro. (1 Akor. 16:13) Tingachite zimenezi ndi thandizo la Yehova, mwa kudya nthaŵi zonse Mawu ake, kudalira mzimu wake, ndi kukhalabe m’gulu lake.—Sal. 37:28; Aroma 8:38, 39; Chiv. 2:10.
2 Pachifukwa chomveka, mutu wakuti ‘Khalani Aakulu Misinkhu mu Luso la Kuzindikira’ unakambidwa chaka chatha pa pulogalamu ya tsiku la msonkhano wapadera. Unachokera pa 1 Akorinto 14:20, NW, pamene timaŵerenga mawu a mtumwi Paulo akuti: “Abale, musakhale ana mu luso la kuzindikira, koma khalani makanda m’choipa, komatu khalani aakulu misinkhu mu luso la kuzindikira.” Kodi munaiona bwanji pulogalamuyi?
3 “Inali yolimbikitsa kwambiri!” “Izi ndizo tinkafuna!” Zimenezi ndi zina mwa ndemanga zimene ena anena. Ngakhale munthu amene si Mboni, yemwe anabwera patsiku la msonkhano wapadera kudzaonerera mwana wake wamkazi wazaka 12 akubatizidwa ananena kuti anachita chidwi ndi pulogalamuyi ndiponso anaona momwe ikathandizire banja lake. Kodi ndi momwe munaonera? Tiyeni tibwereze zina mwa mfundo zazikulu za msonkhanowu.
4 Chidziŵitso Cholondola N’chofunika Pokulitsa Luso la Kuzindikira: M’nkhani yoyamba yakuti, “Kulitsani Luso lanu la Kuzindikira Tsopano Lino,” kodi wokamba nkhaniyi anati chofunika n’chiyani kuti tithane ndi mavuto amasiku ano? Tifunika zambiri osati nzeru zokha. Tifunika kukulitsa ndi kuzamitsa luso lathu la kuzindikira Baibulo, kupanda kutero kuipa kumene kuli ponseponse kukhoza kutigonjetsa. Kuzindikira kumeneku kumadza chifukwa cha malangizo a Mulungu. Monga wamasalmo, tizipempha Yehova kutithandiza kumvetsetsa malamulo ndi zikumbutso zake kotero kuti tithe kum’tumikira ndi mtima wonse.—Sal. 119:1, 2, 34.
5 M’mbali yotsatira, woyang’anira dera anasonyeza kuti Yehova, kudzera mwa Mawu ake ndi gulu lake, amatipatsa “Zinthu Zotithandiza Kukhala Aakulu Misinkhu M’kumvetsetsa Baibulo.” Ananena kuti kumvetsa kumatanthauza “kutha kuona chimene nkhani ikutanthauza ndi kuzindikira nkhani yonseyo mwa kumvetsetsa kugwirizana kwa mbali zake zonse ndi mutu wa nkhaniyo, potero mukumamvetsa tanthauzo lake.” Kodi n’ndani angatithandize kukulitsa luso limeneli? Yehova wapereka mphatso mwa amuna kuti zitithandize kupita patsogolo mwauzimu. (Aef. 4:11, 12) Gulu lake lapadziko lapansi limatilimbikitsa kuŵerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse ndi kupezeka nthaŵi zonse pa misonkhano yonse ya mpingo. (Sal. 1:2) Timaphunzitsidwa mmene tingagwiritsire ntchito Baibulo ndi zofalitsa zathu zachikristu pa phunziro laumwini ndi labanja komanso pokonzekera misonkhano ndi utumiki wakumunda. Kodi mwagwiritsa ntchito zinthu zonsezi? Kodi mumatsatira ndandanda yanu yoŵerenga Baibulo nthaŵi zonse? Izi n’zofunika ngati tikufuna kupeŵa ngozi ya zochitika, masitayelo, nzeru, ndi zonyenga za dzikoli.—Akol. 2:6-8.
6 Tiphunzitse Luso Lathu la Kuzindikira: M’nkhani yake yoyamba, ya mutu wakuti “Tetezani Mkhalidwe Wauzimu mwa Kuphunzitsa Luso Lanu la Kuzindikira,” mlendo anafotokoza kuti anthu a m’dziko sasiyanitsa chabwino ndi choipa. (Yes. 5:20, 21) Izi zili choncho chifukwa akana kuvomereza ndi kutsatira malamulo olungama a Mulungu. Mosiyana ndi zimenezo, ife amene taphunzira mwauzimu m’gulu la Yehova timazindikira miyezo ya Mulungu, imene imatsogolera zochita zathu ndiponso makhalidwe athu. Chotero, timatha kuzindikira tokha chinthu chabwino ndi chovomerezeka kwa Yehova komanso chimene chikugwirizana ndi chifuno chake changwiro.—Aroma 12:2.
7 Kuti tipeŵe malingaliro osokonekera a dzikoli ndi zotsatira zake zoipa, tipitirize kuphunzitsa luso lathu la kuzindikira. Kodi izi zingatheke bwanji? Monga alembera pa Ahebri 5:12-14, mtumwi Paulo anagogomezera kufunika kwa kudya chakudya china osati “mkaka” wa mawu wokha. Timafunikira chakudya chauzimu chotafuna, monga chimene tikulandira pophunzira ulosi wa Yesaya pa Phunziro la Buku la Mpingo. Ndiyeno tizigwiritsa ntchito mwamsanga pa moyo wathu zinthu zimene timaphunzira. Tikatero, timatsimikizadi kuti mfundo zachikhalidwe za Yehova komanso miyezo yake n’zolondola. Izi zimaphunzitsa luso lathu la kuzindikira kusiyanitsa bwinobwino chabwino ndi choipa.
8 N’zachisoni kuti ena afooka mwauzimu. Chifukwa chiyani? Sanaike malingaliro awo pa zinthu zimene Yehova amati n’zabwino ndi zolungama. Chotero, akomedwa ndi zochitika zosagwirizana ndi Malemba za anthu otchuka a pa wailesi wamba ndiponso a pa wailesi yakanema, nyimbo zolaula, kapena zinthu zoipa za pa intanenti. Mwa kukhala anzeru, tidzapeŵa kutengera anthu opanda khalidwe, opusa, kapena oipa.—Miy. 13:20; Agal. 5:7; 1 Tim. 6:20, 21.
9 Achinyamata Azikhala “Makanda M’choipa”: Pulogalamuyo inali ndi mbali ziŵiri zolimbikitsa makamaka achinyamata kukulitsa luso lawo la kuzindikira. Wokamba nkhani anasonyeza kuti kukhala “makanda m’choipa” kumatanthauza kukhala wosadziŵa, ndiko kuti, wopanda tchimo monga momwe makanda amakhalira, pa zinthu zimene Yehova amaziona kuti n’zodetsedwa. (1 Akor. 14:20) Tonse tinalimbikitsidwa kukhala atcheru kwambiri ndi mmene timagwiritsira ntchito nthaŵi yathu, kuti tipeŵe zoipa ndi kukhudzidwa nazo. (Aef. 5:15-17) Tinalimbikitsidwa kuŵerengera nthaŵi imene timakhala tikuŵerenga nkhani zimene sizitithandiza mwachindunji kukula m’kumvetsetsa zinthu zauzimu. Kodi munachita zimenezi? Kodi munapeza zotani? Kuwonjezera pa kuŵerenga kwanu Baibulo tsiku ndi tsiku, onetsetsani kuti mukupitirizabe kuŵerenga zofalitsa zimene gulu limatipatsa. Kuchita zimenezi kudzathandiza tonsefe, ndi achinyamata omwe, ‘kutenga luntha.’—Miy. 4:7-9.
10 “Pindulani Pogwiritsa Ntchito Mfundo za Khalidwe Labwino za m’Baibulo Mozindikira”: Ndiwo unali mutu wa nkhani yomaliza papulogalamu yatsiku la msonkhano wapadera. Mlendo anafotokoza kuti Yehova ndi Gwero la kuzindikira kopatsa moyo, kumene kuli kopambana kwambiri pokuyerekezera ndi kuzindikira kwa anthu onse. Tangolingalirani kukhala ndi mwayi wolandirako kuzindikira kwa Yehova! Amapereka kuzindikira moolowa manja kwa anthu amene amafunitsitsa ndi kupempha mwachikhulupiriro. (Miy. 2:3-5, 9; 28:5) Kodi mukugwiritsa ntchito mokwanira mwayi umenewu?
11 Tinalimbikitsidwa kuphunzira kuzindikira mfundo zachikhalidwe poŵerenga Baibulo. (2 Tim. 3:16, 17) Phunzirani mosamala mfundozo kuti mumvetsetse molondola zimene Yehova akunena. Khalani ndi nthaŵi yosinkhasinkha mfundozo ndi kuzikhomereza m’maganizo ndi mu mtima mwanu. Izi zidzakulitsa mphamvu zanu za kuzindikira kuti zikuyendereni bwino posankha zochita m’moyo. (Yos. 1:8) Tiyeni tione zinthu zingapo zimene anthu ambiri amakumana nazo ndi kuona momwe kugwiritsa ntchito mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo kungatithandizire kuchita moyenera.
12 ‘Kodi nditengere kavalidwe ndi kudzikongoletsa kwa anthu ena ake?’ Nthaŵi zambiri masitayelo a dzikoli a zovala ndi kudzikongoletsa amasonyeza mzimu wopanduka. Mzimu umenewu umalimbikitsa anthu kuvala mosasamala ndiponso mosaoneka bwino kapena modzutsa chilakolako cha kugonana. Kodi ndi mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo ziti zimene zingatithandize kupeŵa zizoloŵezi zimenezi? Tikaphunzitsa luso lathu la kuzindikira, tidzalingalira mfundo zachikhalidwe zopezeka pa 1 Timoteo 2:9, 10, kuvala ‘ndi manyazi, ndi chidziletso (umo mokomera [anthu] akuvomereza kulemekeza Mulungu).’ Mfundo zina zachikhalidwe zimene zimagwira ntchito ndi zija zotchulidwa pa 2 Akorinto 6:3 ndi Akolose 3:18, 20.
13 ‘Ndingalimbitse bwanji ubale wa banja langa?’ Kulankhulana kwabwino n’kofunika pabanja. Yakobo 1:19 amatiuza kuti: “Munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.” Anthu pabanja afunika kumvetserana ndi kulankhulana chifukwa kulankhula m’banja kuli ngati katungwe. Ngakhale zitakhala kuti zomwe tikunena ndi zoona, tikanena mwaukali, monyada, kapena mopanda chifundo, mosakayikira zidzakhala zovulaza kwambiri osati zothandiza. Choncho kaya ndife mwamuna wokwatira kapena mkazi wokwatiwa, kholo kapena mwana, nthaŵi zonse mawu athu “akhale m’chisomo, okoleretsa.”—Akol. 4:6.
14 ‘Kodi ndayamba kukondetsa chuma?’ Kukondetsa chuma ndi vuto la padziko lonse limene limawononga moyo wa munthu. Chuma sichithandiza munthu kupeza chimwemwe. (Mlal. 5:10; Luka 12:15; 1 Tim. 6:9, 10) Yesu potithandiza kupeŵa vuto limeneli la kukonda chuma, anaphunzitsa mfundo yachikhalidwe yofunika kwambiri iyi: Khalani ndi diso la kumodzi. Kukhala wamoyo wapakati m’pakati, wosafuna zambiri, kumaphatikizapo kuika maso athu pazinthu za Ufumu, zina zonse kubwera pambuyo.—Mat. 6:22, 23, 33.
15 Chomwe Chiyenera Kukhala Cholinga Chathu: Mawu a Mulungu ndi gwero lodalirika, la mfundo zolungama zachikhalidwe zotithandiza posankha zochita. Tifunika kuphunzira mfundo zimenezi, kusinkhasinkha mfundozo, ndi kuzindikira momwe tingazigwiritsire ntchito m’moyo wathu. Mwa ‘kuphunzitsa luso lathu la kuzindikira kusiyanitsa chabwino ndi choipa’ tidzapindula ndiponso tidzalemekeza Yehova.—Aheb. 5:14, NW.