Pulogalamu Yatsopano ya Tsiku la Msonkhano Wapadera
‘Khalani Aakulu Misinkhu mu Luso la Kuzindikira’ ndiwo mutu wa pulogalamu ya tsiku la msonkhano wapadera kuyambira mu September 2000. (1 Akor. 14:20) N’chifukwa chiyani kuli kofunika kwambiri kuti tikapezekeko? Tikukhala m’dziko lodzaza ndi kuipa. Kuti tipeŵe zimenezi, tiyenera kukulitsa chidziŵitso chathu chauzimu kotero kuti tigonjetse choipa n’chabwino. Zimenezi n’zimene pulogalamu ya tsiku la msonkhano wapadera idzatithandiza kuchita.
M’chigawo choyamba, woyang’anira dera adzakamba nkhani yakuti “Zinthu Zotithandiza Kukhala Aakulu Misinkhu M’kumvetsetsa Baibulo.” Adzatisonyeza mmene tingakhalire olimba m’chikhulupiriro chachikristu. Mlendo adzakamba nkhani ya mutu wakuti “Tetezani Mkhalidwe Wauzimu mwa Kuphunzitsa Luso Lanu la Kuzindikira.” Adzasonyeza chifukwa chake kugwiritsa ntchito mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo kuli kofunika pokulitsa luso la kuzindikira.
Achinyamata ayeneranso kukulitsa chidziŵitso. Zimenezi zikakambidwa pa mutu wakuti “Chifukwa Chake Tiyenera Kukhala Makanda M’choipa” ndiponso pa mutu wakuti “Achinyamata Amene Akupeza Luso la Kuzindikira Lerolino.” Kamveni achinyamata akunena zimene amachita podzilimbitsa mwauzimu kuti athe kuletsa chidwi chilichonse chimene angakhale nacho pa zochitika zoipa za m’dzikoli ndi kupeŵa mavuto.
Kodi tingapeze bwanji chimwemwe chochuluka m’moyo? Mlendo adzalongosola zimenezi m’nkhani yothera ya mutu wakuti “Pindulani Pogwiritsa Ntchito Mfundo za Khalidwe Labwino za M’Baibulo Mozindikira.” Adzapereka zitsanzo kusonyeza kuti kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu kumatithandiza kuthana ndi mavuto, kusankha zochita, ndi kupindula kwambiri ndi zimene Yehova akutiphunzitsa.
Amene akufuna kukasonyeza kudzipatulira kwawo kwa Mulungu mwa kubatizidwa pamsonkhano ayenera kudziŵitsa woyang’anira wotsogolera mwamsanga. Pakalendala yanu ikani chizindikiro patsiku la msonkhano wapadera likalengezedwa, ndipo pangani zotheka kuti mukapindule ndi pulogalamu yabwinoyi. Musadzaphonye mbali iliyonse ya tsiku la msonkhano wapadera! Idzakulimbikitsani kupirira dongosolo loipali ndi kukhalabe okhulupirika kwa Yehova.