Programu Yatsopano ya Tsiku la Msonkhano Wapadera
Makonzedwe a masiku a msonkhano wapadera anayamba mu 1987. Misonkhano ya tsiku limodzi imeneyi yakhaladi yomangirira kwa atumiki a Yehova ndi okondwerera amene amapezekapo. Kuyambira mu September 1998, tidzakhala ndi programu yatsopano ya tsiku la msonkhano wapadera. Nkhani zisanu ndi zinayi, kufunsa ndi zokumana nazo zambirimbirizo zidzakhaladi zopindulitsa mwauzimu kwa inu.
“Kuyamikira Gome la Yehova” ndiwo mutu wa programu yatsopanoyi. (Yes. 65:14; 1 Akor. 10:21) Idzalimbikitsa chosankha chathu chakuti kulambira Yehova kuyenera kukhala chinthu choyamba m’miyoyo yathu. (Sal. 27:4) Nkhani ya woyang’anira dera idzalongosola za “Kusanthula Zolingirira za Mitima Yathu” kulinga ku kupezeka pamisonkhano. Mlendo adzatisonyeza mmene ‘tingakhalirebe auzimu mwa kudya pagome la Yehova.’ Achinyamata m’gulu la Yehova adzapatsidwanso chilimbikitso chenicheni cha mmene angakhalire olimba potumikira Mulungu. Nkhani yaikulu ya mlendo yamutu wakuti “Olimba Mwauzimu Kuti Tipereke Umboni Wamphamvu,” idzasonyeza mmene zimene timalandira kupyolera mumpingo zimatikonzekeretsera kuchitira umboni Ufumu mwamphamvu. Ndani amene sangafune kupindula ndi programu imeneyi?
Odzipatulira kumene amene akufuna kudzabatizidwa ayenera kudziŵitsa woyang’anira wotsogoza mwamsanga. Tili otsimikizira kuti pamene tikuyamba chaka cha 12 cha makonzedwe a tsiku la msonkhano wapadera, aliyense amene adzapezekapo adzalimbikitsidwa mwauzimu kaamba ka ntchito ya mtsogolo.