Programu Yatsopano ya Tsiku la msonkhano Wapadera
1 “Khalani Anthu Ophunzitsidwa ndi Yehova” ndiwo mutu wa programu yatsopano ya tsiku la msonkhano wapadera imene idzayamba mu September. (Yohane 6:45, NW) Chiphunzitso chaumulungu chochokera kwa Yehova chimatithandizadi kukhala ndi moyo wokhutiritsa. Chimakulitsa mwa ife chiyamikiro chenicheni cha choloŵa chathu chauzimu. Kuyesayesa kwathu kuthandiza ena kumva uthenga wabwino kumatipangitsa kukhala anthu ofunika m’chitaganya. Tsiku la msonkhano wapadera limeneli lidzasonyeza madalitso amene ali ndi anthu ophunzitsidwa ndi Yehova.
2 Programu imeneyi idzasiyanitsa mapindu a chiphunzitso chaumulungu ndi ngozi za maphunziro akudziko. Tidzaona bwino lomwe mmene Yehova amaperekera mtundu wapamwamba koposa wa maphunziro—maphunziro ozikidwa pa Mawu ake, Baibulo. Mbali zitatu za kulambira zimene timasangalala nazo pokhala ophunzitsidwa ndi Mulungu zidzagogomezeredwa. Ndiponso, achichepere adzalimbikitsidwa kutsanzira zitsanzo zapadera za m’Baibulo monga Davide ndi Timoteo ndi kusumika moyo wawo pa ntchito zauzimu. Chikhulupiriro chathu chidzalimbitsidwa pamenenso kukhulupirika kwa okalamba kudzasonyezedwa. Odzipatulira chatsopano amene ayeneretsedwa adzabatizidwa. Iwo ayenera kudziŵitsa woyang’anira wotsogoza za chikhumbo chimenecho tsiku la msonkhano limeneli likali kutali.
3 Nkhani yaikulu ya tsiku la msonkhano wapadera umenewu ili ndi mutu wakuti “Ophunzitsidwa ndi Yehova Kuchita Chifuniro Chake.” Idzagogomezera zifukwa zimene tonsefe tifunikira kupitirizabe kuphunzira, kukhazikika m’chikhulupiriro, ndi kupitiriza kupita patsogolo. Tidzalimbikitsidwa kutsanzira Yehova mwa kuphunzitsa ena choonadi chotsogolera ku moyo wosatha. Zokumana nazo zolimbikitsa zosonyeza mmene zofalitsa za Sosaite zathandizira ambiri kukhala ophunzitsidwa ndi Yehova zidzaphatikizidwa. Zotulukapo zabwino za programu yophunzitsa ya padziko lonse ya Yehova zidzafotokozedwa.
4 Pangani makonzedwe otsimikizirika kuti mukapezekepo. Limbikitsani okondwerera onse kukapezekapo. Yembekezerani kudzaphunzitsidwa zinthu zabwino zambiri ndi Mlangizi wathu Wamkulu.—Yes. 30:20.