Programu Yatsopano ya Tsiku la Msonkhano Wapadera
‘Chitani Zonse Chifukwa cha Uthenga Wabwino’ ndiwo mutu wa programu yatsopano ya tsiku la msonkhano wapadera kuyambira m’September. (1 Akor. 9:23) Uthenga wabwino wa Ufumu ndiwo uthenga wofunika kwambiri umene ukumveka lerolino. Programuyo idzatithandiza kuyamikira mwaŵi wapadera umene tili nawo wofalitsa uthenga wodabwitsa umenewu. Idzatilimbikitsanso kusaleka kulengeza uthenga wabwino.—Mac. 5:42.
Programuyo idzatisonyeza mmene tingagwiritsirire ntchito maphunziro athu ateokrase kuti tichite zochuluka mu utumiki. Tidzamva za ena amene anasintha zochita zawo kuti afutukule utumiki wawo, kuphatikizapo achinyamata omwe adzipereka kuwanditsa uthenga wabwino.—Yerekezerani ndi Afilipi 2:22.
Nkhani yaikulu imene idzakambidwa ndi mlendo, idzagogomezera kufunika kwa kukhalabe ‘ovomerezeka kuikizidwa Uthenga Wabwino.’ (1 Ates. 2:4) Idzatithandiza kuona kuti ngati titi tisungebe udindo wathu wakuuza ena uthenga wabwino, maganizo athu ndi khalidwe ziyenera kugwirizanabe ndi zofuna za Mulungu ndi malamulo ake. Idzagogomezeranso madalitso amene tidzalandira chifukwa chochita zimenezo.
Musaphonye programu yofunika imeneyi. Odzipatulira chatsopano amene akufuna kubatizidwa patsiku la msonkhano wapadera ayenera kudziŵitsa msanga woyang’anira wotsogoza. Itanani onse amene mumaphunzira nawo kuti adzapezekepo. Tiyeni tilole Yehova atilimbikitse kuchita zonse chifukwa cha uthenga wabwino ndi kuti titsirize ntchito yaikuluyi tidakali tsidya lino la Armagedo.