Programu Yatsopano ya tsiku la Msonkhano Wapadera
1 Kodi nchifukwa ninji tiyenera kulengeza uthenga wabwino kosaleka? Kodi ziyeneretso zofunika kuti munthu akhale mlaliki wa uthenga wabwino nzotani? Kodi ndimotani mmene ngakhale anthu amanyazi ndi amantha angayambire kuuza ena uthenga wabwino? Mafunso ameneŵa ndi ena osonkhezera maganizo adzayankhidwa m’programu ya tsiku la msonkhano wapadera imene idzayamba mu September, ya mutu wakuti “Oyenera Kukhala Atumiki a Uthenga Wabwino.”—Yerekezerani ndi 2 Akorinto 3:5, NW.
2 Monga anthu a Yehova, tiyenera kukhala osamala khalidwe lathu. Zokumana nazo zolimbikitsa zidzasimbidwa ndi achichepere amene adzafotokoza mmene akanizira zitsenderezo za ausinkhu wawo. Makolo adzapatsidwa chilimbikitso chachikondi pa kufunika kwa kuphunzitsa ana awo kukhala atumiki a Mulungu. Ife tonse tidzathandizidwa kuzindikira kufunika kwa kulalikira ndi madalitso amene amakhalapo ponse paŵiri kwa ife eni ndi kwa awo amene amatimvetsera.—1 Tim. 4:16.
3 Zoonadi ubatizo udzakhala chinthu chapadera cha tsikulo. Nthaŵi ya chochitika chimenechi isanafike, nkhani yozikidwa pa Baibulo idzaperekedwa makamaka kwa anthu odzipatulira chatsopano. Ndithudi, onse amene adzakhalapo adzafunikira kumvetsera mosamalitsa pamene nkhani ya ubatizoyo ikukambidwa ndi pamene tanthauzo lake likumveketsedwa bwino. Aliyense amene akufuna kudzabatizidwa pa tsiku la msonkhano wapadera ayenera kudziŵitsa woyang’anira wotsogoza pasadakhale kotero kuti apeze nthaŵi ya kusankha akulu oti apende mafunso olinganizidwa ndi oyembekezera ubatizo.
4 Chochitika china chapadera chidzakhala nkhani yaikulu yokambidwa ndi mlankhuli amene ali mlendo. Ili ndi mutu wakuti “Atumiki a Mulungu Oyenera ndi Okonzekeretsedwa.” Njira zazikulu zinayi zimene zimatikonzekeretsa kukhala atumiki zidzafotokozedwa, ndipo nkhaniyo idzaphatikizapo zokumana nazo zolimbikitsa chikhulupiriro.
5 Yambani tsopano kukonzekera kuti mudzakhalepo pa programu yonse. Tsimikizirani kuitana anthu okondwerera ndi ophunzira Baibulo kuti nawonso adzapindule ndi tsiku limeneli la maphunziro a teokrase. Mwanjira imeneyi tidzasonyezadi kuti tili “oyenera bwino” monga atumiki a uthenga wabwino.