Lunjikani Nawo Bwino Mawu a Mulungu
1 Pamene ankalalikira kwa kazembe, “Filipo anatsegula pakamwa pake, nayamba pa lembo [linalake], nalalikira kwa iye [za] Yesu.” (Mac. 8:35) Filipo ‘analunjika nawo bwino mawu a choonadi.’ (2 Tim. 2:15) Koma masiku ano, oyang’anira oyendayenda aona kuti ofalitsa ambiri sakonda kugwiritsa ntchito Baibulo polalikira. Kodi mumagwiritsa ntchito Baibulo mu utumiki wanu?
2 Mawu a Mulungu ndi gwero la zonse zimene timakhulupirira ndi kuphunzitsa. (2 Tim. 3:16, 17) Ndi limene limakokera anthu kwa Yehova ndi kuwaphunzitsa kuti akapeze moyo. Ndicho chifukwa chake kuli kofunika kugwiritsa ntchito Baibulo mu utumiki wathu m’malo mongokamba pakamwa nkhani zimene zimatisangalatsa. (Aheb. 4:12) Chifukwa chakuti anthu ambiri salidziŵa kwambiri Baibulo, tiziŵerenga m’Baibulo mwenimwenimo powasonyeza malangizo abwino amene lili nawo ndiponso zimene zidzachitikire anthu m’tsogolomu.
3 Ŵerengani m’Baibulo Mwenimwenimo: Popita kukalalikira yesani kupita opanda chikwama cha mabuku. Ikani mabuku amene mukukagaŵira m’kachikwana kakang’ono ndipo tengerani Baibulo m’manja kapena m’thumba. Ndiyeno, mukamakambirana ndi munthu wina, tengani Baibulolo koma musam’chititse munthuyo kuganiza kuti mukufuna kumulalikira kwa nthaŵi yaitali. Imani bwinobwino moti iye aziona nawo m’Baibulo lanulo. Mwina mungam’pemphe kuti aŵerenge vesi mokweza. Akaona zimene Baibulo likunena zimakhazikika kwambiri m’maganizo ake kulekana ndi kungomva zimene inu mukunena. Inde, kuti mum’thandize kumvetsa mfundo ya lembalo, tchulani motsindika mawu a m’vesilo amene akugogomezera mfundo imene mukukambiranayo.
4 Ulaliki wa Lemba Limodzi: Mukamuuza dzina lanu ndi chomwe mwafikira kumeneko, munganene kuti: “Anthu amafunafuna malangizo a moyo wawo kwa anthu osiyanasiyana. Kodi mukuganiza kuti tingapeze kuti malangizo othandiza? [Yembekezani ayankhe.] Kodi mukutipo chiyani pa mawu aŵa? [Ŵerengani Miyambo 2:6, 7, ndipo yembekezani kuti ayankhe.] Nzeru za anthu n’zopereŵera kwambiri, zimasiya anthu ambiri ali otaya mtima. Komano, nzeru za Mulungu, nthaŵi zonse ndi zodalirika ndi zothandiza.” Ndiyeno onetsani buku limene mukugaŵira, ndipo tchulani chitsanzo chimodzi m’bukulo cha nzeru yothandiza ya Mulungu.
5 Yesu anagwiritsa ntchito Malemba kuthandiza anthu oona mtima. (Luka 24:32) Paulo ankapereka umboni wa m’Malemba pa zinthu zimene anali kuphunzitsa. (Mac. 17:2, 3) Tidzatha kudzidalira kwambiri ndi kupeza chimwemwe chachikulu mu utumiki ngati tikhala aluso kwambiri polunjika nawo bwino Mawu a Mulungu.