Pulogalamu Yatsopano ya Msonkhano Wadera
1 Kuti tikhale olimba m’chikhulupiriro m’dziko losinthasintha lino, tiyenera kukhulupirira Yehova. Kodi tingasonyeze motani zimenezi pamoyo wathu watsiku ndi tsiku? Kodi kukhulupirira Yehova kumakhudza motani moyo wathu ndiponso wabanja lathu? Kodi kumatithandiza motani kukana mphamvu ya dziko la Satana? Pulogalamu ya msonkhano wadera ya chaka chautumiki cha 2003 idzayankha mafunso ameneŵa. Mutu wake ndi wakuti “Khulupirirani Yehova, Ndipo Chitani Chokoma.”—Sal. 37:3.
2 Sitikhulupirira Yehova panthaŵi zapadera zokha kapena tikakhala pavuto lalikulu pokha ayi. Kukhulupirira Yehova kumakhudza mbali zonse za moyo wathu watsiku ndi tsiku. Nkhani yoyamba yakuti “Khulupirirani Yehova Nyengo Zonse” idzagogomezera zimenezi. (Sal. 62:8) Nkhani yosiyirana ya mbali zinayi yamutu wakuti “Kusonyeza Kukhulupirira Yehova” idzatiuza momwe tingapezere malangizo a m’Baibulo amene angatithandize kumanga banja labwino, kuthetsa mavuto amene angabuke m’banja, ndiponso malangizo amene angatithandize kupeza zosoŵa zathu. Komanso idzatiuza momwe tingawagwiritsire ntchito malangizowo.
3 Dziko la Satana limayesa kutisokoneza maganizo pankhani ya chabwino ndi choipa ndiponso chimene chili chofunika kwambiri m’moyo ndi chimene chili chosafunika. (Yes. 5:20) Nkhani zakuti “Peŵani Zinthu Zopanda Pake m’Moyo” ndi “Peŵani Zoipa—Khalani Ochita Zabwino” zidzalimbikitsa zimene tasankha zochirikiza malamulo apamwamba a Yehova.—Amosi 5:14.
4 Pamene Yehova azidzawononga dongosolo la zinthu loipa limene lilipoli, atumiki a Mulungu adzafunika kum’khulupirira kwambiri. Izi n’zimene akagogomezere mu nkhani ya onse yakuti “Kupulumutsidwa M’mavuto a Dzikoli Kwayandikira.” Kenako, mu nkhani yakuti “Kodi Mudzayesedwa Oyenera Ufumu wa Mulungu?” akatipempha mwachikondi kuti tidzipende. Pulogalamuyi idzatha ndi langizo lakuti “Khulupirirani Malonjezo a Yehova.”
5 Mbali yosangalatsa kwambiri pa msonkhano wadera uliwonse ndiyo nkhani ya ubatizo. Aliyense amene akufuna kubatizidwa auze woyang’anira wotsogolera mofulumira kuti akonze dongosolo lofunika.
6 M’nthaŵi zosadalirika zino, Yehova yekha ndiye gwero lenileni la chidaliro ndiponso chilimbikitso. (Sal. 118:8, 9) Tonsefe tiyeni tilimbitse chikhulupiriro chathu mwa iye mwa kudzapezeka pa pulogalamu yonse ya msonkhano wadera.