Khalani Wokhulupirika ku Chikristu Wachibale Akachotsedwa mu Mpingo
1. Kodi n’chiyani chingayese kukhulupirika kwa Mkristu?
1 Anthu a m’banja limodzi angakondane zedi. Zimenezi zimaika pachiyeso Mkristu ngati mnzake amene anamanga naye banja, mwana wake, kholo lake kapena wachibale weniweni wachotsedwa mu mpingo kapena wadzilekanitsa yekha ndi mpingo. (Mat. 10:37) Kodi Akristu okhulupirika azikhala naye bwanji wachibale wotereyu? Kodi ngati akukhala naye m’nyumba imodzi, ayenera kukhala momwe anali kukhalira asanachotsedwe? Choyamba, tiyeni tione zimene Baibulo limanena pankhaniyi, mfundo zimene zimagwira ntchito kwa ochotsedwa ndiponso kwa odzilekanitsa.
2. Malinga ndi zimene Baibulo limanena, kodi Akristu ayenera kuchita motani ndi anthu ochotsedwa?
2 Momwe Tiyenera Kuchitira ndi Anthu Ochotsedwa: Mawu a Mulungu amalamula Akristu kuti asacheze kapena kuyanjana ndi munthu amene wachotsedwa mu mpingo. Amati: ‘Musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kukadya naye wotere, iyayi. Chotsani woipayo pakati panu.’ (1 Akor. 5:11, 13) Mawu a Yesu a pa Mateyu 18:17 amagwiranso ntchito pankhaniyi, amati: “Akhale [munthu wochotsedwayo] kwa iwe monga wakunja ndi wamsonkho.” Omvetsera a Yesu ankadziŵa bwino kuti Ayuda m’masiku amenewo sankacheza ndi anthu Akunja ndiponso ankapeŵa okhometsa msonkho chifukwa ankawaona ngati odetsedwa. Chotero Yesu anali kulangiza otsatira ake kuti asamacheze ndi anthu ochotsedwa.—Onani Nsanja ya Olonda ya March 15, 1982, masamba 16-19.
3, 4. Kodi ndi mayanjano ati amene akuletsedwa kuchita ndi anthu ochotsedwa ndi odzilekanitsa?
3 Izi zikutanthauza kuti Akristu okhulupirika sayenera kukambirana nkhani zauzimu ndi munthu aliyense wochotsedwa mu mpingo. Komabe pali zambiri zimene sitifunika kuchita ndi anthu ameneŵa. Mawu a Mulungu amati sitiyenera ‘ngakhale kudya naye wotere, iyayi.’ (1 Akor. 5:11) Choncho, timapeŵanso kucheza nkhani wamba ndi munthu wochotsedwa. Zimenezi zikutanthauza kuti sitiyenera kupita naye limodzi kokasangalala, ku phwando, koseŵera mpira, kapena, kudyera naye pamodzi kunyumba kapena ku lesitiranti.
4 Bwanji nanga kulankhula ndi munthu wochotsedwa? Ngakhale kuti Baibulo silinena zonse zimene sitiyenera kuchita ndi anthu ameneŵa, pa 2 Yohane 10 pamatithandiza kuona maganizo a Yehova pankhaniyi. Lembali limati: “Munthu akadza kwa inu, wosatenga chiphunzitso ichi, musam’landire iye kunyumba, ndipo musam’lankhule.” Pothirira ndemanga pa mawu ameneŵa, Nsanja ya Olonda ya March 15, 1982, patsamba 24 inati: ‘Kupereka ‘‘moni” yekha kwa munthu wina kungakhale sitepe loyambira kukambirana ngakhale ubwenzi umene. Kodi tikufuna kuyamba sitepe limeneli ndi munthu wochotsedwa?’
5. Munthu akachotsedwa, amataya chiyani?
5 Inde, n’zofanana ndi zimene Nsanja ya Olonda tatchula ija inanena patsamba 31, inati: ‘Mfundo ndi yakuti Mkristu akachimwa n’kuchotsedwa amataya zambiri: unansi wake wabwino ndi Mulungu; mayanjano abwino ndi abale, komanso mayanjano ochuluka amene anali nawo ndi achibale achikristu.’
6. Kodi Mkristu akufunika kusiyiratu kucheza ndi wachibale wochotsedwa amene akukhala naye m’nyumba imodzi? Fotokozani.
6 Okhala m’Nyumba Imodzi: Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Akristu amene amakhala ndi wachibale wochotsedwa asamalankhule naye, kudyera naye pamodzi ndiponso kucheza naye pogwira ntchito zawo zatsiku ndi tsiku? Nsanja ya Olonda ya April 15, 1991, pa mawu a m’munsi patsamba 22 inati: “Ngati m’banja lachikristu muli wachibale wochotsedwa, iye akakhalabe ndi phande m’zochitika zanthaŵi zonse za tsiku ndi tsiku zabanjalo.” Choncho, zili kwa achibale apanyumbapo kusankha kuti azifika mpaka pati pankhani ya kudyera pamodzi ndi munthu wochotsedwayo kapena pogwirira naye pamodzi ntchito zina za pakhomopo. Komabe, asapereke chithunzi kwa abale amene amasonkhana nawo kuti palibe chimene chasintha zonse zili monga zinalili asanachotsedwe.
7. Kodi mayanjano auzimu amasintha bwanji m’banja ngati wina ndi wochotsedwa?
7 Komabe, Nsanja ya Olonda ya March 15, 1982, patsamba 27, inatchula zina zokhudza munthu wochotsedwa kapena wodzilekanitsa. Inati: ‘Mayanjano auzimu amene ankakhalapo amatheratu. Zimenezi zimakhala choncho ngakhale kwa achibale ake, kuphatikizapo amene akukhala nawo m’nyumba imodzi. . . . Zimenezi zikutanthauza kuti mayanjano auzimu amene ankakhala m’banjamo amasintha. Mwachitsanzo, ngati mwamuna wachotsedwa, mkazi wake ndi ana sangamve bwino kuti iye azichititsa phunziro la Baibulo la banja kapena kutsogoza kuŵerenga Baibulo ndi pemphero. Ngati iye akufuna kupemphera monga panthaŵi ya chakudya, ali ndi ufulu wochita zimenezo m’nyumba mwakemo. Koma iwo chamumtima angapemphere mapemphero awoawo kwa Mulungu. (Miy. 28:9; Sal. 119:145, 146) Bwanji ngati munthu wochotsedwayo akufuna kukhalapo pamene banjalo likuŵerenga Baibulo pamodzi kapena likuchita phunziro la Baibulo? Enawo angamulole kukhalapo kuti amvetsere ngati iye sadzayamba kuwaphunzitsa kapena kunena zikhulupiriro za chipembedzo chake.’
8. Kodi makolo achikristu ali ndi udindo wotani pa mwana wochotsedwa amene amakhala naye nyumba imodzi?
8 Ngati mwana wamng’ono pabanjapo wachotsedwa, makolo achikristu amakhalabe ndi udindo wom’lera. Nsanja ya Olonda ya November 15, 1988, patsamba 20 inati: ‘Mongadi mmene iwo akapitirizira kumpatsa chakudya, zovala, ndi malo ogona, afunikanso kumulangiza ndi kumulanga mogwirizana ndi Mawu a Mulungu. (Miy. 6:20-22; 29:17) Choncho makolo achikondi angakonze zophunzira naye Baibulo, ngakhale kuti ndi wochotsedwa. Mwinamwake iye angapindule kwambiri ndi malangizo omuthandiza kusintha mwa kuphunzira naye payekha. Kapena iwo angasankhe kuti iye apitirizebe kukhala nawo pa phunziro la banja.’—Onaninso Nsanja ya Olonda ya October 1, 2001, masamba 16-17.
9. Kodi Mkristu angalankhule kufika pati ndi mbale wake wochotsedwa amene amakhala kwina?
9 Achibale Okhala Kwina: ‘Zimasiyana ngati wochotsedwayo kapena wodzilekanitsayo ali wachibale amene amakhala kwina,’ inatero Nsanja ya Olonda ya April 15, 1988, patsamba 28. ‘Zikhoza kutheka kusalankhulana naye m’pang’ono pomwe. Ngakhale kuti pangakhale nkhani zina za pachibale zofunika kukambirana naye, zimenezi zizichitika kamodzikamodzi,’ malinga ndi lamulo la Mulungu lakuti: ‘musayanjane naye, ngati wina’ wachita tchimo osalapa. (1 Akor. 5:11) Akristu okhulupirika aziyesetsa kupeŵa kuyanjana popanda chifukwa chenicheni ndi wachibale wotereyo, komanso azichepetsa nkhani zawo za malonda.—Onaninso Nsanja ya Olonda ya March 15, 1982, masamba 29-30.
10, 11. Kodi Mkristu afunika kulingalira chiyani asanalole wachibale wochotsedwa kudzakhala naye panyumba yake?
10 Nsanja ya Olonda ikutiuzanso china chimene chingachitike: ‘Bwanji ngati wachibale weniweni monga, mwana wamwamuna kapena kholo amene sakhala m’banjamo wachotsedwa, ndiyeno akufuna kubwera panyumbapo? Banjalo lingasankhe zochita malinga ndi mmene zinthu zilili. Mwachitsanzo, kholo lochotsedwa lingakhale likudwala kapena likulephera kupeza ndalama kapena kudzisamalira mwakuthupi. Ana achikristu ali ndi udindo wa m’Malemba ndi wa makhalidwe abwino wowathandiza. (1 Tim. 5:8) . . . Zimene angachite zimadalira pa zosoŵa zenizeni za khololo, mtima wake ndiponso nkhaŵa imene mutu wa banjalo uli nayo pa moyo wauzimu wa banjalo.’—Nsanja ya Olonda ya March 15, 1982 masamba 28-9.
11 Ponena za mwana, nkhani yomweyi inati: “Nthaŵi zina makolo achikristu alolanso mwana wawo wochotsedwa amene akudwala kudzakhala panyumbapo kwakanthaŵi. Komabe mulimonse momwe zingakhalire, makolowo angaone mmene zinthu zilili kwa munthuyo. Kodi mwana wochotsedwayo wakhala akudzisamalira yekha, ndipo tsopano sangathe kutero? Kapena kodi iye akungofuna kubwerera chifukwa chakuti moyo ukakhala wosavutirapo? Bwanji ponena za makhalidwe ake ndi malingaliro ake? Kodi adzaloŵetsa ‘chotupitsa’ m’banjamo?—Agal. 5:9.”
12. Kodi kuchotsa anthu mumpingo n’kopindulitsa motani?
12 Phindu Lokhala Wokhulupirika kwa Yehova: Kumvera dongosolo la m’Malemba lochotsa ndi lopeŵa anthu amene amachita machimo mosalapa, n’kopindulitsa. Kumapangitsa mpingo kukhalabe woyera ndipo kumatipangitsa kukhala anthu ochirikiza miyezo yapamwamba ya makhalidwe abwino ya m’Baibulo. (1 Pet. 1:14-16) Kumatiteteza ku zinthu zoipa. (Agal. 5:7-9) Kumapatsanso mpata munthu wochimwayo kuti apindule kwambiri ndi chilango chimene walandira, zimene zingamuthandize kusonyeza ‘chipatso cha mtendere, ndicho cha chilungamo.’—Aheb. 12:11.
13. Kodi banja lina linachita zotani, ndipo zotsatira zake zinali zotani?
13 Atamvetsera nkhani ya pamsonkhano wadera, mbale wina ndi mchemwali wake anaona kuti anafunika kusintha momwe ankachitira zinthu ndi amayi awo, amene anali kukhala kwina ndiponso anali ochotsedwa kwa zaka zisanu ndi chimodzi. Msonkhanowo utangotha, mbaleyu anaitana amayi ake, ndipo atatha kuwauza kuti amawakonda, anawafotokozera kuti iye ndi mchemwali wakeyo saziwalankhula, aziwalankhula ngati pali nkhani zofunika kwambiri za pachibale zoti akambirane. Patapita nthaŵi pang’ono, mayi ake aja anayamba kupita ku misonkhano ndipo m’kupita kwa nthaŵi anabwezeretsedwa mu mpingo. Komanso mwamuna wa mayiyu yemwe anali wosakhulupirira, anayamba kuphunzira ndipo m’kupita kwa nthaŵi anabatizidwa.
14. N’chifukwa chiyani tifunika kutsatira mokhulupirika dongosolo lochotsa anthu mu mpingo?
14 Kutsatira mokhulupirika dongosolo la kuchotsa anthu mu mpingo lomwe alifotokoza m’Malemba kumasonyeza kuti timakonda Yehova ndipo kumayankha yemwe amamutonza. (Miy. 27:11) Komanso, tingakhale otsimikiza kuti Yehova adzatidalitsa. Mfumu Davide ponena za Yehova analemba kuti: ‘Za malemba ake, sindidzawapambukira. Ndi achifundo (“wokhulupirika,” NW) inu mudzadziwonetsa wachifundo (“wokhulupirika,”).’—2 Sam. 22:23, 26.