Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w13 8/15 tsamba 8
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
  • Nsanja ya Olonda—2013
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Tiyenera Kuchitira ndi Munthu Wochotsedwa
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Khalani Wokhulupirika ku Chikristu Wachibale Akachotsedwa mu Mpingo
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Tizikonda Yehova Kuposa Mmene Timakondera Achibale Athu
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Tsanzirani Chifundo cha Mulungu Lerolino
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2013
w13 8/15 tsamba 8

MAFUNSO OCHOKERA KWA OWERENGA

Kodi n’zoyenera kuti makolo achikhristu azikhala pamodzi ndi mwana wawo wochotsedwa pa misonkhano yampingo?

Malo okhala munthu wochotsedwa m’Nyumba ya Ufumu si nkhani yaikulu. Magazini a Nsanja ya Olonda akhala akulimbikitsa makolo achikhristu kuti ngati zili zoyenera, azithandiza ana awo ochotsedwa amene akukhalabe pakhomo. Mwachitsanzo, Nsanja ya Olonda ya November 15, 1988, patsamba 19 ndi 20, imanena kuti makolo akhoza kumaphunzira Baibulo ndi mwana wawo wachinyamata amene wachotsedwa ngati akukhalabe pakhomopo. Mwina zimenezi zingathandize kuti mwanayo asinthe n’kuyambanso kutumikira Yehova.

Ngati wachinyamata wochotsedwa wabwera ku misonkhano pa Nyumba ya Ufumu, akhoza kukhala limodzi ndi makolo ake. Palibe lamulo loti ochotsedwa azikhala pampando wakumbuyo. Choncho palibe vuto ngati mwana wochotsedwa angakhale pamalo alionse amene makolo ake akhala. Popeza makolo ali ndi udindo wothandiza mwana wawoyo kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu, iwo angachite bwino kuonetsetsa kuti akupindula ndi misonkhano. Kukhala naye pamalo amodzi kungathandize kuti achite zimenezi.

Koma bwanji ngati wochotsedwayo anachoka kunyumba ya makolo ake? Kodi mfundo imene tikunenayi ingagwirenso ntchito? M’mbuyomu, magazini a Nsanja ya Olonda akhala akufotokozanso zimene Mkhristu ayenera kuchita ngati wachibale wake wochotsedwa sakukhalanso pakhomopo.a Komabe anthu akalola kuti wachibale wochotsedwa akhale phee limodzi nawo pa nthawi ya misonkhano zimakhala zosiyana kwambiri ndi kulankhulana naye popanda zifukwa zomveka. Limeneli si vuto ngati achibalewo amaona munthu wochotsedwayo moyenera ndipo amayesetsa kutsatira malangizo a m’Malemba okhudza kuyanjana ndi ochotsedwa.—1 Akor. 5:11, 13; 2 Yoh. 11.

Choncho, palibe vuto ngati munthu wochotsedwa, yemwe sakuvutitsa aliyense, wakhala limodzi ndi wachibale wake kapena munthu wina aliyense pa misonkhano. Kuletsa munthu kukhala pamalo enaake kungayambitse mavuto ena. Ngati anthu onse pa misonkhano komanso achibale a wochotsedwayo akutsatira malangizo a m’Malemba pa nkhani ya ochotsedwa, ndiponso zochita zawo sizikukhumudwitsa abale ena, palibe chifukwa chodera nkhawa za malo amene anthu akukhala pa misonkhano.b

a Onani buku la “Khalanibe M’chikondi cha Mulungu,” tsamba 207 mpaka 209.

b Izi zikusintha zimene zinalembedwa mu Nsanja ya Olonda yachingelezi ya April 1, 1953, tsamba 223 ndiponso mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa May 2002, tsamba  4, ndime 12.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena