Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/02 tsamba 3-5
  • Kodi Kuchotsa Anthu Mumpingo Kumasonyeza Chikondi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kuchotsa Anthu Mumpingo Kumasonyeza Chikondi?
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 5/02 tsamba 3-5

Kodi Kuchotsa Anthu Mumpingo Kumasonyeza Chikondi?

1 Kodi n’chifukwa chiyani sitisintha pankhani imeneyi? Chifukwa chakuti Akristu ambiri oona amachirikiza Mulungu ndiponso malamulo ake olungama mokhulupirika. (1 Ates. 1:2-7; Aheb. 6:10) Komabe, nthaŵi zina, wina amachoka panjira ya choonadi. Ngakhale kuti akulu achikristu angamuthandize, iye angaswe malamulo a Mulungu mosalapa. Kapena angakane chikhulupiriro mwa kuphunzitsa chiphunzitso chabodza kapena angadzilekanitse ndi mpingo. Ndiyeno kodi tiyenera kuchitanji? Popeza zinthu zoterezi zinkachitikanso atumwi ali moyo, tiyeni tione zimene analemba pankhaniyi.

2 Pamene mwamuna wina ku Korinto anali kuchita zoipa mosalapa, Paulo anauza mpingo kuti: ‘Musayanjane naye, ngati munthu wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kudya naye wotere, iyayi.’ (1 Akor. 5:11-13) Anafunika kuchitanso zomwezi kwa anthu ampatuko, monga Humenayo. Anati: “Munthu wopatukira chikhulupiriro, utam’chenjeza kamodzi ndi kaŵiri, um’kanize, podziŵa kuti wotereyo wasandulika konse, nachimwa.” (Tito 3:10, 11; 1 Tim. 1:19, 20) Anafunikanso kupeŵa munthu aliyense wokana mpingo. Anati: “Anatuluka mwa ife, komatu sanali a ife; pakuti akadakhala a ife akadakhalabe ndi ife, koma kudatero kuti aonekere kuti sali onse a ife.”—1 Yoh. 2:18, 19.

3 Timayembekezera kuti woteroyo adzalapa kuti alandiridwenso. (Mac. 3:19) Nanga akachotsedwa, kodi n’koyenera kuti Akristu azicheza naye pang’ono, kapena asamacheze naye m’pang’ono pomwe? Ngati ndi choncho, chifukwa chiyani?

4 Kusiyiratu Kucheza Naye: Akristu amacheza ndi anthu ena. Mwa nthaŵi zonse, timacheza ndi anansi athu, anzathu akuntchito, anzathu akusukulu, ndi anthu ena, komanso timawalalikira ngakhale kuti ena ndi ‘adama, osirira, olanda, kapena opembedza mafano.’ Paulo analemba kuti sitingapeŵeretu anthu ameneŵa, ‘chifukwa bwenzi titatuluka m’dziko lapansi.’ Komabe, iye analangiza kuti ziyenera kusiyana ndi mmene tingachitire ndi “mbale” wamoyo wotere. Iye anati: ‘Musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale [wabwerera ku njira zoterozo], kungakhale kudya naye, iyayi.’—1 Akor. 5:9-11; Marko 2:13-17.

5 M’makalata amene mtumwi Yohane analemba, timapezamo malangizo ofanana ndi ameneŵa omwe amagogomezera momwe Akristu afunikira kupeŵera anthu ameneŵa. Amati: ‘Yense wakupitirira, wosakhala m’chiphunzitso cha Kristu, alibe Mulungu; . . . Munthu akadza kwa inu, wosatenga chiphunzitso ichi, musamulandire iye kunyumba, ndipo musamulankhule. Pakuti iye wakumulankhula ayanjana nazo ntchito zake zoipa.’ (2 Yoh. 9-11) Kodi izi zikutanthauza kuti, ngati pamsewu taona munthu wochotsedwa kapena amene anadzilekanitsa ndi mpingo kapena ngati takumana naye cha kumene timakhala, tizikhala ngati sitinamuone ndiponso tisam’patse “Moni,” kapena “Mwadzuka bwanji”? Inde, n’zimenedi zikutanthauza. Tisacheze naye m’pang’onong’ono pomwe kapena kulankhula naye, ngakhale atakhala kuti poyamba anali mnzathu kapena tinkacheza naye kwambiri.

6 Tikhulupirire kuti zimene Mulungu wakonza zoti Akristu asamacheze ndi munthu amene wachotsedwa chifukwa chochita tchimo osalapa zimatiteteza. “Tsukani chotupitsa chakale, kuti mukakhale mtanda watsopano, monga muli osatupa.” (1 Akor. 5:7) Kupeŵanso anthu amene adzilekanitsa mwadala, kumathandiza Akristu kupeŵa kusuliza, kusayamikira, ngakhalenso maganizo ampatuko.—Aheb. 12:15, 16.

7 Bwanji Ponena za Achibale?: Lamulo la Mulungu n’lakuti, woipa akachotsedwa, Akristu ‘asayanjane naye, ngakhale kudya naye wotere, iyayi.’ Chotero, sayenera kuyanjana, kuphatikizapo kucheza ndi anthu okhulupirika amene amalemekeza ndiponso amafuna kuyenda mogwirizana ndi malamulo a Mulungu. Ena angakhale achibale chapatali, osati a m’banja limodzi. Kungakhale kovuta kwa achibale ameneŵa kutsatira langizo la Mulungu limeneli, monganso momwe zinkavutira makolo achihebri kupha nawo mwana wawo woipa mu nthaŵi ya Chilamulo cha Mose. Komabe, lamulo la Mulungu n’lomveka bwino; choncho tikhulupirire kuti kuchotsa anthu mu mpingo ndi njira yoyenera.—1 Akor. 5:1, 6-8, 11; Tito 3:10, 11; 2 Yoh. 9-11; onani Nsanja ya Olonda ya Chingelezi ya September 15, 1981, masamba 26-31; Nsanja ya Olonda ya Chicheŵa ya April 15, 1988, masamba 28-31.

8 Munthu wochotsedwa kapena amene wadzilekanitsa angapitirizebe kukhala ndi mkazi wake wachikristu ndiponso ana ake okhulupirika. Kulemekeza ziweruzo za Mulungu ndiponso zimene mpingo wachita kudzapangitsa mkazi ndi anawo kuzindikira kuti zimene iye anachita, zinasintha ubale wauzimu womwe unali pakati pawo. Komabe, popeza kuti kuchotsedwa sikuthetsa ubale wawo kapena banja, angapitirize kukondana pabanjapo ndi kuchitira zinthu pamodzi.

9 Zimasiyana ngati wochotsedwayo kapena wodzilekanitsayo ali wachibale amene amakhala kwina. Zikhoza kutheka kusalankhulana naye m’pang’ono pomwe. Ngakhale kuti pangakhale nkhani zina za pachibale zofunika kukambirana naye, zimenezi zizichitika kamodzikamodzi, malinga ndi lamulo la Mulungu lakuti: ‘Musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira [kapena amene wachita tchimo linalake lalikulu], ngakhale kudya naye wotere, iyayi.’—1 Akor. 5:11.

10 Chilango Chimapindulitsa Anthu Ambiri: Inde, izi zingakhale zovuta chifukwa cha maganizo a munthu ndiponso chibale; komabe, zimenezi zimayesa kukhulupirika kwathu kwa Mulungu. Ndipo talingalirani phindu limene wolakwayo ndiponso anthu ena angapeze.

11 Mlongo wina dzina lake Lynette anathirira ndemanga pa zimene anasankha ‘zosiyiratu kucheza’ ndi mchemwali wake Margaret amene anali wochotsedwa. Iye limodzi ndi abale ake Achikristu ‘anali kukhulupirira kuti njira ya Yehova ndi yabwino kwambiri.’ Ndipo n’njabwinodi! Pambuyo pake Margaret anauza Lynette kuti: ‘Ukanakhala kuti unali kuona kuchotsedwa monga nkhani yamaseŵera, ndikudziŵa kuti sindikanachita zinthu zofunika kuti ndibwezeretsedwe mwamsanga monga mmene ndinachitira. Kusiyiratu kucheza ndi okondedwa anga ndiponso kuleka kucheza kwambiri ndi mpingo kunandilimbikitsa zedi kuti ndilape. Ndinazindikira kuopsa kwa choipa chimene ndinachita ndiponso kuopsa kolozetsa nkhongo Yehova.’ Inde, zikufananadi ndi zimene Paulo analemba, kuti: “Chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondweretsa, komatu choŵaŵa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloŵeretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.”—Aheb. 12:11.

12 Akulu amene akuimira mpingo pochotsa munthu wochimwa amene sakulapa, amamufotokozera kuti akhoza kulapa ndipo Mulungu angam’khululukire. Akhoza kumabwera pa misonkhano ku Nyumba ya Ufumu, kumene angamamve malangizo a m’Baibulo omwe angamuthandize kuti alape. Amauzidwanso momwe angasonyezere kuti walapa: (1) mu Nyumba ya Ufumu azikhala kumbuyo; (2) azifika misonkhano ikamayamba; (3) azichoka misonkhano ikangotha, ndiponso (4) asamalankhule ndi munthu aliyense pa Nyumba ya Ufumu.

13 Ngati munthu ndi wochotsedwa kapena anadzilekanitsa ndi mpingo, titsatire malangizo akuti: “Musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kukadya naye wotere, iyayi.” (1 Akor. 5:11) Koma malangizo a m’Baibulo ameneŵa sakukhudza mmene tiyenera kuonera abale athu achikristu amene akukhala ndi munthu wochotsedwa. Zimavuta kuti anthu okhulupirika a mumpingo akacheze kunyumba kwa anthu okhulupirika ameneŵa. Komabe, mosakayikira anthu a m’banjalo adzapitirizabe kupezeka pa misonkhano, choncho akulu oikidwa ayenera kuyesetsa kulimbikitsa anthu ameneŵa mwauzimu. (1 Ates. 5:14) Oŵeta gulu azigwiritsa ntchito mpata uliwonse kulimbikitsa mwauzimu anthu okondedwa ameneŵa, misonkhano yachikristu isanayambe kapena itatha. Akulu angapempherere anthu otereŵa kapena angapemphere nawo pamodzi.

14 Inde, Mulungu anakonza njira imene anthu ochotsedwa mu mpingo, ndiyeno alapa, angabwererere. Taona kuti ngakhale kuchotsedwa kwenikweniko ndi njira yachikondi imene tikufunika kuichirikiza. Koma n’zabwino kwambiri kupeŵa chinthu chomvetsa chisoni chimenechi mwa kutsatira nthaŵi zonse njira zolungama za Mulungu wathu woyera. Nthaŵi zonse tiziyamikira mwayi wotamanda Yehova monga mbali ya gulu lake loyera, lachikondi ndi loteteza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena