Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/02 tsamba 8
  • Lankhulanani!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Lankhulanani!
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova ndi Kristu Olankhula Opambana
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kulankhulana Muuminisitala Wachikristu
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kulankhulana m’Banja ndi Mumpingo
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kulankhulana Kwabwino—Kiyi ya Ukwati Wabwino
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 8/02 tsamba 8

Lankhulanani!

1 Kuti tichite ntchito yathu yolalikira ndi kupanga ophunzira, tiyenera kuuza anthu ena nkhani. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Kulankhulana kungakhale kovuta ngakhale kwa mabwenzi. Kodi n’chiyani chingatithandize kuuza anthu amene sitikuwadziŵa uthenga wabwino?

2 Khalani Bwenzi Lawo Osati Mlendo: Dziyerekezeni inu kukhala anthu amene mumakumana nawo mu utumiki. Malinga ndi momwe dziko lilili masiku ano, mpake kuti ena angakayikire anthu amene sawadziŵa ngakhale kuwaopa kumene. Izi zingalepheretse kulankhulana nawo. Kodi mungatani kuti anthu amene mumakumana nawo asachite nanu mantha? Njira ina imene timalankhulira ndi anthu ngakhale tisanatulutse mawu alionse ndiyo mwa maonekedwe athu abwino. Kuvala kwathu bwino ndiponso mwaulemu kumathandiza kuti asatiope kwambiri.—1 Tim. 2:9, 10.

3 Chinanso chimene chingathandize kulankhulana ndicho kukhala womasuka ndiponso wansangala. Izi zimathandiza anthu ena kumasuka nafe ndiponso zimawapangitsa kuti amvetsere. Kukonzekera bwino n’kofunika pambali imeneyi. Ngati tikudziŵa bwino zimene tikalankhule, timakhala odekha. Ndipo kudekha kumeneku kungakope ena kumvetsera uthenga wathu. Mayi wina ponena za Mboni ina imene inam’chezera anati: “Chimene ndimakumbukira pa nkhope yake yomwetulirayo n’chakuti anali wokhazikika maganizo. Ndinachita chidwi zedi.” Izi zinapangitsa kuti mayiyu amvetsere uthenga wabwino.

4 Makhalidwe Amene Amakopa Anthu: Tifunika kuwaganizira kwambiri anthu ena. (Afil. 2:4) Njira imodzi imene tingachitire zimenezi ndi yakuti tisamangolankhula ife tokha basi. Ndipotu, kulankhulana kumaphatikizapo kumvetsera. Tikapempha omvetsera athu kunena malingaliro awo ndiyeno n’kumvetsera mwachidwi ndemanga zawozo, amaona kuti tikuwaganizira. Choncho omvetsera anu akamalankhula, musawadule pakamwa kuti mupitirize ulaliki wanu umene mwakonzekera. Ayamikireni moona mtima, ndipo wonjezerani pa zimene anenazo. Ngati ndemanga zawo zikusonyeza chimene chimawadetsa nkhaŵa kwambiri, gwirizanitsani zimenezo ndi ulaliki wanu.

5 Kufatsa ndi kudzichepetsa kumathandiza kuti kulankhulana kuyende bwino. (Miy. 11:2; Mac. 20:19) Anthu ankakopeka ndi Yesu chifukwa anali “wofatsa ndi wodzichepetsa.” (Mat. 11:29) Mosiyana ndi zimenezi, mtima wodzikuza umainga anthu. Chotero, ngakhale kuti tili ndi chikhulupiriro chonse chakuti timadziŵa choonadi, timapeŵa mwanzeru kulankhula mwamakani.

6 Bwanji ngati zimene munthuyo wanena zisonyeza kuti zikhulupiriro zake n’zosiyana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa? Kodi tikufunika kumuwongolera? Inde, pang’onopang’ono. Koma tisachite zimenezi paulendo woyamba. Kaŵirikaŵiri ndi bwino kukambirana nkhani zimene zimakhudza tonse, tisanayambe kukambirana ziphunzitso za m’Baibulo zimene zingakhale zom’vuta kwambiri kuzimvetsa. Izi zimafunika kuleza mtima ndiponso luso. Paulo anapereka chitsanzo chabwino pambali imeneyi pamene anali kulalikira woweruza wa ku Areopagi.—Mac. 17:18, 22-31.

7 Koposa zonse, kuwakonda kwathu mopanda dyera kudzatithandiza kulankhula mogwira mtima. Monga Yesu, tiyenera kuwamvera chisoni anthu amene ali “okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.” (Mat. 9:36) Izi zimatilimbikitsa kuwauza uthenga wabwino ndiponso kuwathandiza kuyenda panjira yopita ku moyo. Uthenga wathu ndi wachikondi, choncho tiyeni tipitirize kuwauza anthu mwachikondi. Mwa kuchita zimenezi, timatsanzira Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu amene amadziŵa kulankhula bwino ndi anthu kuposa aliyense m’chilengedwe chonse.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena