Tinapindula Kwambiri ndi Msonkhano Wachigawo Wakuti “Olengeza Ufumu Achangu”
1 Unali Msonkhano Wolimbikitsa: Msonkhano wathu wachigawo wapitawo unalidi wosangalatsa kwambiri. Tinasonkhana ndi cholinga chimodzi, chakuti tikhale okonzeka mokwanira kulengeza Ufumu wa Mulungu mwachangu. Kodi mukukumbukira mmene wokamba nkhani yoyamba anatanthauzira mawu akuti “kulengeza”? Kodi mukukumbukira kuti n’kufufuza kotani kumene nkhani yakuti “Musaope Podziŵa kuti Yehova Ali Nafe” inatilimbikitsa kuti tizichita? Kodi pakalipano ndi nkhani za anthu ati zimene mwaziphunzira mwachifatse?
2 Nkhani yosiyirana yakuti “Chikhulupiriro Chathu Chimayesedwa ndi Mayesero Osiyanasiyana” inatchula zifukwa zazikulu zitatu zimene Yehova amalolera chizunzo. Kodi mungazitchule zifukwazo? Kodi ndi mfundo ziti za m’Malemba zimene zimasonyeza kuti monga Akristu sitiyenera kuloŵerera nawo m’zochitika zadziko? Kodi anatilimbikitsa kuchita chiyani pokonzekera mavuto amene tingapeze chifukwa chosaloŵerera m’zochitika zadziko? Kodi kupirira kwathu mayesero mokhulupirika kumalemekeza motani Yehova?
3 Kodi ndi mbali ziti za seŵero lakuti “Chirimikani m’Nthaŵi Zovuta” zimene zinakulimbikitsani kwambiri? Kodi tingafanane motani ndi Yeremiya?
4 Nkhani ya onse yakuti, “Maonekedwe a Dzikoli Akusintha,” inafotokoza zinthu ziti zimene zidzachitike n’kudzetsa tsiku loopsa la Mulungu? Pamene munkamvetsera nkhani yomaliza yakuti, “Chitani Zabwino Zochuluka Monga Olengeza Ufumu Achangu,” kodi zimene munamva munazigwirizanitsa motani ndi utumiki wanu?
5 Mfundo Zazikulu Zofunika Kuzigwiritsa Ntchito: Monga anafotokozera mu nkhani yakuti, “Khalani Oyamikira,” kodi tingasonyeze motani kuyamikira kwathu konse Yehova? Mu nkhani yaikulu yakuti, “Changu cha Olengeza Ufumu Chinakolezeka,” kodi tinalimbikitsidwa kutsanzira changu cha ndani? Kodi anati tidzipende m’mbali ziti?
6 Kodi nkhani yosiyirana yakuti “Ulosi wa Mika Umatilimbikitsa Kuti Tiyende M’dzina la Yehova” inatchula zinthu zitatu ziti zofunika zimene tiyenera kuchita kuti Yehova atiyanje? Kodi izi n’zotheka? (Mika 6:8) Malinga ndi nkhani yakuti “Khalanibe Oyera mwa Kutchinjiriza Mtima Wanu,” kodi tiyenera kukhala oyera m’mbali ziti? Kodi ndi mbali ziti zimene nkhani yakuti “Peŵani Chinyengo” inatichenjeza kuti tisanyengedwe ndiponso tisanyenge ena?
7 Ndi mfundo zabwino ziti za m’nkhani yosiyirana yakuti “Olengeza Ufumu Amene Amalemekeza Utumiki Wawo” zimene mwayamba kugwiritsa ntchito mu utumiki wanu? M’nkhani yakuti “Kukambirana Nkhani Zauzimu Kumalimbikitsa,” anapenda Afilipi 4:8. Kodi lembali likutithandiza bwanji kuti nkhani zathu zizikhala zokhudza kulambira, ndipo kodi tiyenera kuchita zimenezi liti ndi liti?
8 Nkhani yakuti, “Khulupirirani Yehova ndi Mtima Wonse Panthaŵi za Mavuto” inalongosola momwe tingapiririre masoka, mavuto azachuma, matenda, mavuto am’banja, ndiponso zophophonya zimene timazichita mobwerezabwereza. Kodi tingasonyeze motani kukhulupirira Yehova pamene tili m’mavuto ameneŵa?
9 Chuma Chatsopano Chauzimu: Tinasangalala kulandira buku labwino lakuti Yandikirani kwa Yehova. Kodi mbali zina zapadera za bukuli n’zotani? Kodi ndi mafanizo ati amene mwawakonda kwambiri? Kodi mmene mwaŵerenga bukuli mukuona kuti mwayandikira kwa Yehova? Kodi ndani amenenso angapindule ndi bukuli?
10 Msonkhano Wachigawo wakuti “Olengeza Ufumu Achangu” unatilimbikitsa mwauzimu ndipo n’zimene timafuna kuti tipirire m’nthaŵi zovuta zino. Kuti tipindule mokwanira ndi zinthu zauzimu zapadera zimenezi, tiyesetse kukumbukira zimene zinakambidwa, tiyamikire zimene tinalandira ndiponso tigwiritse ntchito zimene tinaphunzira. (2 Pet. 3:14) Kuchita zimenezi kudzatilimbikitsa kukhalabe okhulupirika ndiponso kukhala olengeza Ufumu achangu potsanzira Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti Yehova alemekezeke.—Afil. 1:9-11.