Ganizirani ndi Kukonda “Ana Amasiye”
1 Yehova ndi “Atate wa ana amasiye.” (Sal. 68:5) Tikuona m’lamulo limene anapereka ku mtundu wakale wa Israyeli kuti iye amaganizira za moyo wawo. Lamulolo limati: “Musazunza mkazi wamasiye, kapena mwana wamasiye aliyense. Ukawazunza ndi kakuti konse, nakandilirira pang’ono ponse iwowa, ndidzamvadi kulira kwawo.” (Eks. 22:22, 23) Chilamulo cha Mulungu chinalinso ndi njira zothandizira anthu ameneŵa kupeza zinthu zofunika pamoyo wawo. (Deut. 24:19-21) M’makonzedwe achikristu, olambira oona amalangizidwa ‘kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa zovuta zawo.’ (Yak. 1:27, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono) Kodi tingamutsanzire bwanji Yehova pankhani yoganizira ndi kukonda anthu amene ali m’mabanja a kholo limodzi kapena amene mnzawo wa muukwati ndi wa chipembedzo china?
2 Maphunziro Auzimu: Ngati ndinu kholo limene muli nokha kapena mnzanu wa muukwati si Mboni, kuchita phunziro la Baibulo lapanyumba mokhazikika ndi ana anu kungakhale kovuta. Koma phunziro la Baibulo lokhazikika ndi latanthauzo n’lofunika kuti ana akule bwino ndi kumachita zinthu mwanzeru. (Miy. 22:6) Kukambirana nawo nkhani zauzimu tsiku lililonse n’kofunikanso. (Deut. 6:6-9) Nthaŵi zina, mungataye mtima, koma musasiye. Pemphani Yehova kuti akupatseni mphamvu ndi kukutsogolerani ‘polera ana anu m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.’—Aef. 6:4.
3 Ngati mukufuna kuti ena akuthandizeni udindo wanu wa m’Malemba, dziŵitsani akulu zimenezo. Angakupatseni malangizo abwino kapena kukuthandizani kukhala ndi ndandanda yabwino yochitira zinthu zauzimu m’banja lanu.
4 Njira Zimene Ena Angathandizire: M’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, Timoteo anali mtumiki wa Yehova wachangu ngakhale kuti anakulira m’banja lomwe bambo ndi mayi ake anali osiyana zipembedzo. Mosakayikira kuyesetsa kwa mayi ake ndi agogo ake kumuphunzitsa malembo opatulika ali mwana, kunathandiza kwambiri. (Mac. 16:1, 2; 2 Tim. 1:5; 3:15) Komabe, anapindulanso ndi kucheza ndi Akristu ena monga mtumwi Paulo, amene amamuona Timoteo monga ‘mwana wake wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye.’—1 Akor. 4:17.
5 Chimodzimodzinso masiku ano, n’zothandiza kwambiri abale ndi alongo okhwima mwauzimu kuganizira ndi kukonda ana amasiye a mumpingo. Kodi mumawadziŵa mayina awo? Kodi mumalankhula nawo pamisonkhano yachikristu ndiponso nthaŵi zina? Apempheni kuyenda nanu mu utumiki wakumunda. Mwinanso nthaŵi zina mungaŵaitane pamodzi ndi kholo lawo, limene mwina lilibe mnzake wa muukwati kapena mnzake wa mu ukwatiyo si Mboni, kukhala nawo paphunziro lanu la banja kapena pamene mwakonza zokasangalala. Ana ameneŵa akamakuonani monga bwenzi lawo, mwachionekere adzatengera chitsanzo chanu ndiponso adzamvera malangizo anu.—Afil. 2:4.
6 Yehova amaganizira kwambiri ana amasiye, ndipo akudalitsa kuyesetsa kwathu kuwathandiza kuti achitenge choonadi kukhala chawochawo. Ana ambiri okulira m’mabanja a kholo limodzi kapena m’banja lomwe bambo ndi mayi ndi osiyana zipembedzo anathandizidwa mwanjira imeneyi ndipo panopo akutumikira mokhulupirika monga apainiya, atumiki otumikira, akulu, oyang’anira oyendayenda, amishonale, kapena m’banja la Beteli. Tiyeni tonse tifufuze njira ‘zokulitsira’ kukonda kwathu ana amasiye, potsatira Atate wathu wa Kumwamba.—2 Akor. 6:11-13.