Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Popeza kuti Baibulo kaŵirikaŵiri limatchula “mnyamata wopanda atate,” kodi zimenezi zimasonyeza chisamaliro chochepa pa atsikana?
Ndithudi ayi.
New World Translation of the Holy Scriptures imagwiritsira ntchito mawu akuti “mnyamata wopanda atate” m’mavesi ambiri amene amasonyeza chisamaliro cha Mulungu pa ana amene alibe kholo. Mulungu anamveketsa bwino lomwe chisamaliro chake m’malamulo amene anapereka kwa Israyeli.
Mwachitsanzo, Mulungu anati: “Musazunza mkazi wamasiye, kapena [mnyamata wopanda atate, NW] aliyense. Ukawazunza ndi kakuti konse, nakandilirira pang’ono ponse iwowa, ndidzamvadi kulira kwawo; ndi mkwiyo wanga udzayaka, ndipo ndidzapha inu ndi lupanga; ndipo akazi anu adzakhala amasiye, ndi ana anu omwe [anyamata opanda atate, NW].” (Eksodo 22:22-24) “Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wa milungu, ndi Mbuye wa ambuye; Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi wowopsa, wosasamalira nkhope za anthu, kapena kulandira chokometsera mlandu. Aweruzira [mnyamata wopanda atate] ndi mkazi wamasiye.”—Deuteronomo 10:17, 18; 14:29; 24:17; 27:19.
Matembenuzidwe ambiri a Baibulo amanena kuti “mwana wopanda atate” kapena “mwana wamasiye” m’mavesi ameneŵa, motero kuphatikiza anyamata ndi atsikana omwe. Komabe, mamasulidwe otero amanyalanyaza mkhalidwe wa liwu lake Lachihebri (ya·thohmʹ), limene lili mumkhalidwe wachimuna. Mmalomwake, New World Translation of the Holy Scriptures imagwiritsira ntchito mamasulidwe olondola akuti “mnyamata (anyamata) wopanda atate,” monga pa Salmo 68:5, pamene pamati: “Atate wa anyamata opanda atate ndi woweruza wa akazi amasiye ndiye Mulungu m’malo ake oyera.” Mozikidwa pa kuzindikiridwa kumodzimodziko kwa magwero ake a Chihebri, mkhalidwe wachikazi wa verebu pa Salmo 68:11 umafuna kulemba kuti: “Akazi akulalikira uthengawo ndiwo khamu lalikulu.”a
Ngakhale kuti mawuwo “mnyamata wopanda atate” ndiwo mamasulidwe aakulu a ya·thohmʹ, zimenezi siziyenera kuonedwa kukhala zikusonyeza kusoŵeka kwa chisamaliro pa atsikana amene alibe kholo. Ndime zogwidwa mawuzo ndi zina zimasonyeza kuti anthu a Mulungu analimbikitsidwa kusamalira akazi, akazi amasiye. (Salmo 146:9; Yesaya 1:17; Yeremiya 22:3; Zekariya 7:9, 10; Malaki 3:5) M’Chilamulo, Mulungu anaphatikizamonso nkhani yonena za chigamulo cha mlandu chimene chinatsimikiziritsa choloŵa cha ana aakazi opanda atate wawo a Tselofekadi. Chigamulo chimenecho chinakhala lamulo losamalirira milandu yofanana ndi umenewo, motero chikumachirikiza zoyenera za atsikana opanda atate.—Numeri 27:1-8.
Yesu sanasonyeze tsankho kwa ana aamuna kapena aakazi posonyeza kukoma mtima kwa iwo. Mmalomwake, timaŵerenga kuti: “Analinkudza nato kwa iye tiana, kuti akatikhudze; ndipo ophunzirawo anawadzudzula. Koma pamene Yesu anaona anakwiya, ndipo anati kwa iwo, Lolani tiana tidze kwa ine; musatiletse: pakuti ufumu wa Mulungu uli wa totere. Ndithu ndinena ndi inu, Munthu aliyense wosalandira ufumu wa Mulungu ngati kamwana, sadzaloŵamo konse. Ndipo iye anatiyangata, natidalitsa, ndi kuika manja ake pa ito.”—Marko 10:13-16.
Liwu Lachigiriki lotembenuzidwa “tiana” lili mumkhalidwe wosasonyeza umuna kapena ukazi. Dikishonale ina Yachigiriki yotchuka imanena kuti liwuli “limagwira ntchito kwa anyamata ndi atsikana.” Yesu anali kusonyeza chikondwerero cholingana ndi cha Yehova mwa ana onse, anyamata ndi atsikana. (Ahebri 1:3; yerekezerani ndi Deuteronomo 16:14; Marko 5:35, 38-42.) Chotero tiyenera kuzindikira kuti uphungu wa m’Malemba Achihebri wonena za kusamalira “anyamata opanda atate” ndiuphungu wonenanso za mmene tiyenera kusamalira ana onse amene alibe kholo kapena makolo.
[Mawu a M’munsi]
a Tanakh Yachiyuda imati: “AMBUYE apereka lamulo; akazi amene abweretsa mbiri yabwino ali khamu lalikulu.”