Mabanja Opanda Bambo—Chizindikiro cha Nthaŵi
KODI mungati vuto lalikulu kwambiri la kakhalidwe ka anthu lero n’liti? Pafupifupi anthu 80 mwa anthu 100 amene anafunsidwa pa kafukufuku wochitidwa ndi Gallup ku United States akukhulupirira kuti ndi “kusapezeka kwa bambo panyumba.” Malingana ndi zimene ananena Gallup, ana opitirira 27 miliyoni ku United States sakhala ndi abambo awo owabereka, ndipo chiŵerengero chimenecho chikuwonjezeka mofulumira kwambiri. Lipoti la bungwe la United Nations Children’s Fund linanena kuti pafupifupi ana 50 mwa ana 100 achizungu ku United States amene abadwa kuyambira mu 1980 “adzakhala m’mabanja a kholo limodzi m’gawo lina la ubwana wawo. Kwa ana achikuda chiŵerengero chake ndi 80.” Motero magazini yotchedwa USA Today inati dziko la United States ndilo “lotsogolera pa mabanja opanda abambo padziko lonse.”
Komabe, nkhani ya m’magazini otchedwa Atlantic Monthly inati: “Kukwera kwa kusweka kwa mabanja sikukuchitika pakati pa anthu a ku America okha. Kukuchitika pafupifupi m’mayiko onse otukuka, kuphatikizapo dziko la Japan.” Ndipo pakuti kupeza ziŵerengero n’kovuta, zikuoneka kuti mayiko ambiri amene akungotukuka akupezanso vutoli. Malingana ndi magazini yotchedwa World Watch, “amuna a m’mayiko osauka nthaŵi zambiri amasiya akazi ndi ana awo chifukwa cha kuchuluka kwa mavuto a zachuma.” N’zoonadi, kafukufuku amene anachitidwa m’dziko lina ku Carribean anavumbula kuti ndi abambo 22 okha mwa abambo 100 a ana a zaka zisanu ndi zitatu amene ankakhala ndi ana awo.
Ana opanda bambo anali ponseponse ngakhale m’nthaŵi za Baibulo. (Deuteronomo 27:19; Salmo 94:6) Komabe, panthaŵiyo, chifukwa chachikulu chimene ana ankakhalira amasiye chinali imfa ya bambo. David Blankenhorn, akuti: “Lero chifukwa chachikulu kwambiri cha kukhala opanda bambo ndicho kufuna kwa bamboyo.” N’zoonadi, monga mmene tikuonera, kukwera kwa chiŵerengero cha ana opanda bambo kukupereka umboni wosonyeza kuti anthu ambiri lero alibe “chikondi chachibadwidwe.” Malingana ndi zimene Baibulo linanena, uwu ndi umboni wina wosonyeza kuti tikukhala “m’masiku otsiriza.”—2 Timoteo 3:1-3.
Komabe kwa ana aang’ono, kusoŵa kwa bambo m’moyo wawo kumakhala tsoka lawo. Kumayambitsa zoŵaŵa zosatha zimene zingakhale ndi zotsatira zosatha msanga. Motero, m’nkhani zotsatirazi, tikambirana za zoŵaŵa zosatha zimenezi, osati n’cholinga chofooketsa oŵerenga, koma chopereka chidziŵitso chimene chingathandize mabanja kuthetsa vuto lowonongali.