Ntchito Yomanga Nyumba za Ufumu Padziko Lonse M’mayiko Ena a ku Ulaya
1 Zaka makumi angapo zapitazi ntchito ya Mboni za Yehova m’mayiko angapo a ku Ulaya, kuphatikizapo kum’maŵa kwa Ulaya, inali yoletsedwa. Nthaŵi zambiri, chiletsochi ankachikhwimitsa kwambiri. Kunali kovuta kuchita misonkhano poyera, ndipo kukhala ndi Nyumba ya Ufumu yochitiramo misonkhano tingoti kunali kosatheka. Koma m’zaka zaposachedwapa, “Yehova anatichitira ife zazikulu; potero tikhala okondwera.”—Sal. 126:3.
2 Kuyambira mu 1983, kupondereza Mboni za Yehova kunayamba kuchepako. Pofika mu 1989, Mboni za Yehova zinavomerezedwa ndi boma ku Poland ndi ku Hungary. Mu 1991, Mboni za Yehova ku Russia zinaloledwa kulembetsa ku boma. Kuyambira pamenepo, ntchito ya Mboni za Yehova yapita patsogolo ku Russia ndi ku mayiko amene ankapanga dziko la Soviet Union. Kuyambira mu March 1996 mpaka mu October 1998, Bungwe Lolamulira linavomereza ndalama zomangira Nyumba za Ufumu 359 zimene nthambi zoyang’anira mayiko 11 a ku Ulaya zinapempha.
3 Mukamaona zithunzi zimene zili mu mphatika ino, ganizirani za zinthu zazikulu ndi zodabwitsa zimene Yehova wachitira anthu ake. (Sal. 136:4) Musangalala kudziŵa kuti zopereka za abale athu padziko lonse zikugwiritsiridwa ntchito bwino kwambiri, mogwirizana ndi zimene Yesu ananena pa Yohane 13:35 kuti: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.”
4 Dziko limodzi la ku Ulaya limene likupindula ndi njira yothandiza kuti m’mayiko osauka mumangidwe Nyumba za Ufumu ndi dziko la Romania, kumene Nyumba za Ufumu 36 zamangidwa kuyambira mu July 2000. Pogwiritsira ntchito pulani yofanana pomanga pafupifupi Nyumba za Ufumu zonse, m’dziko la Ukraine anamanga Nyumba za Ufumu 61 mu 2001 ndipo m’chaka cha 2002 anamanga zinanso 76. Pogwiritsira ntchito ndalama zimene zinasonkhedwa ku Thumba la Nyumba za Ufumu, ku Bulgaria, Croatia, Macedonia, Moldova, Russia, ndi Serbia ndi Montenegro kwamangidwa Nyumba za Ufumu mazana ambiri.
5 M’mayiko ena kumanga Nyumba za Ufumu kwakhala kovuta kwambiri, ndipo pamakhala zambiri zofunika kuchita ntchito yomangayo isanayambe. Nthaŵi zambiri zimenezi zimatenga nthaŵi yaitali. Komanso, pamafunika ndalama zambiri zomangira Nyumba ya Ufumu ku dera limeneli la Ulaya poyerekezera ndi madera ambiri a ku Africa kuno kapena ku South America. Koma chifukwa chakuti anthu olambira Yehova akuwonjezeka kwambiri, Nyumba za Ufumu mazana ambiri zikufunikabe m’mayiko osauka a ku Ulaya!
6 N’zosangalatsa kwambiri kuona ntchito yomanga Nyumba za Ufumu imeneyi ikuwonjezeka kwambiri chonchi! M’madera amene mwamangidwa Nyumba za Ufumuzi, umboni wabwino kwambiri waperekedwa, malinga ndi mmene zochitika zambiri zikusonyezera. M’madera ena, akuluakulu a boma amachita chidwi kwambiri poona kuti timagwirizana nawo potsatira malangizo awo omangira nyumba.
7 Yesaya molondola analosera za kuonjezeka kwa olambira oona m’nthaŵi yathu ino. Kudzera mwa m’neneriyu, Mulungu ananeneratu kuti: “Ine Yehova ndidzafulumiza ichi m’nthaŵi yake.” (Yes. 60:22) Mosakayikira, zaka khumi zapitazi zaonetsa kuti inali nthaŵi ya Yehova yoti ntchitoyi iwonjezeke kum’maŵa kwa Ulaya komanso ndi m’mayiko ena ambiri kuphatikizapo Malawi. Yehova apitirizebe kudalitsa zimene tikuyesetsa kuchita kuti ntchitoyi ifulumire m’Malawi muno mwa kuthandiza ndi ndalama zathu ndiponso m’njira zina zimene tingathe. Zimenezi zithandiza kuti kulambira koyera kupite patsogolo m’Malawi muno, ndipo zithandizanso kuti umboni waukulu uperekedwe ku “malekezero a dziko.”—Mac. 13:47.
[Zithunzi patsamba 3]
Nyumba ya Ufumu ku Moscow, Russia
[Zithunzi pamasamba 4-6]
Nyumba za Ufumu zatsopano kum’maŵa kwa Ulaya
Strumica, ku Macedonia
Daruvar, ku Croatia
Bitola, ku Macedonia
Sokal m’chigawo cha Lviv, ku Ukraine
Mladost, ku Bulgaria
Kransnooktyabrskiy, m’dera la Maykop, ku Russia
Bački Petrovac, ku Serbia ndi Montenegro
Plovdiv, ku Bulgaria
Tlumach, m’chigawo cha Ivano-Frankivsk, ku Ukraine
Rava-Ruska, m’chigawo cha Lviv, ku Ukraine
Stara Pazova, ku Serbia ndi Montenegro
Zenica, ku Bosnia ndi Herzegovina
Sokal, m’chigawo cha Lviv, ku Ukraine
Zhydachivl, m’chigawo cha Lviv, ku Ukraine