Lemekezani Yehova mwa Kulalikira Mwamwayi
1 Atumiki okhulupirika a Yehova amafunafuna mipata yomulemekezera tsiku ndi tsiku. (Sal. 96:2, 3; Aheb. 13:15) Njira imodzi imene tingamulemekezere ndi mwa kulalikira mwamwayi. Olambira Yehova ambiri masiku ano amayamikira kuti winawake anawafotokozera uthenga wa Ufumu powalalikira mwamwayi.
2 Kulalikira mwamwayi kwa munthu mmodzi nthaŵi zambiri kumathandiza kuti ena amve uthenga wa Ufumu. Mwachitsanzo, zimene Yesu anakambirana ndi mkazi wachisamariya pa chitsime cha Yakobo zinachititsa kuti anthu ambiri achite chidwi ndi uthenga wabwino. (Yoh. 4:6-30, 39-42) Pamene Paulo ndi Sila anali m’ndende ku Filipi, analalikira kwa mdindo wandendeyo, ndipo banja lonse la mwamunayo linakhulupirira choonadi.—Mac. 16:25-34.
3 Mipata Yolalikira: Kodi muli ndi mipata yotani yolalikira mwamwayi? Ena amalalikira pamene akugula zinthu, akakwera basi kapena minibasi, kapena akakhala pamzera kuchipatala. Ena amatha kulalikira panthaŵi yopuma kuntchito kapena kusukulu. Kungokhala ndi chimodzi mwa zofalitsa zathu zofotokoza Baibulo poonekera kungachititse ena kutifunsa zimene timakhulupirira.—1 Pet. 3:15.
4 Mmene Mungayambire: Kamtsikana kamanyazi ka zaka zisanu ndi ziŵiri kanamva pa msonkhano kuti n’kofunika kwambiri kuti onse azilalikira. Choncho, kakupita kokagula zinthu ndi mayi ake, kanaika mabulosha aŵiri m’chikwama chake. Pamene mayi ake anali kulipira ndalama, kamtsikana kaja kanagaŵira bulosha kwa mkazi wina amene analilandira mosangalala. Atakafunsa chimene chinakalimbitsa mtima kuti kathe kulalikira kwa mkaziyo, kamtsikana kamanyazika kanayankha kuti: “Ndinangoti, Wani, Thu, Fili, Yamba! N’kuyamba!”
5 Kuti tilalikire mwamwayi, tonsefe tikufunika kukhala ndi mtima ngati wa kamtsikana kameneka. Kodi n’chiyani chingatithandize? Pempherani kuti mulimbe mtima kuti mulankhule. (1 Ates. 2:2) Konzekerani funso kapena ndemanga pa nkhani yochititsa chidwi imene ingakuthandizeni kuyamba kukambirana ndi ena. Ndiyeno khulupirirani kuti Yehova adzadalitsa khama lanu.—Luka 12:11, 12.
6 Kulalikira mwamwayi kwa anthu amene timakumana nawo tsiku ndi tsiku kumachititsa kuti Yehova alemekezeke ndiponso kumatipatsa chimwemwe. Kungathandize wina kupeza njira ya kumoyo wosatha.