Khalani Akhama ‘Pochitira Umboni Mokwanira’
1, 2. N’chiyani chikukuchititsani chidwi ndi mmene Paulo anaonera ntchito yolalikira uthenga wabwino, ndipo kodi tingatsatire bwanji chitsanzo chake ‘chochitira umboni mokwanira’?
1 Monga Yesu ndi atumiki ena ambiri okhulupirika akale, mtumwi Paulo anali mlaliki wachangu wa uthenga wabwino, ‘anachitira umboni [mokwanira, NW]’ zivute zitani. Ngakhale ali pa ukaidi wosachoka panyumba, anali ‘kulandira onse akufika kwa iye, ndi kulalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuphunzitsa za Ambuye Yesu Kristu ndi kulimbika konse.’—Mac. 28:16-31.
2 Ifenso tingakhale akhama nthaŵi zonse ‘pochitira umboni mokwanira.’ Izi zikuphatikizapo kulalikira anthu amene takumana nawo popita ndi pobwera ku Msonkhano Wachigawo wakuti “Patsani Mulungu Ulemerero” ndiponso pamene tili pa malo a msonkhanowo.—Mac. 28:23; Sal. 145:10-13.
3. Kodi tingatani kuti ulaliki wathu wamwamwayi usakhale chinthu chochitika mwadzidzidzi?
3 Kodi Ulaliki Wamwamwayi N’chiyani? Ulaliki wamwamwayi sumangochitika mwadzidzidzi kapena popanda cholinga, ngati kuti ndi wosakonzekera kapena ndi wosafunika kwenikweni. Utumiki wathu suli wotero. Monga anachitira Paulo, kupatsa Mulungu ulemerero mwa kulalikira n’kofunika kwambiri kwa ife, ndipo chizikhala cholinga chathu kulalikira paliponse poyenera pamene tikuyenda maulendo athu m’miyezi ikubwerayi. Komabe, kalalikidwe aka tingakafotokoze moyenera kuti ndi ulaliki wamwamwayi, kutanthauza kuti timachita zimenezi momasuka, mwaubwenzi ndiponso mwachibadwa. Kalalikidwe kameneka kangakhale ndi zotsatira zabwino.
4. N’chiyani chinathandiza Paulo kulalikira kunyumba kwake?
4 Konzekerani Kulalikira: Paulo ali pa ukaidi wosachoka panyumba ku Roma anapeza njira zolalikirira. Ali kunyumba kwake, anachitapo kanthu pomaitanira kunyumba kwakeko atsogoleri achiyuda akumeneko. (Mac. 28:17) Ngakhale kuti ku Roma kunali mpingo wachikristu, Paulo anadziŵa kuti anthu achiyuda mu mzinda umenewo anali kudziŵa zochepa za chikhulupiriro cha Akristu. (Mac. 28:22; Aroma 1:7) Sanaleke ‘kuchitira umboni mokwanira’ za Yesu Kristu ndi Ufumu wa Mulungu.
5, 6. Kodi ndi pati pamene tingalalikire mwamwayi, ndipo tingakonzekere bwanji kuti tichite zimenezo mogwira mtima?
5 Ganizirani za anthu onse amene mungakumane nawo paulendo wanu amene amangodziŵa zochepa za Mboni za Yehova. Zingatheke kuti sadziŵanso kuti timachititsa maphunziro a Baibulo apanyumba aulere. Khalani tcheru kuti mupeze mpata wolalikira kwa anthu amene mwakumana nawo paulendo, pogula zinthu, pakudya ku resitilanti, poyenda pa zoyendera za anthu onse, ndi zina zotero. Konzekerani zimene munganene kuti muyambe kukambirana ndi kulalikira mwachidule. Mwina masiku akadalipo mungayesere kulalikira mwamwayi kwa anthu amene mwayandikana nawo, achibale anu, anzanu akuntchito, ndi odziŵana nawo ena.
6 Mudzafunika zofalitsa zoti mugwiritse ntchito polalikira mwamwayi. Monga ziti? Mungagwiritse ntchito thirakiti lakuti Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo? Fotokozani ndime zisanu zoyambazo, zimene zikulongosola zifukwa zosiyanasiyana zoŵerengera Baibulo. Asonyezeni kabokosi kali kumbuyo kwa thirakitilo kopemphera phunziro la Baibulo lapanyumba laulere. Mukapeza munthu womvetsera, gaŵirani bulosha la Mulungu Amafunanji. Ngati mukuyenda pa galimoto, mutha kuwatengeranso anthu amene angachitedi chidwi ndi uthenga wa Ufumu zofalitsa zina zimene zimafotokoza nkhani zazikulu za m’Baibulo.
7, 8. Kodi tiyenera kumvera langizo liti lokhudza maonekedwe athu ndi khalidwe lathu popita ndi pochokera ku msonkhano ndiponso mapulogalamu a tsiku lililonse akatha?
7 Ganizirani Maonekedwe Anu ndi Khalidwe Lanu: Tiyenera kuonetsetsa kuti khalidwe lathu komanso mavalidwe ndi kudzikongoletsa kwathu kusapatse anthu ena maganizo olakwika kapena ‘kulinena’ gulu la Yehova. (Mac. 28:22) Zimenezi tifunika kuchita pamsonkhano, popita ndi pochokera kumsonkhano ndiponso mapulogalamu a tsiku lililonse akatha. Nsanja ya Olonda ya August 1, 2002, tsamba 18, pandime 14, inatilangiza kuti: “Kaonekedwe kathu sikayenera kukhala kosadziletsa, kuvala masitayelo osayenera, kuvala modzutsa chilakolako cha kugonana, zovala zoonetsa m’kati, kapena zosonyeza kutengeka kwambiri ndi mafashoni. Ndiponso, tiyenera kuvala mosonyeza kuti ‘timalemekeza Mulungu.’ Kodi zimenezi sizikutichititsa kuiganizira bwino nkhaniyi? Imeneyi si nkhani yongovala moyenerera popita ku misonkhano ya mpingo [kapena pa msonkhano wachigawo] ndiyeno n’kutayirira ngati si nthaŵi ya misonkhano. Kaonekedwe kathu nthaŵi zonse kayenera kusonyeza ulemu chifukwa ndife Akristu ndiponso atumiki tsiku lonse lathunthu.”—1 Tim. 2:9, 10.
8 Tiyenera kuvala bwino ndiponso mopatsa ulemu. Ngati nthaŵi zonse maonekedwe athu ndi khalidwe lathu zisonyeza kuti timakhulupirira Mulungu, sitidzasiya kulalikira mwamwayi chifukwa chakuti sitikuoneka bwino.—1 Pet. 3:15.
9. Kodi zinthu zinamuyendera bwanji Paulo polalikira ku Roma?
9 Ulaliki Wamwamwayi Umabala Zipatso: Zaka ziŵiri zimene Paulo anali pa ukaidi wosachoka panyumba ku Roma, anaona zotsatira zabwino chifukwa choyesetsa kulalikira. Luka anati “ena anamvera zonenedwazo.” (Mac. 28:24) Paulo mwiniyo anasonyeza kuti ‘kuchitira kwake umboni mokwanira’ kunali kogwira mtima pamene analemba kuti: “Zija za kwa ine zidachita makamaka kuthandizira Uthenga Wabwino; kotero kuti zomangira zanga zinaonekera mwa Kristu m’bwalo lonse la alonda, ndi kwa onse ena; ndi kuti unyinji wa abale mwa Ambuye, pokhulupirira m’zomangira zanga, alimbika mtima koposa kulankhula mawu a Mulungu opanda mantha.”—Afil. 1:12-14.
10. Kodi banja lina chaka chatha zinthu zinawayendera bwanji polalikira?
10 Chaka chathachi, banja lina litakhala tsiku lonse pa msonkhano wachigawo, linali ndi chokumana nacho chosangalatsa kwambiri polalikira mwamwayi kwa mkazi amene anafunsa za mabaji awo a msonkhano. Anamuuza za msonkhano ndiponso zimene Baibulo limanena kuti anthu ayenera kuyembekezera kuti zichitika m’tsogolomu. Anamupatsa thirakiti lakuti Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo? ndipo anafotokoza za phunziro la Baibulo la panyumba laulere. Mkaziyo anati wakonda kuti wina adzamuyendere, analemba dzina lake ndi adiresi kumbuyo kwa thirakitilo, ndipo anapempha banjalo kuti likonze zoti adzayenderedwe. Kodi zinthu zingakuyendereni bwanji chaka chino chifukwa chochita khama ‘pochitira umboni mokwanira’?
11. Kodi tiyenera kuchita zotani kuti tipititse patsogolo uthenga wabwino chaka chino ‘pochitira umboni mokwanira’?
11 Pititsani Patsogolo Mokwanira Uthenga Wabwino: Tangoganizirani momwe Paulo anasangalalira atamva kuti Akristu anzake anali kutengera changu chake. Tiyenitu tichite khama ndipo titsimikize mtima kupititsa patsogolo uthenga wabwino mwa kulalikira mwamwayi chikhulupiriro chathu cha m’Baibulo komanso pamene tikupindula ndi msonkhano wachigawo wa chaka chino.
[Bokosi patsamba 3]
Zofalitsa Zofunika Polalikira Mwamwayi
■ Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo? (thirakiti)
■ Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? (bulosha)
■ Zofalitsa zina zofunika
[Bokosi patsamba 4]
Musawaiwale!
Ndani? Anthu onse achidwi amene anapezeka pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu kapena pankhani yapadera. Kodi tawapempha kuti adzapezeke pa msonkhano wachigawo wa chaka chinowu? Mwachionekere ambiri mwa iwo, atalimbikitsidwa mokoma mtima, angadzapezekepo. Mayanjano abwino a pamsonkhano ndiponso pulogalamu yolimbikitsa mwauzimu imeneyo, idzawalimbikitsa kuyandikira kwa Yehova ndi gulu lake. Bwanji osawaitanira ndi kuona kuti ati bwanji? Adziŵitseni zonse zimene akufunika kudziŵa, monga masiku a msonkhano, mayendedwe ake kuti akafike ku malo a msonkhano, ndiponso nthaŵi yoyambira chigawo chilichonse ndi yothera yomwe.