Ntchito Imene Imatsitsimula
1 Uthenga wa m’Baibulo umatsitsimula anthu onse amene amaulandira ndi kuugwiritsa ntchito pa moyo wawo. (Sal. 19:7, 8) Umawathandiza kumasuka ku ziphunzitso zonyenga ndi kusiya makhalidwe oika moyo pachiswe ndiponso umawapatsa chiyembekezo chodalirika cha m’tsogolo. Komabe, amene amapindula si anthu amene amalandira uthenga wabwino okhawo ayi. Anthu amene amauza ena choonadi chotsitsimula cha m’Baibulo nawonso amatsitsimulidwa.—Miy. 11:25.
2 Kupeza Mphamvu Chifukwa cha Utumiki: Yesu ananena kuti amene amasenza goli lokhala wophunzira wa Kristu, limene limaphatikizapo ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira, ‘adzapeza mpumulo wa miyoyo yawo.’ (Mat. 11:29) Iyenso payekha anaona kuti kulalikira kwa ena kunam’patsa mphamvu. Kwa iye, ntchito imeneyi inali ngati chakudya. (Yoh. 4:34) Pamene Yesu anatumiza ophunzira 70 kuti akalalikire, ophunzirawo anasangalala ataona kuti Yehova wadalitsa khama lawo.—Luka 10:17.
3 Mofananamo, Akristu ambiri masiku ano amapezanso mphamvu akamagwira nawo ntchito yolalikira. Mlongo wina anati: “Utumiki ndi wotsitsimula chifukwa umandithandiza kukhala ndi cholinga pa moyo. Mavuto anga ndi nkhaŵa za tsiku ndi tsiku zimachepa ndikamalalikira.” Mtumiki wina wachangu anati: “Utumiki . . . umandichititsa kuti ndizimuona Yehova kukhala weniweni tsiku ndi tsiku ndipo umandithandiza kukhala ndi mtendere komanso chimwemwe cha mumtima chimene sichingapezeke m’njira ina iliyonse.” Tili ndi mwayi waukulu wokhala “antchito anzake a Mulungu.”—1 Akor. 3:9.
4 Goli la Kristu N’lofeŵa: Ngakhale kuti Akristu akulimbikitsidwa ‘kuyesetsa [“mwakhama,” NW],’ Yesu sakufuna kuti tichite zinthu zimene sitingathe. (Luka 13:24) Ndipotu, amatipempha mwachikondi ‘kusenza goli lake.’ (Mat. 11:29) Amene akukumana ndi mavuto pamoyo wawo angakhulupirire kuti utumiki wawo umene amachita ndi mtima wonse, ngakhale kuti ndi wochepa, umasangalatsa Mulungu.—Marko 14:6-8; Akol. 3:23.
5 N’zotsitsimula kwambiri kutumikira Mulungu amene amayamikira zilizonse zimene timachita chifukwa cha dzina lake. (Aheb. 6:10) Tiyenitu tiyesetse kum’patsa zonse zimene tingathe.