Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/08 tsamba 1
  • “Senzani Goli Langa”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Senzani Goli Langa”
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Kupeza Mpumulo wa Miyoyo Yanu’
    Nsanja ya Olonda—1989
  • “Goli Langa Lili Lofeŵa, ndi Katundu Wanga Ali Wopepuka”
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Yesu Ankatsitsimula Ena
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • “Bwerani kwa Ine . . . Ndipo Ndidzakutsitsimutsani”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
km 5/08 tsamba 1

“Senzani Goli Langa”

1 Ngakhale kuti tikukhala m’dziko lamavuto limene anthu ambiri ali ndi nkhawa, ifeyo tapeza mpumulo chifukwa cholabadira pempho la Yesu lakuti tisenze goli lake lotsitsimutsa. (Mat. 11:29, 30) Kusenza goli mwa kukhala wophunzira wa Yesu kumaphatikizapo kugwira ntchito yovuta koma yotsitsimula. Ntchitoyi ndi yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndi kuthandiza anthu ena kuti nawonso apeze chitsitsimutso posenza goli lofewa la Yesu.—Mat. 24:14; 28:19, 20.

2 Utumiki Umatitsitsimula: Yesu sanapemphe otsatira ake kuwonjezera katundu wake pa katundu wawo. Koma iye anawapempha kusinthanitsa katundu wawo wolemerayo ndi katundu wake wopepuka. Ifeyo tili ndi chiyembekezo ndipo sitilemedwa ndi nkhawa za dongosolo lino la zinthu. Komanso sitilimbana ndi kufunafuna chuma chosadalirika. (Luka 21:34; 1 Tim. 6:17) N’zoona kuti timatanganidwa ndiponso timagwira ntchito kuti tipeze zofunika pamoyo, komabe kulambira Mulungu timakuika patsogolo. (Mat. 6:33) Ngati timaona kuti utumiki ndi wofunika kwambiri, utumikiwo umakhala wotsitsimutsa osati wotopetsa.—Afil. 1:10.

3 Mwachibadwa, timalankhula za zinthu zimene timazikonda kwambiri. (Luka 6:45) Akhristu onse amakonda kwambiri Yehova komanso madalitso a Ufumu amene iye walonjeza. N’chifukwa chake tikakhala mu utumiki timatsitsimulidwa kwambiri tikamalankhula za “uthenga wabwino wa zinthu zabwino,” n’kuiwala za mavuto athu. (Aroma 10:15) Pajatu tikamachita chinthu mobwerezabwereza luso lathu limakula, ndipo zimenezi zimawonjezera chimwemwe chathu. Motero tiyenera kumathera nthawi yochuluka muutumiki ngati tingakwanitse, ndipo tikamatero tidzatsitsimulidwa kwambiri. Ndipo zimakhala zosangalatsa kwambiri kuona anthu akulabadira ulaliki wathu. (Mac. 15:3) Ngakhale pamene anthu alibe chidwi kapena akutitsutsa, utumiki umatitsitsimulabe mwauzimu. Zili choncho chifukwa chakuti timadziwa kuti Yehova amasangalala ndi khama lathu ndiponso timadziwa kuti zabwino zilizonse zimene timapeza mu utumiki wathu zimatheka chifukwa cha madalitso ake.—Mac. 5:41; 1 Akor. 3:9.

4 Mwa kulabadira pempho la Yesu, timakhala ndi mwayi wotumikira naye limodzi monga Mboni za Yehova. (Yes. 43:10; Chiv. 1:5) Palibe chinthu china chomwe chingatitsitsimule kuposa zimenezi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena