Tsanzirani Ubwino wa Yehova
1 Tikaona kuloŵa kwa dzuŵa kochititsa chidwi kapena tikadya chakudya chokoma kwambiri, kodi sizitichititsa kuyamikira Yehova, yemwe ndi Gwero la zinthu zonse zabwino? Ubwino wake umatichititsa kufuna kumutsanzira. (Sal. 119:66, 68; Aef. 5:1) Kodi tingasonyeze bwanji ubwino?
2 kwa Anthu Osakhulupirira: Imodzi mwa njira zimene tingatsanzirire ubwino wa Yehova ndiyo mwa kusonyeza ndi mtima wonse kuti timaganizira anthu osakhulupirira. (Agal. 6:10) Kusonyeza ubwino powathandiza kungawachititse kuziona bwino Mboni za Yehova ndiponso uthenga umene timalalikira.
3 Mwachitsanzo, mpainiya wina wachinyamata ali pa mzera kuti alandire mankhwala pa chipatala china, anakhala pafupi ndi mzimayi wachikulire amene ankaoneka kuti akudwala kwambiri kuposa ambiri mwa anthu amene analipo. Itafika nthaŵi yoti mbaleyo aonane ndi dokotala, anauza mzimayiyo kuti apite m’malo mwa iye. Patapita nthaŵi anadzakumananso, koma panthaŵiyi kunali ku msika ndipo mzimayiyo anasangalala kumuona mbaleyo. Ngakhale kuti poyamba sanali kumvetsera uthenga wabwino, tsopano anati anadziŵa kuti Mboni za Yehova zimakondadi anzawo. Anayamba phunziro la Baibulo la nthaŵi zonse.
4 kwa Abale Athu: Timatsanziranso ubwino wa Yehova tikamathandiza okhulupirira anzathu. Pakachitika mavuto adzidzidzi, timakhala m’gulu la anthu oyambirira kuthandiza abale athu. Timasonyezanso mtima umenewu pothandiza anthu amene amafuna zoyendera kuti apite ku misonkhano, pochezera anthu odwala chifukwa cha ukalamba, ndiponso posonyeza chikondi kwa anthu amene sitikuwadziŵa bwino mumpingomo.—2 Akor. 6:11-13; Aheb. 13:16.
5 Njira ina imene Yehova amasonyezera ubwino ndiyo mwa kukhala “wokhululukira.” (Sal. 86:5) Pomutsanzira, tingasonyeze kuti timakonda ubwino mwa kukhululukira ena. (Aef. 4:32) Zimenezi zimathandiza kuti kukhala kwathu pamodzi ndi okhulupirira anzathu kukhale ‘kokoma ndi kokondweretsa.’—Sal. 133:1-3.
6 Ubwino wochuluka wa Yehova utichititse kum’tamanda kwambiri komanso kukhala ndi chimwemwe chodzaza tsaya. Ndiponso utilimbikitse kuyesetsa kutsanzira ubwino wake pa zonse zimene timachita.—Sal. 145:7; Yer. 31:12.