Valani Kudzichepetsa
1 Davide, mbusa wachinyamata, anadalira Yehova ndipo anagonjetsa msilikali wamphamvu kwambiri. (1 Sam. 17:45-47) Yobu, munthu wolemera, anapiririra mavuto moleza mtima. (Yobu 1:20-22; 2:9, 10) Yesu Mwana wa Mulungu anati zonse zimene anaphunzitsa zinali zochokera kwaAtate ake. (Yoh. 7:15-18; 8:28) M’zitsanzo zonsezi, anthuwo anadzichepetsa kwambiri. Masiku anonso, kudzichepetsa n’kofunika kwambiri pamene tikukumana ndi zinthu zosiyanasiyana.—Akol. 3:12.
2 Polalikira: Ife monga atumiki achikristu, timalalikira choonadi kwa anthu a mitundu yonse modzichepetsa, osawaweruziratu chifukwa cha mtundu wawo, chikhalidwe chawo, kapena moyo wawo. (1 Akor. 9:22, 23) Ngati ena ali amwano kapena akukana uthenga wa Ufumu mwachipongwe, sitiwabwezera koma timapitiriza moleza mtima kufunafuna anthu oyenerera. (Mat. 10:11, 14) M’malo mofuna kugometsa anthu ndi zimene tikudziŵa kapena maphunziro athu, timawasonyeza Mawu a Mulungu, pozindikira kuti mawuwo akhoza kuwalimbikitsa kuchitapo kanthu kuposa chilichonse chimene tinganene. (1 Akor. 2:1-5; Aheb. 4:12) Potsanzira Yesu, timatamanda Yehova m’zonse.—Marko 10:17, 18.
3 Mu Mpingo: Akristu ayeneranso ‘kuvala kudzichepetsa kuti atumikirane.’ (1 Pet. 5:5) Tikamaona anthu ena kukhala otiposa, tidzafufuza njira zotumikirira abale athu m’malo mofuna kuti iwowo azititumikira. (Yoh. 13:12-17; Afil. 2:3, 4) Sitidzadziona ngati ndife apamwamba oti sitingagwire nawo ntchito zina monga kuyeretsa pa Nyumba ya Ufumu.
4 Kudzichepetsa kumatithandiza “kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi” ndipo tikatero timalimbitsa mtendere ndi mgwirizano mumpingo. (Aef. 4:1-3) Kumatithandiza kugonjera anthu amene aikidwa kuti azititsogolera. (Aheb. 13:17) Kumatichititsa kulandira malangizo kapena chilango chimene tingapatsidwe. (Sal. 141:5) Ndipo kudzichepetsa kumatilimbikitsa kudalira Yehova pogwira ntchito iliyonse imene tingapatsidwe mumpingo. (1 Pet. 4:11) Mofanana ndi Davide, timazindikira kuti zinthu zikayenda bwino sikuti n’chifukwa cha luso la anthu koma n’chifukwa cha dalitso la Mulungu.—1 Sam. 17:37.
5 Kwa Mulungu Wathu: Koposa zonse, tifunika ‘kudzichepetsa pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu.’ (1 Pet. 5:6) Ngati tikulimbana ndi mavuto ena ake, tingafune mpumulo umene Ufumuwo udzabweretsa. Komabe timaleza mtima modzichepetsa, kuyembekezera Yehova kuti adzakwaniritse malonjezo ake panthaŵi yake yoikika. (Yak. 5:7-11) Monga mmene anachitira Yobu wokhulupirika, nkhaŵa yathu yaikulu ndi yoti “lidalitsike dzina la Yehova.”—Yobu 1:21.
6 Mneneri Danieli ‘anadzichepetsa pamaso pa Mulungu wake’ ndipo Yehova anakondwera naye n’kumupatsa mwayi waukulu wom’tumikira. (Dan. 10:11, 12) Mofanana ndi Danieli, tiyeni tivale kudzichepetsa podziŵa kuti “mphotho ya chifatso ndi kuopa Yehova ndiye chuma, ndi ulemu, ndi moyo.”—Miy. 22:4.