Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/03 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira September 8
  • Mlungu Woyambira September 15
  • Mlungu Woyambira September 22
  • Mlungu Woyambira September 29
  • Mlungu Woyambira October 6
Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
km 9/03 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira September 8

Nyimbo Na. 10

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Sankhani zilengezo zina mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Limbikitsani anthu onse kuti akaonenso notsi zawo za msonkhano wadera wa chaka chautumiki chapita pokonzekera Msonkhano wa Utumiki wa mlungu wamaŵa.

Mph. 10: Kalata Yochokera ku Nthambi. Wofalitsa amene anayamba kale ntchitoyi, amene zingakhale bwino atakhala mkulu, akambirane ndi wofalitsa wachinyamata. Wofalitsa wachinyamatayo afunse wofalitsa amene anayamba kaleyo ngati waona kalata yochokera ku nthambi mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Wofalitsa amene anayamba kaleyo afotokoze kuti m’zaka za m’ma 1960 ndi m’ma 1970, kalata yochokera ku nthambi anali kuilemba mu Utumiki Wathu wa Ufumu uliwonse. Ndiyeno akambirane kalata imene ili patsamba loyambalo ndipo atsindike mfundo zazikulu za kalatayo.

Mph. 25: “Achinyamata—Konzani Maziko Abwino a Tsogolo Lanu.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Mkulu akambe nkhani imeneyi pogwiritsa ntchito mafunso amene aperekedwawo. Pokambirana ndime 5, gogomezerani chimwemwe ndi madalitso amene amapezeka chifukwa chochita utumiki wa nthaŵi zonse.

Nyimbo Na. 170 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira September 15

Nyimbo Na. 199

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.

Mph. 10: “Kuphunzira buku la Lambirani Mulungu.” Nkhaniyi ikambidwe ndi woyang’anira phunziro la buku. Tchulani za ndandanda yophunzirira bukuli. Pokambirana ndime yachinayi, phatikizanipo ndemanga za m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 28, ndime 1, ndi tsamba 70.

Mph. 25: “Khulupirirani Yehova Ndipo Chitani Chokoma.” (Sal. 37:3) Kukambirana ndi omvetsera pogwiritsa ntchito mafunso otsatiraŵa omwe akusonyeza mfundo zazikulu za msonkhano wadera wa chaka chautumiki chapitachi. Pemphani omvetserawo kuti m’ndemanga zawo atchuleponso mmene anagwiritsira ntchito mfundo zazikuluzo paokha kapena monga banja. Kambiranani nkhani za msonkhano zotsatirazi: (1) “Kusonyeza Kukhulupirira Yehova.” N’chifukwa chiyani n’kofunika kwambiri kusonyeza kukhulupirira Yehova pa zochita zonse? (it-2 tsa. 521) Kodi Watch Tower Publications Index ingatithandize bwanji? (2) “Samalani ndi Zinthu Zopanda Pake pa Moyo.” (Mlal. 2:4-8, 11) Kodi ndi ntchito zopanda pake ziti zimene tiyenera kusamala nazo, ndipo tingachite bwanji zimenezo? (3) “Peŵani Zoipa, Khalani Ochita Zokoma.” N’chifukwa chiyani n’kofunika kutsatira miyezo ya Yehova? (Yes. 5:20) Kodi tiyenera kuthera nthaŵi yathu yambiri kuchita ntchito zabwino zotani? (4) “Kupitirizabe Kukhulupirira Yehova.” Kodi n’chiyani chingatithandize kukhalabe olimba tikamakumana ndi ziyeso kapena zokopa? N’chifukwa chiyani tifunika kusiya zinthu zina m’manja mwa Yehova? (5) “Kodi Mudzaŵerengedwa Oyenera Ufumu wa Mulungu?” (Akol. 1:10) Kodi ndi zitsanzo za m’Baibulo ziti zimene zikutilimbikitsa kupitirizabe kuyenda moyenera Yehova? (6) “Khulupirirani Malonjezo a Yehova.” Kodi kuchita zimenezi kudzakhudza bwanji moyo wathu?

Nyimbo Na. 58 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira September 22

Nyimbo Na. 7

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo zimene zili patsamba 4, khalani ndi zitsanzo ziŵiri zosonyeza zomwe zingachitikedi pogaŵira Nsanja ya Olonda ya September 15 ndi Galamukani! ya September 8. M’chitsanzo chimodzi, sonyezani mwana wasukulu kapena kholo likulalikira kwa mphunzitsi.

Mph. 15: Kodi Tinachita Zotani Chaka Chatha? Woyang’anira utumiki afotokoze mfundo zazikulu za lipoti la mpingowo la chaka chautumiki cha 2003. Yamikirani anthu mumpingomo chifukwa cha ntchito yabwino imene anachita. Phatikizanipo mfundo zoyenerera za lipoti la woyang’anira dera la ulendo wapita. Tchulani cholinga chimodzi kapena ziŵiri zimene zingatheke kuzikwaniritsa chaka chamaŵa.

Mph. 20: Kodi Mulungu Amavomereza Zipembedzo Zonse? Kukambirana ndi omvetsera pogwiritsa ntchito buku la Kukambitsirana. Kambiranani mmene tingakambirane mfundo imeneyi ndi munthu wina. (rs-CN tsa. 83 mpaka 85) Fotokozani zina mwa njira zimene tingadziŵire chipembedzo choona. (rs-CN tsa. 89 mpaka 91) Utumiki wathu umathandiza anthu kusankha kalambiridwe kamene Mulungu amavomereza.—Akol. 1:9, 10.

Nyimbo Na. 39 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira September 29

Nyimbo Na. 194

Mph. 13: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wawo wakumunda a September. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo zimene zili patsamba 4, khalani ndi zitsanzo ziŵiri zosonyeza mmene tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya October 1 ndi Galamukani! ya September 8. Tchulani mabuku amene tidzagaŵira mu October. Sonyezani chitsanzo chachidule cha mmene tingayambitsire phunziro la Baibulo pogwiritsa ntchito bulosha la Mulungu Amafunanji.

Mph. 12: Zosoŵa za pampingo.

Mph. 20: “Valani Kudzichepetsa.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Limbikitsani omvetserawo kufotokoza mmene malembawo akugwirizanira ndi nkhaniyi.

Nyimbo Na. 224 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira October 6

Nyimbo Na. 170

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Mwezi uno tikufuna kuyesetsa mwapadera kuti tiyambitse maphunziro a Baibulo. Pendani mwachidule Utumiki Wathu wa Ufumu wa May 2002, tsamba 1, ndime 1.

Mph. 15: “Tsimikizani Kuika Zinthu Zofunika Pamalo Oyamba!” Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera pogwiritsa ntchito nkhani imene ili mu Nsanja ya Olonda ya September 1, 1998, masamba 19 mpaka 21. Tchulani masiku amene kudzakhale zochitika zauzimu m’miyezi ingapo ikubwerayi, ndipo limbikitsani onse kulemba masiku ameneŵa pa makalendala awo. Pemphani omvetserawo kufotokoza zimene amachita kuti asaphonye zochitika zauzimu.

Mph. 20: Kusalolera Kutengera Zimene Ena Akuchita. Funsani mkulu kapena mtumiki wotumikira amene anakulira m’banja lachikristu. Gwiritsani ntchito mfundo zomwe musankhe mu Nsanja ya Olonda ya February 15, 2003. Kodi mbaleyo anakumana ndi zovuta zotani kusukulu? (tsa. 24 ndime 3; tsa. 25 ndime 4 mpaka 5) Kodi anakumanapo ndi anthu amene ankachita zinthu zoipa zimene akanatha kutengera? (tsa. 26 ndime 4 mpaka 6) Kodi panopa, pamene ali wamkulu, amakumanabe ndi vuto lofuna kutengera zimene ena akuchita? N’chiyani chamuthandiza kuti asalolere kutengera zimene ena akuchita? Pomaliza, kambani nkhani yachidule kuchokera mu Nsanja ya Olonda ya August 1, 1999 masamba 24 mpaka 25. Tsindikani phindu locheza ndi anthu oyenera.

Nyimbo Na. 26 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena