Nyimbo 170
“Mulungu Akhale Wowona”
1. Yehova ndiwacho’nadi;
Samanama konse.
Nthaŵi zonse timdalira;
Sangadzikanetu.
Iye alitu wowona
Munthu ndiwonama.
Cho’nadi chake chikhala
Kunthaŵi zosatha.
2. Pamene anatumiza
Mwana’ke padziko,
Yesu anasonyezabe,
Kuwona kwa M’lungu.
Chifuno cha Ya chinali,
Lamulo kwa iye.
Anakondwa m’choyenera
Natsogoza “nkhosa.”
3. Ngakhale anthu anyoza
Mawu a Mulungu,
Ife tisonyeza kuti;
M’lungu ndiwowona.
Tilalikira cho’nadi
Chokhala ndi mphamvu.
Tifuna cho’nadi chake,
Ndi kumvera M’lungu.