Ntchito Imene Imatheka Chifukwa cha Mulungu
1 Mwa atumiki a Mulungu masiku ano, ndi ochepa amene ali ndi maphunziro apamwamba, chuma, kapena amene ali otchuka m’dzikoli. Pachifukwa chimenechi, anthu ena amangoti utumiki wathu ndi wopanda phindu. (Yes. 53:3) Komabe, ntchito imene timachitayi yophunzitsa anthu Baibulo yapatsa ambiri chitonthozo ndi chiyembekezo padziko lonse lapansi. Kodi zatheka bwanji kuti anthu wamba achite zinthu zazikulu choncho? Zatheka chifukwa cha Mulungu. (Mat. 28:19, 20; Mac. 1:8) Mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Zofooka za dziko lapansi Mulungu anazisankhula, kuti akachititse manyazi zamphamvu.”—1 Akor. 1:26-29.
2 Atumwi ambiri komanso Akristu ena a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino anali “osaphunzira ndi opulukira [“anthu wamba,” NW].” (Mac. 4:13) Ngakhale ndi choncho, iwo molimba mtima anachita ntchito yawo yolalikira uthenga wabwino, ndipo Yehova anawadalitsa. Ngakhale kuti iwo anakumana ndi mavuto ndi anthu otsutsa, “mawu a Ambuye anachuluka mwamphamvu nalakika.” Palibe chimene chikanaletsa ntchitoyo chifukwa Mulungu ndiye anali mwiniwake. (Mac. 5:38, 39; 19:20) Ndi mmenenso zilili masiku ano. Ngakhale olamulira amphamvu amene ayesetsa kutsutsa kuti uthenga wabwino usachuluke ndi kulakika alephera.—Yes. 54:17.
3 Ulemu Wonse Upite kwa Mulungu: Kodi mwayi umene tili nawo wokhala atumiki a Mulungu umatipatsa chifukwa chodzitamandira? Kutalitali. Za utumiki wachikristu, Paulo analemba kuti: “Tili nacho chuma ichi m’zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife.” (2 Akor. 4:7) Paulo anazindikira kuti anatha kuchita utumiki wake chifukwa cha nyonga imene Mulungu anam’patsa.—Aef. 6:19, 20; Afil. 4:13.
4 Ifenso timazindikira kuti ntchito yathu yolalikira ikutheka chifukwa ‘chothandizidwa ndi Mulungu.’ (Mac. 26:22) Mwa ntchito yolengeza imeneyi padziko lonse, Yehova akutigwiritsa ntchito mwamphamvu kugwedeza amitundu monga chizindikiro cha chiwonongeko choopsa chimene chikudza posachedwa. (Hag. 2:7) Komatu ndiye tili ndi mwayi waukulu pokhala “antchito anzake a Mulungu” pantchito yaikuluyi yotuta mwauzimu!—1 Akor. 3:6-9.