“Tikweze Dzina Lake Pamodzi”
1. Kodi ndi mpata uti umene tikhale nawo wokweza dzina la Mulungu pamodzi, ndipo kodi tingachite chiyani pakalipano pokonzekera?
1 Wamasalmo anaimba kuti: “Bukitsani pamodzi ndi ine ukulu wa Yehova, ndipo tikweze dzina lake pamodzi.” (Sal. 34:3) Msonkhano wathu Wachigawo umene ukubwerawu wakuti “Yendani ndi Mulungu” udzatipatsa mpata wokweza dzina la Yehova, tili pamodzi ndi abale ndi alongo athu a m’mipingo yosiyanasiyana. Kodi mwakonza za malo ogona, kayendedwe, ndiponso zotenga tchuti ku ntchito? Tingachite bwino kuchitiratu zinthu zimenezi kukadali nthaŵi.—Miy. 21:5.
2. N’chifukwa chiyani ndi bwino kukonza zokafika msanga pamalo amsonkhano?
2 Kufika Pamalo Amsonkhano: Pali nkhani zambiri zofunika kuzisamalira pamene tikupita kumsonkhano. Kunyamuka mwamsanga kudzatithandiza kuthana bwinobwino ndi zochitika mwadzidzidzi zimene zingatichedwetse ndiponso kudzatithandiza kukhala m’malo athu panthaŵi yake kuti tiimbe nawo nyimbo yotsegulira ndi mtima wonse ndiponso kuti titsatire bwinobwino pemphero loyamba. (Sal. 69:30) Kutatsala mphindi zingapo kuti mapulogalamu achigawo chilichonse ayambe, tcheyamani adzakhala papulatifomu nyimbo za Ufumu za pamakaseti zikuimbidwa. Tonse tiyenera kukhala pansi panthaŵi imeneyi kuti pulogalamu iyambe bwino.—1 Akor. 14:33, 40.
3. Kodi tingasonyeze bwanji kuganizira ena pamene tikupeza malo okhala?
3 Mawu a Mulungu amatilangiza kuti zochita ‘zathu zonse zichitike m’chikondi.’ (1 Akor. 16:14) Akatsegula makomo pa 7:00 m’maŵa, ngati timaganizira ena tidzapeŵa kuthamanga, kuyenda mofulumira kapena kukankhana pothamangira kukapeza malo okhala amene tikufuna ena asanakhalepo. Tingasungire malo anthu okhawo amene tabwera nawo pagalimoto imodzi kapena amene timakhala nawo nyumba imodzi.—1 Akor. 13:5; Afil. 2:4.
4. Kodi tiyenera kuchitanji masana panthaŵi yopuma, ndipo n’chifukwa chiyani ndi bwino kutero?
4 Chonde mudzatenge chakudya chamasana m’malo mochoka pamalo amsonkhano kukagula chakudya panthaŵi yopuma. Izi zidzathandiza onse kusangalala ndi macheza olimbikitsa ndiponso kuti azikhalapo pamene chigawo chamasana chikuyamba. Chonde kumbukirani kuti zotengera zagalasi ndi moŵa siziloledwa pamalo a msonkhano.
5. Kodi tingakonzekeretse bwanji mitima yathu kuti tikalandire malangizo?
5 Phwando Lauzimu Likutidikira: Mfumu Yehosafati anali munthu amene ‘analunjikitsa mtima wake kufuna Mulungu.’ (2 Mbiri 19:3) Kodi tingalunjikitse kapena kuti tingakonzekeretse bwanji mtima wathu msonkhano usanafike? Patsamba lomaliza la Galamukani! ya June 8 pali nkhani yofotokoza mwachidule chakudya chauzimu chimene chikaperekedwe. Bwanji osakhala ndi nthaŵi yolingalira nkhani zimenezi, kuti muwonjezere chidwi chanu poyembekezera zimene Yehova watisungira? Kukonzekeretsa mtima wathu kumaphatikizapo kupempha Yehova kuti akatithandize kumvetsa mfundo za malangizo amene tikalandire ndiponso kuwagwiritsa ntchito.—Sal. 25:4, 5.
6. Kodi tikulakalaka chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani?
6 Tonse tikulakalaka kukaphunzira zambiri za m’Mawu a Mulungu, chifukwa tikudziŵa kuti zimenezi zingatithandize kuti tidzapulumuke. (1 Pet. 2:2) Choncho, tiyeni tikapezekepo pa Msonkhano wathu Wachigawo wakuti “Yendani ndi Mulungu” ndi ‘kukweza dzina la Yehova pamodzi.’—Sal. 34:3.
[Bokosi patsamba 3]
Njira Zokwezera Dzina la Mulungu
◼ Kukonzekereratu kukadali nthaŵi
◼ Sonyezani kukonda ena
◼ Konzekeretsani mtima wanu