Kusonkhana Pamodzi Kuti Titamande Yehova
1. Kodi msonkhano wachigawo uli ndi mutu wotani, ndipo n’chifukwa chiyani Yehova ndi woyenera kumutamanda?
1 Yehova ndi wamphamvuyonse, ndi wanzeru zosasanthulika, chilungamo chake n’changwiro, ndipo iye ndiye chikondi. Monga Mlengi, Wopereka Moyo, ndiponso Wolamulira wa Chilengedwe Chonse, iye yekha ndi amene tiyenera kumulambira. (Sal. 36:9; Chiv. 4:11; 15:3, 4) Msonkhano Wachigawo wa chaka chino wakuti “Patsani Mulungu Ulemerero” udzalimbitsa kutsimikiza mtima kwathu kumutamanda monga Mulungu woona yekha.—Sal. 86:8-10.
2, 3. Kodi kukonzekera bwino kudzatithandiza bwanji kupindula mokwanira?
2 Kukonzekera Bwino N’kofunika: Kuti tikapindule mokwanira pa phwando lauzimu limene Yehova watisungira, n’kofunika kukonzekera bwino. (Aef. 5:15, 16) Kodi mwamaliza kukonzekera za kayendedwe, ndi kupempha tchuti kuntchito kapena kusukulu? Musangokhala kuti mudzakonze zinthu zofunika zimenezi nthaŵi itangotsala pang’ono. Mukachedwa kupempha tchuti, mungaphonye mbali ina ya nthaŵi yosangalatsa imeneyi. Tonsefe tifunika kudzapezeka pa chigawo chilichonse.
3 Khalani ndi cholinga chodzafika mofulumira pa malo a msonkhanowu tsiku lililonse. Zimenezi zidzakuthandizani kukhazikika m’malo mwanu nyimbo yotsegulira isanayambe ndipo zidzakuthandizaninso kukonzekeretsa maganizo anu kuti mulandire malangizo amene adzakhala akuperekedwa.
4. N’chifukwa chiyani tonsefe tikupemphedwa kudzabweretsa chakudya chamasana ku msonkhano?
4 Tonsefe tikupemphedwa kudzabweretsa chakudya chathu cha masana osati kuchoka pa malo a msonkhano kukagula chakudya pa nthaŵi yopuma masana. Mukatsatira dongosolo limeneli zidzathandiza kuti pakhale bata ndiponso zidzakuthandizani kukhala ndi nthaŵi yokwanira yocheza ndi okhulupirira anzanu. (Sal. 133:1-3) Kumbukirani kuti zotengera zagalasi komanso mowa n’zosaloleka pa malo a msonkhano.
5. Kodi tingayambe bwanji kukonzekeretsa mitima yathu kuti tikapindule pamsonkhanowu?
5 Mvetserani Ndiponso Phunzirani: Ezara anakonzekeretsa mtima wake mwapemphero kuti alandire mawu a Mulungu. (Ezara 7:10) Analozetsa mtima wake ku zimene Yehova anaphunzitsa. (Miy. 2:2) Tingayambe kukonzekeretsa mitima yathu kuti tikapindule pamsonkhanowu ngakhale tisanachoke panyumba mwa kusinkhasinkha mutu wa msonkhano ndi kuukambirana ndi a m’banja mwathu.
6. N’chiyani chingatithandize kuika maganizo athu pa pulogalamu? (Onani bokosi.)
6 Pa malo a msonkhano pangakhale zinthu zambiri zofuna kuziona ndi kuzimvetsera zimene zingadodometse kutchera kwathu khutu. Zododometsa zimenezo zingatichititse kusamvetsera amene akukamba nkhani. Zikatere, timaphonya mfundo zofunika kwambiri. Mfundo zimene zili m’bokosi limene lili m’nkhani ino zingatithandize kunola luso lathu loika maganizo pa pulogalamu.
7, 8. Kodi tingasonyeze bwanji kuganizira ena?
7 Ganizirani Ena: Makamera angagwiritsidwe ntchito pulogalamu ili m’kati, koma popewa kudodometsa ena, muzingojambula kuchokera pa malo amene mwakhala basi. Muyenera kutseka matelefoni a m’manja kuti asadodometse ena. Musalumikize chipangizo chanu chilichonse ku magetsi kapena zokuzira mawu za pamsonkhano.
8 Inde, tikuyembekezera mwachidwi kudzasonkhana pamodzi kuti tidzatamande Yehova. Tiyenitu titsimikize mtima kudzamulemekeza mwa kupezeka pa chigawo chilichonse, kumvetsera mosamalitsa, ndi kugwiritsa ntchito zimene tidzaphunzira.—Deut. 31:12.
[Bokosi patsamba 3]
Kumvetsera pa Misonkhano Yachigawo
▪ Sinkhasinkhani mitu ya nkhanizo
▪ Ŵerenga nawoni malemba
▪ Lembani notsi zachidule
▪ Onani mfundo zimene mukazigwiritse ntchito
▪ Bwerezani zimene mwaphunzira