Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/04 tsamba 8
  • Tsanzirani Mtima wa Yesu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tsanzirani Mtima wa Yesu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Nkhani Yofanana
  • Sonyezani Mtima wa Kristu
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Muzitsanzira Yesu Potumikira Ena
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Cholinga Chabwino Kwambiri M’chaka Chautumiki Chatsopano
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Chikondi cha Khristu Chimatilimbikitsa Kukonda Ena
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
km 4/04 tsamba 8

Tsanzirani Mtima wa Yesu

1. Kodi Yesu anasonyeza mtima wotani?

1 Ngakhale kuti sitinamuonepo Yesu, Mwana wa Mulungu, tafika pom’konda kwambiri chifukwa cha nkhani zimene zinalembedwa zonena za moyo wake ndi utumiki wake. (1 Pet. 1:8) Pochita zofuna za Atate wake, anasiya malo ake okwezeka kumwamba n’kubwera padziko lapansi pano. Monga munthu, anatumikira anthu ena mopanda dyera ndipo kenako anapereka moyo wake m’malo mwa anthu. (Mat. 20:28) Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti: “Mukhale nawo mtima mkati mwanu umene unalinso mwa Kristu Yesu.” Kodi tingatsanzire bwanji mtima wake wodzipereka?—Afil. 2:5-8.

2. Kodi Akristu ambiri amakumana ndi vuto lanji, ndipo n’chiyani chingawathandize kugonjetsa vutolo?

2 Tikatopa: Ngakhale kuti Yesu anali wangwiro, iye ankatopa. Nthaŵi ina, ‘atalema ndi ulendo,’ anachitira umboni mokwanira kwa mkazi wachisamariya. (Yoh. 4:6) Akristu ambiri masiku ano amakumananso ndi vuto limeneli. Pamapeto a mlungu umene tagwira ntchito yotopetsa, zingakhale zovuta kupeza mphamvu kuti tichite nawo ntchito yolalikira. Komabe, ngati tichita utumiki wachikristu nthaŵi zonse, tidzaona kuti utumikiwu umatitsitsimula mwauzimu.—Yoh. 4:32-34.

3. Kodi tingatsanzire bwanji mtima wa Yesu wofunitsitsa kuphunzitsa?

3 Nthaŵi ina, Yesu ndi ophunzira ake anapita kumalo awokha kuti akapumule pang’ono. Komabe, khamu la anthu linadziŵa zimenezi ndipo linathamanga n’kukayamba ndilo kufika pamalowo kuti likumane nawo. M’malo mokwiya, Yesu ‘anagwidwa chifundo ndi iwo’ ndipo anayamba “kuwaphunzitsa zinthu zambiri.” (Marko 6:30-34) Mtima ngati umenewu ndi umene umafunika kuti tithe kuyambitsa maphunziro a Baibulo ndi kupitiriza kuchititsa maphunzirowo. Pamafunika kulimbikira kwambiri ndiponso kuwakondadi anthu. Ngati panopo mulibe phunziro la Baibulo musasiye kufufuza.

4. Kodi upainiya wothandiza ungatithandize bwanji kutsanzira mtima wa Kristu?

4 Tsogozani Zinthu Zauzimu: Upainiya wothandiza ungatithandize kuika mtima kwambiri pa zochita zauzimu. Mlongo wina wachitsikana analemba kuti: “Amayi ake a mnzanga wina anatilimbikitsa kuchitira nawo pamodzi upainiya wothandiza kwa mwezi umodzi. Ndimasangalala kwambiri kuti ndinachita nawo. Ndinasangalala kuwadziŵa bwino abale ndi alongo, ndipo mosakhalitsa ndinayamba kuwaona ngati a m’banja langa. Ndinasangalalanso kuti ndinali ndi nthaŵi yambiri youza ena za Yehova ndiponso kuwaphunzitsa mfundo zosangalatsa za Ufumu. Zonsezi zinandithandiza kuyandikana kwambiri ndi Yehova ndi gulu lake.”—Sal. 34:8.

5. Kodi n’chifukwa chiyani nthaŵi zonse tiyenera kuyesetsa kutsanzira mtima wa Yesu?

5 Tonsefe timakhala pa nkhondo pakati pa thupi lathu lopanda ungwiroli ndi chikhumbo chathu chofuna kusangalatsa Yehova. (Aroma 7:21-23) Tiyenera kupeŵa mtima wosadzipereka wa dzikoli. (Mat. 16:22, 23) Yehova angatithandize mwa mzimu wake woyera kupambana nkhondoyi. (Agal. 5:16, 17) Pamene tikudikira kupulumutsidwa kuloŵa m’dziko latsopano la Mulungu limene mudzakhale chilungamo, tiyeni titsanzire mtima wa Yesu mwa kuika zinthu za Ufumu ndiponso zokonda za ena patsogolo pa zokonda zathu.—Mat. 6:33; Aroma 15:1-3.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena