Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/04 tsamba 1
  • Tsanzirani Chilungamo cha Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tsanzirani Chilungamo cha Yehova
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Nkhani Yofanana
  • Tsanzirani Yehova—Chitani Chilungamo
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Yehova—Gwero la Chilungamo Chenicheni
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Yehova Wokonda Chilungamo ndi Chiweruzo
    Nsanja ya Olonda—1996
  • “Njira Zake Zonse Ndi Zolungama”
    Yandikirani Yehova
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
km 7/04 tsamba 1

Tsanzirani Chilungamo cha Yehova

1 “Yehova akonda chiweruzo [“chilungamo, NW].” (Sal. 37:28) Choncho, ngakhale kuti walamula kuti dziko loipali liyenera kuwonongedwa, wakonza zoti choyamba chenjezo liperekedwe. (Mark 13:10) Zimenezi zikupereka mwayi wakuti anthu alape ndi kupulumuka. (2 Pet. 3:9) Kodi tikuyesetsa kutsanzira chilungamo cha Yehova chimenechi? Kodi mavuto amene anthu onse akukumana nawo amatilimbikitsa kuuza ena za chiyembekezo cha Ufumu? (Miy. 3:27) Ngati timakonda chilungamo, tidzalalikira mwachangu.

2 Lalikirani Mopanda Tsankho: Mwa kulalikira za chifuno cha Mulungu kwa aliyense mopanda tsankho, ‘timachita cholungama.’ (Mika 6:8) Chifukwa cha kupanda ungwiro tili ndi chibadwa chokonda kuweruza ena mwa maonekedwe awo akunja, koma tiyenera kupewa zimenezo. (Yak. 2:1-4, 9) Cholinga cha Yehova n’chakuti “anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.” (1 Tim. 2:4) Choonadi cha mawu a Mulungu chingathe kusintha miyoyo ya anthu. (Aheb. 4:12) Kuzindikira zimenezi kungatilimbitse mtima kuti tifikire aliyense, ngakhalenso aja amene anakana uthenga wathu m’mbuyomo.

3 Mlongo wina amene amagwira ntchito m’sitolo, anali wodabwa kwambiri ndi maonekedwe a munthu wina amene anali kukonda kuwagula zinthu. Koma pamene mpata wabwino unapezeka, mlongoyo anayesa kulalikira munthuyo kumuuza za Paradaiso amene Mulungu analonjeza. Mwamunayo, mosazengereza komanso mwamwano, anayankha kuti sakhulupirira nthano zabodza komanso kuti iye sagwirizana ndi chikhalidwe cha anthu akumeneko ndiponso amakonda kumwa mankhwala osokoneza bongo. Komabe mlongoyo sanalekere pomwepo. Tsiku lina mwamunayo anafunsa mlongoyo maganizo ake pa za tsitsi lake lalitali. Mlongoyo mosamala anafotokoza zimene Baibulo limanena pa nkhani imeneyi. (1 Akor. 11:14) Mosayembekezera, tsiku lotsatira mwamunayo anali atameta tsitsi lake ndipo anali ndi tsitsi lalifupi bwino! Anapempha phunziro la Baibulo, ndipo mbale wina anayamba kuphunzira ndi mwamunayu. Iye anapita patsogolo mpaka anadzipatulira ndi kubatizidwa. Mofanana ndi mwamuna ameneyu, ambiri amene akutumikira Yehova lerolino ndi oyamikira chifukwa cha kupanda tsankho komanso kupirira kwa amene anawabweretsera uthenga wa Ufumu.

4 Posachedwapa Yehova adzachotsa kuipa konse padziko lonse lapansili. (2 Pet. 3:10, 13) Kwa nthaŵi yochepa imene yatsalayi, tiyeni tiyesetse kutsanzira chilungamo cha Yehova mwa kupereka mwayi kwa onse woti adzapulumuke chiwonongeko cha dziko loipa la Satanali chomwe chikudzacho.—1 Yoh. 2:17.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena