Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo—Gawo 2:
Kukonzekera Kuchititsa Phunziro
1 Kuphunzitsa kogwira mtima pochititsa phunziro la Baibulo kumafuna zambiri m’malo mongokambirana nkhaniyo ndi kuŵerenga malemba amene sanagwidwe mawu. Pophunzitsa, tiyenera kum’fika pamtima wophunzira wathu. Zimenezi zimafuna kuti tizikonzekera mokwanira bwino ndiponso tiziganiza za wophunzira wathuyo pamene tikukonzekera.—Miy. 15:28.
2 Mmene Mungakonzekerere: Choyamba, pempherani kwa Yehova za wophunzira wanu ndi zosoŵa zake. M’pempheni Yehova kuti akuthandizeni kum’fika pamtima wophunzira wanu. (Akol. 1:9, 10) Kuti mumvetsetse bwino kwambiri mfundo yaikulu ya nkhani imene mukaphunzire, ganizani kaye za mutu wa nkhaniyo, timitu take , ndi zithunzi zake. Dzifunseni kuti, ‘Kodi cholinga chake cha nkhaniyi n’chiyani?’ Zimenezi zidzakuthandizani kuti pokachititsa phunzirolo, mukatsindike mfundo zake zazikulu.
3 Mosamalitsa, ŵerengani nkhaniyo ndime ndi ndime. Pezani mayankho a mafunso amene aperekedwa, ndi kudula mzera kunsi kwa mawu okhawo amene ali ofunikira kwambiri. Ŵerengani malemba osagwidwa mawu ndi kuona mmene akugwirizanirana ndi mfundo yaikulu m’ndimeyo, ndipo sankhani amene mukaŵerenge pochititsa phunzirolo. Zimathandizanso kulemba timawu tochepa m’mphepete mwa tsamba la buku lanulo tofotokozera malembawo. Wophunzira wanu azitha kuona kuti zimene akuphunzira zilidi zochokera m’Mawu a Mulungu.—1 Ates. 2:13.
4 Gwirizanitsani Nkhaniyo ndi Zosoŵa Zake: Kenako, ganizirani za mmene nkhani imeneyo ikukhudzira wophunzira wanuyo. Yesani kupeza mafunso amene wophunzira wanu akhoza kukafunsa ndi mfundo zina zimene zingam’vute kuti azimvetsetse kapena kuti azivomereze. Dzifunseni kuti: ‘Kodi n’chiyani chimene afunika kumvetsetsa kapena kuwongolera kuti apite patsogolo mwauzimu? Kodi ndingam’fike bwanji pamtima? Ndiyeno konzani kaphunzitsidwe kanu kuti kagwirizane ndi zimene mwapezazo. Nthaŵi zina, mungaone kuti m’pofunika kukonza fanizo, kumveketsa bwinobwino mfundo inayake, kapena kukafunsa mafunso angapo kuti mukam’thandize wophunzirayo kumvetsa zimene mfundo inayake kapena lemba likutanthauza. (Neh. 8:8) Koma peŵani kuphatikizapo mfundo zina zimene sizikugwirizana kwenikweni ndi nkhaniyo. Pomaliza phunzirolo, bwereranimo mwachidule m’nkhaniyo kuti muthandize wophunzirayo kukumbukira mfundo zazikulu.
5 Timasangalala kwambiri atsopano akayamba kubereka zipatso zolungama zolemekeza Yehova! ( Afil. 1:11) Kuti muwathandize kufika pamenepo, muzikonzekera mokwanira bwino nthaŵi iliyonse pamene mukukachititsa phunziro la Baibulo.