Msonkhano Wachigawo Watilimbikitsa Kuyenda ndi Mulungu
Msonkhano Wachigawo wamutu wakuti “Yendani ndi Mulungu” unamveketsa bwino kwambiri langizo la Yehova lakuti: “Njira ndi iyi, yendani inu m’menemo”! (Yes. 30:21) Kugwiritsa ntchito malangizo amene tinalandira kudzatithandiza ‘kupenya bwino umo tiyendera.’ (Aef. 5:15) Kusinkhasinkha zimene tinaphunzira kudzatithandiza pamene tikupitirizabe ‘kuyenda m’choonadi.’—3 Yoh. 3.
Gwiritsani ntchito mafunso otsatirawa limodzi ndi manotsi anu amene munalemba kumsonkhano wachigawo kuti mukonzekere ndi kukatenga nawo mbali pomakabwereza pulogalamu ya msonkhano wa chaka chino. Kubwerezaku kudzachitika pa Msonkhano wa Utumiki wa mlungu woyambira October 18.
1. Kodi Enoke anatha bwanji kuyenda ndi Mulungu ngakhale kuti anali kukhala m’nthaŵi ya chipwirikiti? (Aheb. 11:1, 5, 6; Yuda 14, 15; “Yendani ndi Mulungu Nthaŵi ya Chipwirikiti”)
2. Kodi ndi mbali ziti za moyo zimene tingagwiritse ntchito mfundo imene ili pa Luka 16:10? (“Kodi Ndinu ‘Wokhulupirika M’zinthu Zazing’ono’?”)
3. (a) Tchulani mfundo zinayi zofunika zimene tinaphunzira m’buku la Hoseya chaputala 6 mpaka chaputala 9 zimene zidzatithandiza kuyenda ndi Mulungu. (Hos. 6:6, 7; 7:14; 8:7) (b) Kodi ndi mfundo zina ziti m’machaputala 10 mpaka 14 a Hoseya zimene zikutithandiza kuyenda ndi Mulungu? (“Ulosi wa Hoseya Umatithandiza Kuyenda ndi Mulungu”—Yosiyirana)
4. Kodi amuna ndi akazi achikristu okwatirana angachite zinthu ziti kuti ukwati wawo ukhale wolimba? (Miy. 12:4; Aef. 5:29; “Musalekanitse Chimene ‘Mulungu Anachimanga Pamodzi’”)
5. Kodi timasonyeza bwanji kuti timalemekeza misonkhano yathu yopatulika? (Mlal. 5:1; Yes. 66:23; “Kulemekeza Misonkhano Yathu Yopatulika”)
6. (a) Pantchito yathu yolalikira, kodi ndi zinthu zitatu zofunika ziti zimene tifunika kuziona bwino kuti titsimikizire kuti tikutenga nawo mbali mokwanira mu ntchito imeneyi? (Yes. 52:7; Zek. 8:23; Marko 6:34) (b) Ndi zinthu ziti m’kabuku ka Uthenga Wabwino wa Anthu a Mitundu Yonse zimene mwaziona kukhala zothandiza kwambiri? (“Uthenga Wabwino wa Anthu a Mitundu Yonse”; “Kuthandiza Anthu Olankhula Chinenero China”)
7. Kodi tingawathandize bwanji atsopano kukhala olimba mtima pouza ena za uthenga wa Ufumu? (Ower. 7:17; “Kuthandiza Anthu Ambiri Kutsagana Nafe mu Utumiki”)
8. Kodi timaonetsa motani kuti timakhulupirira zoti “tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi”? (Zef. 1:14; ‘Kuyenda mwa Chikhulupiriro Osati mwa Zooneka’)
9. (a) Kodi nkhani ya kukhumudwa n’njoopsa motani? (Marko 9:42-48) (b) Kodi tingapewe bwanji kukhumudwa? (Sal. 119:165) (c) Kodi tingapewe bwanji kukhumudwitsa ena? (1 Akor. 10:24; “Peŵani Zokhumudwitsa Zilizonse”)
10. Kodi tingatani kuti tikhale osamala pa nkhani yofuna munthu wokwatirana naye, thanzi labwino, ndi posamalira nkhani za malonda? (Sal. 26:4; Mat. 6:25; 1 Tim. 6:9; “Sungani Maganizo Anu Bwino Lomwe”)
11. (a) Kodi chochititsa chidwi n’chiyani ndi nthaŵi zimene ena anachereza Yesu? (Luka 10:42; 24:32) (b) Kodi tingachite zotani kuti tisangalale m’njira imene ingatitsitsimule, ife ndi ena? (1 Akor. 10:31-33; “Zochita Zabwino Zimene Zimatsitsimula”)
12. Mogwirizana ndi Salmo la 23, kodi ndi madalitso otani amene timalandira monga nkhosa za Yehova, ndipo kodi ifeyo udindo wathu n’ngotani? (1 Akor. 10:21; “Yehova Ndiye Mbusa Wathu”)
13. Kodi Akristu amachita chiyani pomvera langizo louziridwa lakuti afunika kuwombola nthaŵi? (Aef. 5:16; “Kuwombola Nthaŵi”)
14. (a) Kodi “nthaŵi ya chiŵeruzo” yotchulidwa pa Chivumbulutso 14:7 imaphatikizapo chiyani? (b) Kodi timapereka motani umboni wakuti tilidi osiyana ndi Babulo Wamkulu? (‘“Dikirani’ Chifukwa Nthaŵi ya Chiŵeruzo Yafika”) (c) Kodi ndi mfundo ziti zimene mwasangalala nazo m’bulosha la Dikirani!?
15. Tchulani makhalidwe atatu amene ali ofunika kuti ‘tisasiye njira yolunjika.’ (2 Pet. 2:15; “‘Musasiye Njira Yolunjika’”)
16. Kodi achinyamata angapeŵe motani ‘njira ya oipa’? (Miy. 4:14; “Achinyamata—Yendani M’njira ya Chilungamo”)
17. (a) Kodi Paulo anali chitsanzo chabwino cha kupirira m’njira zotani? (Mac. 14:19, 20; 16:25-33) (b) N’chifukwa chiyani sitiyenera kuopa otsutsa kulambira koona? (Seŵero ndi nkhani “Chitirani Umboni Mokwanira Masiku Ano Ngakhale Pali Otsutsa”)
18. Kodi amene amayenda ndi Mulungu amapeza madalitso otani? (“Kuyenda ndi Mulungu Kumadzetsa Madalitso Panopa Mpaka Muyaya”)
Tiyesetse kulabadira ‘mawu kumbuyo kwathu’ kuti tiyende ndi Atate wathu wakumwamba mpaka muyaya.—Yes. 30:21; Yoh. 3:36.