Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo—Gawo 5
Kuona Kuchuluka kwa Zimene Mungaphunzitse
1 Pamene Yesu anali kuphunzitsa ophunzira ake, anali kuwaganizira podziwa zimene angakwanitse kuzisunga mwa kulankhula nawo “monga anakhoza kumva.” (Marko 4:33; Yoh. 16:12) Mofananamo, aphunzitsi a Mawu a Mulungu masiku ano ayenera kuona kuchuluka kwa zimene angaphunzitse pa phunziro la Baibulo. Kuchuluka kwa zimene angaphunzitse kudzadalira luso ndi zochitika za pa moyo wa onse awiri, mphunzitsi ndi wophunzira.
2 Mangani Chikhulupiriro Cholimba: Ophunzira ena angafunike kuphunzira nawo maulendo awiri kapena atatu zinthu zomwe ophunzira ena akhoza kungoziphunzira ulendo umodzi wokha. Tisalepheretse wophunzirayo kumvetsetsa bwino zimene akuphunzira. Zimenezi zingachitike ngati tim’phunzitsa zinthu zambirimbiri paulendo umodzi n’cholinga choti tikamalize msanga kuphunzira naye. Wophunzira aliyense amafunika maziko olimba a chikhulupiriro chimene wangokhala nacho kumene m’Mawu a Mulungu.—Miy. 4:7; Aroma 12:2.
3 Mlungu uliwonse mukamachititsa phunziro, muzikhala ndi nthawi yokwanira yothandizira wophunzira kumvetsetsa ndi kuvomereza zimene akuphunzira m’Mawu a Mulungu. Pewani kuphunzitsa mothamanga kwambiri, zimene zikhoza kulepheretsa wophunzira kupindula ndi choonadi chimene akuphunzira. Khalani ndi nthawi yokwanira yokambirana mfundo zofunika zopezeka m’nkhaniyo ndiponso kukambirana malemba ofunika amene ndi maziko a chiphunzitsocho.—2 Tim. 3:16, 17.
4 Phunzirolo Liziyenda: Ngakhale kuti tifunika kupewa kuphunzitsa mothamanga kwambiri, tifunikanso kupewa kulowetsapo zina za pambali. Ngati wophunzira akukonda kukamba kwambiri zinthu zaumwini, tingakonze kukambirana zimenezo titamaliza phunziro.—Mlal. 3:1.
5 Komanso, chifukwa chokonda choonadi kwambiri zingativute kupewa kulankhula zambiri pa phunziro. (Sal. 145:6, 7) Nthawi zina kutchula mfundo ina ya pambali kapena zimene zinachitikapo kumathandiza kuti phunziro likhale lopindulitsa. Koma sizifunika kukhala zambirimbiri kapena zazitali zoti mpaka n’kumulepheretsa wophunzira kudziwa molondola ziphunzitso zoyambirira za Baibulo.
6 Mwa kuphunzitsa zinthu zokwanira bwino pa nthawi iliyonse ya phunziro, timathandiza ophunzira Baibulo ‘kuyenda m’kuwala kwa Yehova.’—Yes. 2:5.