Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/05 tsamba 1
  • Branch Letter

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Branch Letter
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Nkhani Yofanana
  • Branch Letter
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Kodi Kuofesi ya Mboni za Yehova Kumachitika Zotani?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
  • Branch Letter
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Umboni wa Chikondi, Chikhulupiriro, ndi Kumvera
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 9/05 tsamba 1

Branch Letter

Okondedwa Ofalitsa Ufumu Nonse:

Pamene chaka cha utumiki chatsopano chimayamba, mipingo 36 yatsopano yapangidwa m’gawo la nthambi yathu, kupangitsa chiwerengero cha mipingo yatsopano kufika pa 312 m’kati mwa zaka zisanu zapitazi. Mwa mipingo imeneyi, umodzi ndi wachitumbuka, inayi ndi yachingelezi ndipo 287 ndi yachichewa. Tsopano gawo la nthambi yathu lili ndi madera 41 ndi zigawo 4.

Ntchito yochititsa chidwi yofalitsa uthenga wabwino ikuchitika kulikonse kumene kumapezeka anthu. M’mwezi wa April, ofalitsa 64,693 anapereka malipoti a utumiki wa kumunda. Zimenezi zikutanthauza kuti ofalitsa anawonjezeka ndi 10.4 peresenti kuposa chaka chatha. Musangalala kudziwa kuti chiwerengero chatsopano cha maphunziro a Baibulo chinafika pa 65,275. Chosangalatsa kwambiri n’chakuti, ndi chiwerengero chapamwamba chimenechi, tingati wofalitsa aliyense anachititsa phunziro limodzi la Baibulo m’mwezi wa April. Bwanji ponena za ntchito yomanga Nyumba za Ufumu ndi Malo a Misonkhano? Pamene mwezi wa May umatha, Nyumba za Ufumu zokwanira 820 ndi Malo a Misonkhano okwanira 7 zinamangidwa. Tikuthokoza abale ndi alongo amene anadzipereka pogwira nawo ntchito yomanga malo olambirirawa.

Alendo akhala akubwera mwaunyinji wawo kudzaona ofesi ya nthambi ku Lilongwe. Atayendera malowa kwa nthawi yoyamba, mpainiya wina wapadera anati: “Zikomo kwambiri. Ndili wosangalala chifukwa cha kubwera kwanga kuno ndiponso chifukwa cha kucheza kolimbikitsa kwambiri. Sindidzaiwala ulendo umenewu moyo wanga wonse. Zimene ndaona ndi kuziphunzira zandilimbikitsa kuti ndikatumikire Yehova ndi moyo wanga wonse. Yehova akuthandizadi atumiki ake. Ndikuyembekezera nthawi pamene tidzatumikira Mulungu tili angwiro.” Mlongo wina wa zaka 16 atayendera malowa anati: “Sindinaonepo malo okongola chonchi! Ndachita chidwi ndi mmene amamasulira mabuku ofotokoza Baibulo. Zikusonyezadi kuti Yehova akuchirikiza anthu ake. Zimenezi zandilimbikitsa kwambiri kuti ndizichita zambiri pa ntchito yolalikira kuti ndisonyeze kuyamikira kwanga ntchito imene abale ndi alongo akuigwira yokonza mabuku ofotokoza Baibulo. Inenso, ndikufuna kutumikira Yehova mofananamo.” Mbale winanso anati: “Ndaona chilichonse chomwe ndimafuna kuona. Ndinali ndi mafunso ambiri okhudza ntchito za pa Beteli, koma lero ndapeza mayankho ake onse!” Ndifedi odala kwambiri kukhala pakati pa abale achikristu okondana chonchi!—1 Pet. 2:17.

Tikuyamikira kwambiri onse amene anagwira nawo ntchito imeneyi yopititsa patsogolo zinthu za Ufumu ndi mtima wonse. Tikukuthokozaninso kwambiri chifukwa cha kuolowa manja kwanu popereka thandizo la ndalama zochirikizira ntchitoyi. (Miy. 3:9, 10) Tikufuna kukutsimikizirani kuti timakukondani kwambiri ndipo tikuyamikira ntchito yanu yomwe mukuigwira ndi mphamvu zanu zonse. Tikupemphera kuti Yehova apitirize kudalitsa mgwirizano wathu kotero kuti “tikakhale chiyamiko cha ulemerero wake.”—Aef. 1:12, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.

Ndife abale anu,

Ofesi yaNthambi ya Malawi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena