Branch Letter
Okondedwa Ofalitsa Ufumu Nonse:
Ndife osangalala kuona mmene ntchito ya Ufumu yapitira patsogolo m’gawo la nthambi yathu, m’chaka cha utumiki cha 2007. Ntchito yomanga Nyumba za Ufumu ndiponso Malo a Msonkhano yathandiza kuti tikhale ndi malo abwino olambirira amene amatamanda dzina la Yehova. Mungasangalale kudziwa kuti pofika kumapeto a mwezi wa May 2007, Nyumba za Ufumu 900 ndiponso Malo a Msonkhano 30 anali atamangidwa.
Amalizanso kumanga nyumba za Sukulu Yophunzitsa Utumiki, zimene zili pafupi ndi ofesi ya nthambi ku Lilongwe. Zinagwiritsidwa ntchito koyamba kuchitiramo Sukulu ya Oyang’anira Oyendayenda, imene inayamba pa February 2 ndipo inatha pa March 30, 2007. Nyumbazi zigwiritsidwanso ntchito kuchitiramo makalasi awiri oyambirira a Sukulu Yophunzitsa Utumiki omwe akhale m’Chingelezi, ndipo kenako makalasi otsatira adzakhala m’Chichewa.
Dziko la Malawi linali ndi chiwerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa okwanira 68,611 m’mwezi wa April, 2007. Kameneka kanali kachiwiri m’chaka cha utumiki cha 2007 kukhala ndi chiwerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa. Lipoti la April linasonyezanso chiwerengero chapamwamba chatsopano cha maphunziro a Baibulo chokwanira pafupifupi 73,000. Chiwerengerochi chikusonyeza kuti paavereji, wofalitsa aliyense anali ndi phunziro la Baibulo loposa limodzi.
Lipoti lomwe silinathe la chaka chino la anthu opezeka pa Chikumbutso okwanira 248,500 likusonyeza kuti chiwerengerochi chawonjezereka ndi anthu 60,000 kuposa chaka chatha. Ndipo zimenezi zikusonyeza kuti padakali ntchito yaikulu yopanga ophunzira. (Mateyo 28:19, 20) Ndife osangalala kugwira nanu limodzi ntchito yofunika imeneyi, ndipo landirani moni wathu wachikondi chachikhristu.
Ndife abale anu,
Ofesi ya Nthambi ya Malawi