Kodi Tingathandize Motani?
1 Mboni za Yehova zikamva za tsoka limene lachitika mbali ina ya dziko zimafunsa funso lakuti, “Kodi tingathandize motani?” Monga mmene lemba la Machitidwe 11:27-30 limasonyezera, Akristu oyambirira anapereka thandizo kwa abale omwe amakhala m’Yudeya chifukwa kunagwa njala.
2 Masiku ano, malamulo athu amalola kugwiritsa ntchito ndalama monga chithandizo kwa anthu omwe akuvutika ndi masoka achilengedwe kapenanso masoka ochititsidwa ndi anthu, ngakhalenso kugwiritsa ntchito ndalama pa nthawi imene pangafunike thandizo lina lililonse.
3 Mwachitsanzo, chaka chathachi abale ambiri anapereka thandizo la ndalama lothandiza anthu amene anakhudzidwa ndi tsoka la tsunami, lomwe linachitika kum’mwera kwa Asia. Zopereka zimenezi zochokera pansi pa mtima, zomwe zinaperekedwa ku thumba limene gulu linakhazikitsa la ndalama za chithandizo zinayamikiridwa kwambiri. Komabe, ngati zopereka zikonzedwa mwapadera kuti zithandize pa tsoka lakutilakuti, m’mayiko ena malamulo amafuna kuti ndalamazo zigwire ntchito imene munthu waziperekera basi ndiponso panyengo ndi nthawi yakutiyakuti, kaya abale athu ovutikawo asamalidwa kapena ayi.
4 Chifukwa cha zimenezi, ndi bwino kuti zopereka za chithandizo zimenezi ziziperekedwa ku ntchito ya padziko lonse. Ndalama za thumba limeneli zimagwiritsidwa ntchito kuthandiza anthu osowa komanso kuthandiza pa zosowa zauzimu za abale achikristu. Ngati, pazifukwa zina wina akufuna kupereka thandizo la ndalama mosiyanitsa ndi zopereka za ntchito ya padziko lonse, zidzalandiridwabe ndipo zidzagwiritsidwa ntchito kulikonse komwe kungafunike thandizo. Komabe, zingakhale bwino kwambiri ngati zoperekazo zingaperekedwe popanda kutchula kumene ndalamazo zikagwiritsidwe ntchito ndi mmene zikagwirire ntchito.
5 Ngati zopereka zathu tiziika ku ntchito ya padziko lonse, zimathandiza kuti pakhale ndalama zokwanira zofunika pa ntchito zonse za Ufumu, kusiyana ndi kungozisungira chithandizo cha m’tsogolo cha anthu osowa thandizo. Zimenezi zikugwirizana ndi mfundo yopezeka pa Aefeso 4:16, yakuti tizigwira ntchito limodzi kupereka zofunika kuti ‘thupi likule, kufikira chimango chake mwa chikondi.’