Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/06 tsamba 1
  • Utumiki Wathu Ndi Ntchito Imene Imasonyeza Chifundo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Utumiki Wathu Ndi Ntchito Imene Imasonyeza Chifundo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Nkhani Yofanana
  • “Chifundo Chachikulu cha Mulungu Wathu”
    Yandikirani Yehova
  • Tizitsanzira Yehova pa Nkhani ya Chifundo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • “Anagwidwa ndi Chifundo”
    ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
  • Yehova Amalamulira Mwachifundo
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 6/06 tsamba 1

Utumiki Wathu Ndi Ntchito Imene Imasonyeza Chifundo

1 Yesu anazindikira kuti ambiri mwa anthu amene ankamvetsera uthenga wake anali “okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.” (Mat. 9:36) Mokoma mtima ndi mwachikondi, anawaphunzitsa miyezo ya Yehova, anawakhazika mitima pansi, ndipo mwachifundo anasamalira zosowa zawo zauzimu. Tikamasinkhasinkha za mmene Yesu ankachitira zinthu, timaphunzira kuganiza ndiponso kumva ngati mmene iye ankachitira. Ndipo khalidwe la chifundo limeneli limaonekera bwino mu utumiki wathu.

2 Tangoganizirani mmene Yesu anachitira, anthu osowa thandizo atam’peza. (Luka 5:12, 13; 8:43-48) Iye anachitira chifundo anthu amene anali ndi zosowa zapadera. (Marko 7:31-35) Ankadziwa mmene anthu amamvera mumtima mwawo ndipo anali kuwadera nkhawa kwambiri. Sikuti ankangoona maonekedwe awo okha ayi. (Luka 7:36-40) N’zoona kuti Yesu anatsanzira ndendende chifundo cha Mulungu wathu!

3 ‘Anagwidwa Chifundo’: Yesu sankaona utumiki wake monga ntchito yoti n’kungoichita mwamwambo. Iye ‘anagwidwa chifundo’ ndi anthu. (Marko 6:34) N’chimodzimodzinso masiku ano, sikuti ntchito yathu ndi kungolengeza uthenga basi, koma tikuyesetsanso kupulumutsa miyoyo ya anthu. Yesetsani kuzindikira chifukwa chimene anthu amalabadirira kapena kusalabadira uthenga wathu. N’chifukwa chiyani akuoneka ankhawa ndi osakhazikika maganizo? Kapena kodi abusa a chipembedzo chonyenga awataya ndi kuwaphimba m’maso? Chidwi chenicheni chimene tingakhale nacho pa anthu, n’chimene chingawachititse kuti amvetsere uthenga wabwino.—2 Akor. 6:4, 6.

4 Anthu amakhudzidwa mtima akasonyezedwa chifundo. Mwachitsanzo: Mwana wa miyezi itatu wa mayi wina atamwalira, mayi wakeyo anathedwa nzeru kwambiri. Alongo awiri anafika pakhomo pa mayiyo, ndipo iye anawalowetsa m’nyumba n’cholinga choti atsutsane nawo za chifukwa chimene Mulungu akulolera anthu kuvutika. Komano pambuyo pokambirana ndi alongowo, mayiyo ananena kuti: “Mmene ndinkawafotokozera za nkhani yanga iwo anachita nane chifundo kwambiri, ndipo pamene amachoka n’kuti ndikumvako bwino ndipo ndinawalola kuti adzabwerenso.” Kodi nanunso mumayesetsa kusonyeza chifundo munthu wina aliyense amene mwakumana naye mu utumiki?

5 Kukhala achifundo n’kothandiza kuti uthenga wathu ukhale wotonthoza kwa anthu. Kuchita zimenezi n’kofunika kuti tilemekeze “Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse,” Yehova.—2 Akor. 1:3.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena