Sonyezani Ena Chidwi mwa Kuwayamikira
1 Kuyamikira ena moona mtima kumalimbikitsa, kumachititsa munthu kuchita zinthu mofunitsitsa, ndipo kumapatsa chimwemwe. Ofalitsa ambiri aona kuti pamene ali mu utumiki, kuuza ena mawu ochepa chabe owayamikira, nthawi zambiri kumachititsa kuti anthuwo aziwamvetsera. Kodi tingawayamikire bwanji anthu pamene tikufuna kuwauza uthenga wabwino?
2 Khalani Maso: Yesu Kristu atabwerera kumwamba anayamikira ntchito yabwino imene mipingo isanu ndi iwiri ya ku Asia Minor inachita. (Chiv. 2:2, 3, 13, 19; 3:8) Nafenso ngati tili ndi chidwi chenicheni ndi anthu amene timakumana nawo mu utumiki wathu, tidzafufuza mipata yoti tiwayamikire. Mwachitsanzo, tingayamikire anthu chifukwa chosamalira bwino panyumba pawo, kholo limene likusonyeza kuti limasamalira bwino mwana wake, kapena chifukwa cha kumwetulira ndiponso moni wawo wansangala. Kodi mumakhala maso n’kugwiritsa ntchito mipata imeneyi?
3 Amvetsereni: Pamene mukulalikira ena, afunseni mafunso oyenerera kuti akuuzeni zambiri zokhudza moyo wawo. Alemekezeni mwa kumvetsera mwachidwi zimene akunena. (Aroma 12:10) Sitikukayikira kuti pa zinthu zimene angalankhule, mungapezepo chinachake chimene mungafune kuwayamikira nacho, ndiyeno yambani kukambirana nawo kuchokera pa zimene mwawayamikira nazozo.
4 Chitani Zinthu Mwanzeru: Kodi tingachite chiyani ngati mwininyumba walankhula chinachake chosagwirizana ndi choonadi cha m’Baibulo? M’malo motsutsana naye pa mawu ake olakwikawo, ingoyamikirani zimene wanena ndi kupitiriza ndi mawu onga akuti: “Ndikuona kuti muli ndi chidwi kwambiri ndi nkhani imeneyi.” (Akol. 4:6) Ngakhale ngati munthu akungofuna kukangana nafe, tingathebe kumuyamikira pa chifukwa chakuti ali nayo chidwi nkhaniyo. Kuchita zinthu mwa njira imeneyi kungachititse kuti anthu amene amatsutsa kwambiri asinthe mitima n’kumvetsera uthenga wabwino.—Miy. 25:15.
5 Kuti kuyamikira kwathu kukhale kwaphindu, tiyenera kunena zinthu zoona zokhazokha. Mawu oyamikira otere, amalemekeza Yehova ndipo amatha kuchititsa anthu kulabadira uthenga wa Ufumu.