Ndife Osangalala Kutumikira Yehova Modzipereka
1 Mtumwi Paulo anasangalala ‘kudzipereka kotheratu’ kuti akwaniritse utumiki wake wachikhristu. (2 Akor. 12:15) N’chimodzimodzi masiku ano, Akhristu ambiri amene ndi apainiya amagwira ntchito mwakhama. Akhristu ena omwe ali ndi udindo waukulu m’banja ndiponso ndi otanganidwa amapatula nthawi kuti azilalikira nawo mlungu uliwonse. Ena amene amadwaladwala amagwiritsa ntchito nyonga zawo zochepa m’ntchito ya Ufumu. N’zolimbikitsa kwambiri kuona anthu a Yehova, kaya ndi okalamba kapena ayi ndiponso kaya moyo wawo ndi wotani, akutumikira Yehova modzipereka.
2 Kukonda Mnansi: Tikamachita zonse zimene tingathe kutumikira Yehova ndi kukonda Mulungu ndi mnansi wathu, timakhala ndi chikumbumtima chabwino. Popeza kuti Paulo anadzipereka kwambiri polalikira uthenga wabwino, iye anatha kunena mosangalala kuti: “Mukhale mboni leroli, kuti ine ndili woyera pa mlandu wa magazi a anthu onse.” (Mac. 20:24, 26; 1 Ates. 2:8) Kulalikira nawo mmene tingathere mogwirizana ndi mmene moyo wathu ulili, kungatithandize kupewa mlandu wa magazi.—Ezek. 3:18-21.
3 Kugwira ntchito modzipereka kuti tithandize ena kumabweretsa chisangalalo. (Mac. 20:35) Mbale wina anati: “Kunena zoona, ndikabwerera ku nyumba madzulo pambuyo pokhala tsiku lonse muutumiki wa Yehova, ndimakhala wotopa. Komabe, ndimasangalala ndipo ndimathokoza Yehova chifukwa chondipatsa chimwemwe chimene palibe munthu amene angandilande.”
4 Kukonda Mulungu: Chifukwa chachikulu chotumikira Yehova modzipereka n’choti Atate wathu wa kumwamba amasangalala tikamatero. Tikamakonda Mulungu, timamvera malamulo ake, amene amaphatikizapo kulalikira ndi kupanga ophunzira. (1 Yoh. 5:3) Ngakhale pamene anthu sakufuna kumvetsera kapena akutitsutsa, timapitirizabe mosangalala kugwira ntchito ya Yehova mwakhama.
5 Ino si nthawi yochepetsa zimene timachita mu utumiki wa Yehova chifukwa choti tikukhala m’nthawi yokolola. (Mat. 9:37) Mlimi amagwira ntchito maola ambiri panthawi yokolola chifukwa chakuti amakhala ndi nthawi yochepa yoti akolole dzinthu zake zisanawonongeke. Nthawinso yoti tichite ntchito yokolola mwauzimu ndi yochepa. Motero, tiyeni tizikumbukira nthawi imene tikukhalamo ndipo tipitirize kuyesetsa mwamphamvu kuchita utumiki wa Mulungu.—Luka 13:24; 1 Akor. 7:29-31.